Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

108 Mau a Mulungu Okondwera ndi Yehova

M’salmo 37:4 Davide anati, “Sangalala mwa Yehova, ndipo adzakupatsa zokhumba za mtima wako.” Kusangalala kumeneku, ndiko kukhala wachimwemwe chenicheni, wokhutira ndi chinthu chomwe chimatipatsa chimwemwe choona. Baibulo limatiphunzitsa kuti chimwemwe choonachi chimapezeka mwa Mulungu yekha. Tikamasangalala mwa Iye, mavuto athu ndi zovuta zathu zimachepa, podziwa kuti Iye ndiye wolamulira wa miyoyo yathu.

Tikamasangalala mwa Mulungu, ubwenzi wathu ndi Iye umalimba, timamuyandikira kwambiri, ndipo timaphunzira kudalira malonjezo ake. Kusangalala mwa Iye kumatithandizanso kukhala oyamikira, podziwa kuti madalitso athu onse amachokera ku chikondi chake ndi chisamaliro chake pa ife.

Koma kusangalala mwa Mulungu sikutanthauza kunyalanyaza maudindo athu a tsiku ndi tsiku kapena kuthawa mavuto. M’malomwake, kumatanthauza kupeza mphamvu ndi nzeru mwa Iye kuti tithe kuthana ndi mavutowo molimba mtima komanso modalira.

Kumbukira kuti kusangalala mwa Mulungu kumatipatsa moyo wabwino komanso watanthauzo. Kumatithandiza kupeza chikhutiro choona ndi kudziwa cholinga chimene Iye ali nacho pa moyo wathu.

Pakati pa zovuta ndi zosokoneza za dziko lino, tikumbukire kuti mwa Mulungu yekha ndi komwe tingapeze chimwemwe chimene mitima yathu imakhumba.


Masalimo 119:16

Ndidzadzikondweretsa nao malemba anu; sindidzaiwala mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 15:16

Mau anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mau anu anakhala kwa ine chikondwero ndi chisangalalo cha mtima wanga; pakuti ndatchedwa dzina lanu, Yehova Mulungu wa makamu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 22:8

Adadzitengera kwa Yehova; kuti adzampulumutsa, amlanditse tsopano popeza akondwera naye.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:4

Kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 16:11

Mudzandidziwitsa njira ya moyo, pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 61:10

Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:4

Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 40:8

kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga; ndipo malamulo anu ali m'kati mwamtima mwanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 1:2

Komatu m'chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m'chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 112:1

Aleluya. Wodala munthu wakuopa Yehova, wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 2:1

Ndipo Hana anapemphera, nati, Mtima wanga umyuka mokondwera kwa Yehova, nyanga yanga yakwezeka mwa Yehova; pakamwa panga pakula kwa adani anga; popeza ndikondwera m'chipulumutso chanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Nehemiya 8:10

Nanena naonso, Mukani, mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lake iye amene sanamkonzeretu kanthu; chifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamachita chisoni; pakuti chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu yanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 27:4

Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa mu Kachisi wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Nehemiya 9:25

Ndipo analanda mizinda yamalinga, ndi dziko la zonona, nalandira zikhale zaozao nyumba zodzala ndi zokoma zilizonse, zitsime zokumbidwa, minda yampesa, ndi minda ya azitona, ndi mitengo yambiri yazipatso; nadya iwo, nakhuta, nanenepa, nakondwera nako kukoma kwanu kwakukulu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 34:8

Talawani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino; wodala munthuyo wakukhulupirira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 58:14

pomwepo udzakondwa mwa Yehova; ndipo Ine ndidzakuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi; ndipo ndidzakudyetsa cholowa cha kholo lako Yakobo; pakuti pakamwa pa Yehova pananenapo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:35

Mundiyendetse mopita malamulo anu; pakuti ndikondwera m'menemo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 9:2

Ndidzakondwerera ndi kusekera mwa Inu; ndidzaimbira dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yobu 22:26

Pakuti pamenepo udzakondwera naye Wamphamvuyonse, ndi kuweramutsa nkhope yako kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:92

Chilamulo chanu chikadapanda kukhala chikondweretso changa, ndikadatayika m'kuzunzika kwanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 94:19

Pondichulukira zolingalira zanga m'kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 147:10

Mphamvu ya kavalo siimkonda: Sakondwera nayo miyendo ya munthu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 55:2

Bwanji inu mulikutayira ndalama chinthu chosadya, ndi kutayira malipiro anu zosakhutitsa? Mverani Ine mosamalitsa, nimudye chimene chili chabwino, moyo wanu nukondwere ndi zonona.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 14:10

Atero Yehova kwa anthu awa, Chomwecho akonda kusocherera; sanakanize mapazi ao; chifukwa chake Yehova sawalandira; tsopano adzakumbukira choipa chao, nadzalanga zochimwa zao.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 8:30-31

Ndinali pa mbali pake ngati mmisiri; ndinamsekeretsa tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera pamaso pake nthawi zonse;

ndi kukondwera ndi dziko lake lokhalamo anthu, ndi kusekerera ndi ana a anthu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mika 7:18

Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:47

Ndipo ndidzadzikondweretsa nao malamulo anu, amene ndiwakonda.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:111

Ndinalandira mboni zanu zikhale cholandira chosatha; pakuti ndizo zokondweretsa mtima wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 15:13

Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 19:8

Malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima; malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:23

Yehova akhazikitsa mayendedwe a munthu; ndipo akondwera nayo njira yake.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 1:8

amene mungakhale simunamuone mumkonda; amene mungakhale simumpenya tsopano, pokhulupirira, mukondwera naye ndi chimwemwe chosaneneka, ndi cha ulemerero:

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 15:11

Izi ndalankhula ndi inu, kuti chimwemwe changa chikhale mwa inu, ndi kuti chimwemwe chanu chidzale.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:114

Inu ndinu pobisalapo panga, ndi chikopa changa; ndiyembekezera mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 92:4

Popeza Inu, Yehova, munandikondweretsa ndi kuchita kwanu, ndidzafuula mokondwera pa ntchito ya manja anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 100:2

Tumikirani Yehova ndi chikondwerero: Idzani pamaso pake ndi kumuimbira mokondwera.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 149:4

Popeza Yehova akondwera nao anthu ake; adzakometsa ofatsa ndi chipulumutso.

Mutu    |  Mabaibulo
Zefaniya 3:17

Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi chimwemwe, adzakhala wopanda thamo m'chikondi chake; adzasekerera nawe ndi kuimbirapo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:14

Ndinakondwera m'njira ya mboni zanu, koposa ndi chuma chonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 32:11

Sekerani mwa Yehova, ndimo kondwerani inu olungama mtima; ndipo fuulani mokondwera nonsenu oongoka mtima.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 118:24

Tsiku ili ndilo adaliika Yehova; tidzasekera ndi kukondwera m'mwemo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 63:5-6

Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi zonona; ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani ndi milomo yakufuula mokondwera.

Pokumbukira Inu pa kama wanga, ndi kulingalira za Inu maulonda a usiku.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 12:2-3

Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.

Chifukwa chake mudzakondwera pakutunga madzi m'zitsime za chipulumutso.

Mutu    |  Mabaibulo
Habakuku 3:18

koma ndidzakondwera mwa Yehova, ndidzasekerera mwa Mulungu wa chipulumutso changa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 33:21

Pakuti mtima wathu udzakondwera mwa Iye, chifukwa takhulupirira dzina lake loyera.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:162

Ndikondwera nao mau anu, ngati munthu wakupeza zofunkha zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 5:11

Ndipo si chotero chokha, koma ife tikondwera ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene talandira naye tsopano chiyanjanitso.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 3:1

Chotsalira, abale anga, kondwerani mwa Ambuye. Kulembera zomwezo kwa inu, sikundivuta ine, koma kwa inu kuli kukhazikitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 31:7

Ndidzakondwera ndi kusangalala m'chifundo chanu, pakuti mudapenya zunzo langa; ndipo mudadziwa mzimu wanga mu nsautso yanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 97:12

Kondwerani mwa Yehova, olungama inu; ndipo yamikani pokumbukira chiyero chake.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mbiri 16:27

Pamaso pake pali ulemu ndi ukulu, m'malo mwake muli mphamvu ndi chimwemwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 21:6

Pakuti mumuikira madalitso kunthawi zonse; mumkondweretsa ndi chimwemwe pankhope panu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 26:8

Inde m'njira ya maweruziro anu, Yehova, ife talindira Inu; moyo wathu ukhumba dzina lanu, ndi chikumbukiro chanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 42:1

Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje; motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 5:16-18

Kondwerani nthawi zonse;

Pempherani kosaleka;

M'zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 35:9

Ndipo moyo wanga udzakondwera mwa Yehova; udzasekera mwa chipulumutso chake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 84:10

Pakuti tsiku limodzi m'mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena. Kukhala ine wapakhomo m'nyumba ya Mulungu wanga, kundikonda ine koposa kugonera m'mahema a choipa.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 10:20

Koma musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti maina anu alembedwa mu Mwamba.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 89:15-16

Odala anthu odziwa liu la lipenga; ayenda m'kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.

Akondwera m'dzina lanu tsiku lonse; ndipo akwezeka m'chilungamo chanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:7

Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:24

Mboni zanu zomwe ndizo zondikondweretsa, ndizo zondipangira nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 104:34

Pomlingirira Iye pandikonde; ndidzakondwera mwa Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:103

Mau anu azunadi powalawa ine! Koposa uchi m'kamwa mwanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:167

Moyo wanga unasamalira mboni zanu; ndipo ndizikonda kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 106:5

Kuti ndione chokomacho cha osankhika anu, kuti ndikondwere nacho chikondwerero cha anthu anu, kuti ndidzitamandire pamodzi ndi cholowa chanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:12

kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:22

Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 28:7

Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza, chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu; ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 16:24

Kufikira tsopano simunapemphe kanthu m'dzina langa; pemphani, ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikwaniridwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 107:9

Pakuti akhutitsa mtima wolakalaka, nadzaza mtima wanjala ndi zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 71:23

Milomo yanga idzafuula mokondwera poimbira Inu nyimbo; inde, moyo wanga umene munaombola.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 1:4

ndipo izi tilemba ife, kuti chimwemwe chathu chikwaniridwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:143

Kusautsika ndi kupsinjika kwandigwera; koma malamulo anu ndiwo ondikondweretsa ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 146:5

Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 144:15

Odala anthu akuona zotere; odala anthu amene Mulungu wao ndi Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 97:1

Yehova achita ufumu; dziko lapansi likondwere; zisumbu zambiri zikondwerere.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 35:10

ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni alikuimba; kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; iwo adzakhala ndi kusekerera ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:70

Mtima wao unona ngati mafuta; koma ine ndikondwera nacho chilamulo chanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 15:13

Mtima wokondwa usekeretsa nkhope; koma moyo umasweka ndi zowawa za m'mtima.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 65:18-19

Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala kunthawi zonse ndi ichi ndichilenga; pakuti taonani, ndilenga Yerusalemu wosangalala, ndi anthu ake okondwa.

Ndipo ndidzasangalala mu Yerusalemu, ndi kukondwera mwa anthu anga; ndipo mau akulira sadzamvekanso mwa iye, pena mau akufuula.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 30:11

Munasanduliza kulira kwanga kukhale kusekera; munandivula chiguduli changa, ndipo munandiveka chikondwero,

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 10:10

Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga. Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 2:28

munandidziwitsa ine njira za moyo; mudzandidzaza ndi kukondwera pamaso panu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 51:3

Pakuti Yehova watonthoza mtima wa Ziyoni, watonthoza mtima wa malo ake onse abwinja; ndipo wasandutsa chipululu chake ngati Edeni, ndi malo ake ouma ngati munda wa Yehova; kukondwa ndi kusangalala kudzapezedwa m'menemo, mayamikiro, ndi mau a nyimbo yokoma.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 36:8

Adzakhuta kwambiri ndi zonona za m'nyumba mwanu, ndipo mudzawamwetsa mu mtsinje wa zokondweretsa zanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 1:25

Ndipo pokhulupirira pamenepo ndidziwa kuti ndidzakhala, ndi kukhalitsa ndi inu nonse, kuonjezera chimwemwe cha chikhulupiriro chanu;

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 16:20

Wolabadira mau adzapeza bwino; ndipo wokhulupirira Yehova adala.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 126:3

Yehova anatichitira ife zazikulu; potero tikhala okondwera.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 43:4

Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu, kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni, ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:77

Nsoni zokoma zanu zindidzere, kuti ndikhale ndi moyo; popeza chilamulo chanu chindikondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:174

Ndinakhumba chipulumutso chanu, Yehova; ndipo chilamulo chanu ndicho chondikondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:11

Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nao mtendere wochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 1:47

ndipo mzimu wanga wakondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 63:3

Pakuti chifundo chanu chiposa moyo makomedwe ake; milomo yanga idzakulemekezani.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 9:3

Inu mwachulukitsa mtundu, inu mwaenjezera kukondwa kwao; iwo akondwa pamaso panu monga akondwera m'masika, monga anthu akondwa pogawana zofunkha.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:13

Wodala ndi wopeza nzeru, ndi woona luntha;

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 90:14

Mutikhutitse nacho chifundo chanu m'mawa; ndipo tidzafuula mokondwera ndi kukondwera masiku athu onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 63:7

Pakuti munakhala mthandizi wanga; ndipo ndidzafuula mokondwera mu mthunzi wa mapiko anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 14:17

Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 138:5

Ndipo adzaimbira njira za Yehova; pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:72

Chilamulo cha pakamwa panu chindikomera koposa golide ndi siliva zikwizikwi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 65:4

Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa, akhale m'mabwalo anu. Tidzakhuta nazo zokoma za m'nyumba yanu, za m'malo oyera a Kachisi wanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 95:1-2

Tiyeni tiimbire Yehova mokondwera; tifuule kwa thanthwe la chipulumutso chathu.

Zaka makumi anai mbadwo uwu unandimvetsa chisoni, ndipo ndinati, Iwo ndiwo anthu osokerera mtima, ndipo sadziwa njira zanga.

Chifukwa chake ndinalumbira mu mkwiyo wanga, ngati adzalowa mpumulo wanga.

Tidze nacho chiyamiko pamaso pake, timfuulire Iye mokondwera ndi nyimbo.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 2:17-18

Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse;

momwemonso kondwerani inu, nimukondwere pamodzi ndi ine.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mbiri 16:10

Mudzitamandire ndi dzina lake lopatulika; mitima yao ya iwo ofuna Yehova ikondwere.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 84:2

Moyo wanga ulakalaka, inde ukomokanso ndi kufuna mabwalo a Yehova; mtima wanga ndi thupi langa zifuulira kwa Mulungu wamoyo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:165

Akukonda chilamulo chanu ali nao mtendere wambiri; ndipo alibe chokhumudwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 43:5

Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamyamikanso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga, ndi Mulungu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Mulungu wanga, kukhalapo kwanu n'kodabwitsa kwa ine. Mwa inu ndimapeza mtendere, chimwemwe, bata, ndi chikondi chanu chosatha. Muli nazo zonse zomwe ndikusowa; ndinu mphamvu yanga, mlengi wanga. Palibe tsiku limodzi lomwe sindiona chifundo chanu chachikulu pa moyo wanga. Munthirira ine ndi chisomo ndi ubwino wanu, mundidzaza ndi madalitso ochuluka omwe amandipangitsa kusangalala. Sindingathe kukhala wopanda chimwemwe pamaso panu. Ndikulakalaka kukhala nanu nthawi zonse, cholinga changa ndi kusangalala tsiku lililonse ndi chikondi chanu ndi mawu anu, ndi kukhala wofukiza wabwino pamaso panu. Ndikupemphani, musalole chilichonse kundilekanitsa ndi chiyero chanu. Mundibatize ndi chikondi chanu, mundigwire mwamphamvu kufikira nditakhala mmodzi ndi inu. Ndinu chikondi changa, chilungamo changa, ndi chitetezo changa. Ndikukuthokozani chifukwa cha zonse; malingaliro anu ndi abwino kwa ine, ndipo ndikudziwa kuti zonse zimandigwirira ntchito yabwino. Ndimakulambirani ndi kukukwezani, m'dzina la Yesu, Ameni.