Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


MAVESI OLALIKIRA

MAVESI OLALIKIRA

Ndili ndi uthenga wabwino kwambiri woti ndikugawireni lero. Mulungu watipatsa ntchito yofunika kwambiri, yolalikira uthenga wabwino kwa aliyense. Baibulo limati, “Ndipo anawauza iwo, Mukaonke padziko lonse lapansi, mulalikire Uthenga Wabwino ku cholengedwa chonse.” (Marko 16:15).

Konzekerani kugwira ntchito yokongola iyi imene Mulungu watipatsa. Muuzeni aliyense amene sadziwa Mulungu za chikondi chake. Werengani Mawu a Mulungu mwachidwi, ndipo mudzadziwa mmene mungayankhulire ndi anthu amene Mulungu akuika pa moyo wanu. Limbikani mtima, musachite mantha kuuza anthu uthenga wabwino wa chipulumutso ndi moyo wosatha umene Mulungu wakupatsani kale.

Mulungu adzakupatsani mphamvu ndi kukulimbikitsani tsiku lililonse kudzera m’Mawu ake. Baibulo limati, “Koma Mulungu atsimikiza chikondi chake kwa ife, mwa kuti pokhala ife ochimwa, Khristu adatifera ife.” (Aroma 5:8).




Yeremiya 17:7-8

Wodala munthu amene akhulupirira Yehova, amene chikhulupiriro chake ndi Yehova. Ndipo adzakhala ngati mtengo wooka kuli madzi, wotambalitsa mizu yake pamtsinje, wosaopa pofika nyengo yadzuwa, koma tsamba lake likhala laliwisi; ndipo suvutika chaka cha chilala, suleka kubala zipatso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:1-2

Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye wam'munda. Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'chikondi changa; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'chikondi chake. Izi ndalankhula ndi inu, kuti chimwemwe changa chikhale mwa inu, ndi kuti chimwemwe chanu chidzale. Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mnzake, monga ndakonda inu. Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulani inu. Sinditchanso inu akapolo; chifukwa kapolo sadziwa chimene mbuye wake achita; koma ndatcha inu abwenzi; chifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziwitsani. Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala chipatso, ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chilichonse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu. Zinthu izi ndilamula inu, kuti mukondane wina ndi mnzake. Ngati dziko lapansi lida inu, mudziwa kuti lidada Ine lisanayambe kuda inu. Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zake za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma Ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu. Nthambi iliyonse ya mwa Ine yosabala chipatso, aichotsa; ndi iliyonse yakubala chipatso, aisadza, kuti ikabale chipatso chochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:16

Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala chipatso, ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chilichonse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22-23

Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 3:8

Onetsani inu zipatso zakuyenera kutembenuka mtima:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:17-20

Chomwecho mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa. Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuchi kupatsa zipatso zokoma. Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto. Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso. Inde chomwecho pa zipatso zao mudzawazindikira iwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:5

Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zake: wakukhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye, ameneyo abala chipatso chambiri; pakuti kopanda Ine simungathe kuchita kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:8

Mwa ichi alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale chipatso chambiri; ndipo mudzakhala ophunzira anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:22

Ndipo iye amene afesedwa kuminga, uyu ndiye wakumva mau; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma chitsamwitsa mau, ndipo akhala wopanda chipatso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 7:4

Chotero, abale anga, inunso munayesedwa akufa ku chilamulo ndi thupi la Khristu; kuti mukakhale ake a wina, ndiye amene anaukitsidwa kwa akufa, kuti ife timbalire Mulungu zipatso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 26:3-4

Mukamayenda m'malemba anga, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwachita; Ndipo ndidzaononga malo amsanje anu, ndi kulikha zoimiritsa zanu za dzuwa, ndi kuponya mitembo yanu pa mitembo ya mafano anu; ndi moyo wanga udzanyansidwa nanu. Ndipo ndidzasandutsa mizinda yanu bwinja, ndi kupasula malo anu opatulika, wosanunkhiza Ine za fungo lanu lokoma. Inde, ndidzapasula dzikoli, ndipo adani anu akukhala m'mwemo adzadabwa nako. Ndipo ndidzabalalitsa inu mwa amitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi mizinda yanu idzakhala bwinja. Pamenepo dzikoli lidzakondwera nao masabata ake, masiku onse a kupasuka kwake, pokhala inu m'dziko la adani anu; pamenepo dziko lidzapumula, ndi kukondwera nao masabata ake. Masiku onse a kupasuka kwake lipumula; ndiko mpumulo udalisowa m'masabata anu, pokhala inu pamenepo. Kunena za iwo akutsalira, ndidzalonga kukomoka kumtima kwao m'maiko a adani ao; ndi liu la tsamba lotengeka ndi mphepo lidzawapirikitsa; ndipo adzathawa monga amathawa lupanga; ndipo adzagwa wopanda wakuwalondola. Ndipo adzakhumudwitsana monga pothawa lupanga, wopanda wakuwalondola; ndipo mudzakhala opanda mphamvu yakuima pamaso pa adani anu. Ndipo mudzatayika mwa amitundu, ndi dziko la adani anu lidzakudyani. Ndipo otsala mwa inu adzazunzika m'moyo ndi mphulupulu zao m'maiko a adani anu; ndiponso ndi mphulupulu za makolo ao adzazunzika m'moyo. ndidzakupatsani mvula m'nyengo zake, ndi dziko lidzapereka zipatso zake, ndi mitengo ya m'minda idzabala zipatso zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:18

Ndipo chipatso cha chilungamo chifesedwa mumtendere kwa iwo akuchita mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 1:3

Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:11

Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 1:28

Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:43-45

Pakuti palibe mtengo wabwino wakupatsa zipatso zovunda; kapenanso mtengo woipa wakupatsa zipatso zabwino. Pakuti mtengo uliwonse uzindikirika ndi chipatso chake. Pakuti anthu samatchera nkhuyu paminga, kapena pamtungwi samatchera mphesa. Munthu wabwino atulutsa zabwino m'chuma chokoma cha mtima wake; ndi munthu woipa atulutsa zoipa m'choipa chake: pakuti m'kamwa mwake mungolankhula mwa kuchuluka kwa mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:16-18

Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse chilakolako cha thupi. Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazichite. Ngati Mzimu akutsogolerani, simuli omvera lamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 1:29

Ndipo anati Mulungu, Taonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbeu lili padziko lapansi, ndi mitengo yonse m'mene muli chipatso cha mtengo wakubala mbeu; chidzakhala chakudya cha inu:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:15

Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:13

Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Aonetsere ndi mayendedwe ake abwino ntchito zake mu nzeru yofatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 3:8-9

Chifukwa chake balani zipatso zakuyenera kulapa mtima, ndipo musayambe kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye ndiye Abrahamu: pakuti ndinena kwa inu, kuti ali ndi mphamvu Mulungu, mwa miyala iyi, kuukitsira Abrahamu ana. Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo; chotero mtengo uliwonse wosabala chipatso chabwino udulidwa, nuponyedwa pamoto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:33

Ukakoma mtengo, chipatso chake chomwe chikoma; ukaipa mtengo, chipatso chake chomwe chiipa; pakuti ndi chipatso chake mtengo udziwika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:2

Nthambi iliyonse ya mwa Ine yosabala chipatso, aichotsa; ndi iliyonse yakubala chipatso, aisadza, kuti ikabale chipatso chochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:14

Ndipo anthu athu aphunzirenso asunge ntchito zabwino zofunika, kuti asakhale osabala zipatso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 92:12-14

Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa; adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni. Iwo ookedwa m'nyumba ya Yehova, adzaphuka m'mabwalo a Mulungu wathu. Atakalamba adzapatsanso zipatso; adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriwiri,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:30

Chipatso cha wolungama ndi mtengo wa moyo; ndipo wokola mtima ali wanzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:17

Koma nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yosadzikometsera pamaso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 1:5-8

Ndipo mwa ichi chomwe, pakutengeraponso changu chonse, muonjezerapo ukoma pa chikhulupiriro chanu, ndi paukoma chizindikiritso; ndi pachizindikiritso chodziletsa; ndi pachodziletsa chipiriro; ndi pachipiriro chipembedzo; ndi pachipembedzo chikondi cha pa abale; ndi pachikondi cha pa abale chikondi. Pakuti izi zikakhala ndi inu, ndipo zikachuluka, zidzachita kuti musakhale aulesi kapena opanda zipatso pa chizindikiritso cha Ambuye Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 4:20

Ndipo iwo ofesedwa pa nthaka yabwino ndiwo oterewa akumva mau, nawalandira, nabala zipatso zakupindula makumi atatu, ndi makumi asanu ndi limodzi, ndi makumi khumi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 126:5-6

Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera. Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbeu yakufesa; adzabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera, alikunyamula mitolo yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 12:24

Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati mbeu ya tirigu siigwa m'nthaka, nifa, ikhala pa yokha iyo; koma ngati ifa, ibala chipatso chambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:8-9

pakuti kale munali mdima, koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuunika, pakuti chipatso cha kuunika tichipeza mu ubwino wonse, ndi chilungamo, ndi choonadi,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:13

Ndipo sindifuna kuti inu, abale, mudzakhala osadziwa, kuti kawirikawiri ndikanena mumtima kuti ndikafike kwa inu, koma ndaletsedwa kufikira lero, kuti ndikaone zobala zina mwa inunso, monga mwa anthu amitundu ena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:10

kuti mukayenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m'chizindikiritso cha Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 8:15

Ndipo zija za m'nthaka yokoma, ndiwo amene anamva mau nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:11

odzala nacho chipatso cha chilungamo, chimene chili mwa Yesu Khristu, kuchitira Mulungu ulemerero ndi chiyamiko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:9

pakuti chipatso cha kuunika tichipeza mu ubwino wonse, ndi chilungamo, ndi choonadi,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:29

Ngati mudziwa kuti ali wolungama, muzindikira kuti aliyensenso wakuchita chilungamo abadwa kuchokera mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 107:37

nafese m'minda, naoke mipesa, ndiyo yakubala zipatso zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 21:43

Chifukwa chake ndinena kwa inu, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:58

Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:7-9

Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta. Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m'thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha. Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:23-24

chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ai; podziwa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya cholowa; mutumikira Ambuye Khristu mwaukapolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:28

Koma pamene ndikatsiriza ichi, ndi kuwasindikizira iwo chipatso ichi, ndidzapyola kwanu kupita ku Spaniya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 128:2

Pakuti udzadya za ntchito ya manja ako; wodala iwe, ndipo kudzakukomera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 20:35

M'zinthu zonse ndinakupatsani chitsanzo, chakuti pogwiritsa ntchito, kotero muyenera kuthandiza ofooka ndi kukumbuka mau a Ambuye Yesu, kuti anati yekha, Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:42

Ndipo aliyense amene adzamwetsa mmodzi wa ang'ono awa chikho chokha cha madzi ozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 15:5

Ndalama zake sakongoletsa mofuna phindu lalikulu, ndipo salandira chokometsera mlandu kutsutsa wosachimwa. Munthu wakuchita izi sadzagwedezeka kunthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 32:17

Ndi ntchito ya chilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata chilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika kunthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:10

monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 4:36

Wakumweta alandira kulipira, nasonkhanitsira chobala kumoyo wosatha; kuti wofesayo akakondwere pamodzi ndi womwetayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22

Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:22

Koma tsopano, pamene munamasulidwa kuuchimo, ndi kukhala akapolo a Mulungu, muli nacho chobala chanu chakufikira chiyeretso, ndi chimaliziro chake moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 9:7

Msilikali ndani achita nkhondo, nthawi iliyonse, nadzifunira zake yekha? Aoka mipesa ndani, osadya chipatso chake? Kapena aweta gulu ndani, osadya mkaka wake wa gululo? Kodi ndilankhula izi monga mwa anthu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 26:9

Musandichotsere mzimu wanga pamodzi ndi olakwa, kapena moyo wanga pamodzi ndi anthu okhetsa mwazi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:2

Ndipo ananena kwa iwo, Dzinthu dzichuluka, koma antchito achepa; potero pemphani Mwini dzinthu, kuti akankhe antchito kukututa kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:25

Mtima wa mataya udzalemera; wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 30:5

Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 52:8

Koma ine ndine ngati mtengo wauwisi wa azitona m'nyumba ya Mulungu. Ndikhulupirira chifundo cha Mulungu kunthawi za nthawi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:3

ndikakonzere iwo amene alira maliro mu Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 1:29-30

Ndipo anati Mulungu, Taonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbeu lili padziko lapansi, ndi mitengo yonse m'mene muli chipatso cha mtengo wakubala mbeu; chidzakhala chakudya cha inu: Ndipo anati Mulungu, Kuyere; ndipo kunayera. ndiponso ndapatsa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi zokwawa zonse za dziko lapansi m'mene muli moyo, therere laliwisi lonse likhale chakudya: ndipo kunatero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:3

Khulupirira Yehova, ndipo chita chokoma; khala m'dziko, ndipo tsata choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:10-11

Ndipo iye wopatsa mbeu kwa wofesa, ndi mkate ukhale chakudya, adzapatsa ndi kuchulukitsa mbeu yanu yofesa, nadzaonjezapo pa zipatso za chilungamo chanu; polemeretsedwa inu m'zonse kukuolowa manja konse, kumene kuchita mwa ife chiyamiko cha kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 3:2

mphindi yakubadwa ndi mphindi yakumwalira; mphindi yakubzala ndi mphindi yakuzula zobzalazo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:18

kuti achite zabwino, nachuluke ndi ntchito zabwino, nakondwere kugawira ena, nayanjane;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 72:7

Masiku ake wolungama adzakhazikika; ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:7-8

Pakuti nthaka imene idamwa mvula iigwera kawirikawiri, nipatsa therere loyenera iwo amene adailimira, ilandira dalitso lochokera kwa Mulungu: koma ikabala minga ndi mitungwi, itayika; nitsala pang'ono ikadatembereredwa; chitsiriziro chake ndicho kutenthedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:16

Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:1-2

Odala angwiro m'mayendedwe ao, akuyenda m'chilamulo cha Yehova. Ndinakufunani ndi mtima wanga wonse; ndisasokere kusiyana nao malamulo anu. Ndizindikira koposa okalamba popeza ndinasunga malangizo anu. Ndinaletsa mapazi anga njira iliyonse yaoipa, kuti ndisamalire mau anu. Sindinapatukane nao maweruzo anu; pakuti Inu munandiphunzitsa. Mau anu azunadi powalawa ine! Koposa uchi m'kamwa mwanga. Malangizo anu andizindikiritsa; chifukwa chake ndidana nao mayendedwe onse achinyengo. Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga. Ndinalumbira, ndipo ndinatsimikiza mtima, kuti ndidzasamalira maweruzo anu olungama. Ndazunzika kwambiri: Ndipatseni moyo, Yehova, monga mwa mau anu. Landirani, Yehova, zopereka zaufulu za pakamwa panga, ndipo ndiphunzitseni maweruzo anu. Moyo wanga ukhala m'dzanja langa chikhalire; koma sindiiwala chilamulo chanu. Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu. Oipa ananditchera msampha; koma sindinasokere m'malangizo anu. Ndinalandira mboni zanu zikhale cholandira chosatha; pakuti ndizo zokondweretsa mtima wanga. Ndinalingitsa mtima wanga uchite malemba anu, kosatha, kufikira chimaliziro. Ndidana nao a mitima iwiri; koma ndikonda chilamulo chanu. Inu ndinu pobisalapo panga, ndi chikopa changa; ndiyembekezera mau anu. Mundichokere ochita zoipa inu; kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga. Mundichirikize monga mwa mau anu, kuti ndikhale ndi moyo; ndipo ndisachite manyazi pa chiyembekezo changa. Mundigwirizize ndipo ndidzapulumutsidwa, ndipo ndidzasamalira malemba anu chisamalire. Mupepula onse akusokera m'malemba anu; popeza chinyengo chao ndi bodza. Muchotsa oipa onse a padziko lapansi ngati mphala: Chifukwa chake ndikonda mboni zanu. Inu ndinu wodala Yehova; ndiphunzitseni malemba anu. Thupi langa linjenjemera ndi kuopa Inu; ndipo ndichita mantha nao maweruzo anu. Ndinachita chiweruzo ndi chilungamo; musandisiyira akundisautsa. Mumkhalire chikole mtumiki wanu chimkomere; odzikuza asandisautse. Maso anga anatha mphamvu pofuna chipulumutso chanu, ndi mau a chilungamo chanu. Muchitire mtumiki wanu monga mwa chifundo chanu, ndipo ndiphunzitseni malemba anu. Ine ndine mtumiki wanu, ndizindikiritseni; kuti ndidziwe mboni zanu. Yafika nyengo yakuti Yehova achite kanthu; pakuti anaswa chilamulo chanu. Chifukwa chake ndikonda malamulo anu koposa golide, inde golide woyengeka. Chifukwa chake ndiyesa ngolunjika malangizo anu onse akunena zonse; koma ndidana nazo njira zonse zonyenga. Mboni zanu nzodabwitsa; chifukwa chake moyo wanga uzisunga. Ndinafotokozera ndi milomo yanga maweruzo onse a pakamwa panu. Potsegulira mau anu paunikira; kuzindikiritsa opusa. Ndinatsegula pakamwa panga, ndi kupuma wefuwefu; popeza ndinakhumba malamulo anu. Munditembenukire, ndi kundichitira chifundo, monga mumatero nao akukonda dzina lanu. Khazikitsani mapazi anga m'mau anu; ndipo zisandigonjetse zopanda pake zilizonse. Mundiombole kunsautso ya munthu: Ndipo ndidzasamalira malangizo anu. Muwalitse nkhope yanu pa mtumiki wanu; ndipo mundiphunzitse malemba anu. Maso anga atsitsa mitsinje ya madzi, popeza sasamalira chilamulo chanu. Inu ndinu wolungama, Yehova, ndipo maweruzo anu ndiwo olunjika. Mboni zanuzo mudazilamulira zili zolungama ndi zokhulupirika ndithu. Changu changa chinandithera, popeza akundisautsa anaiwala mau anu. Ndinakondwera m'njira ya mboni zanu, koposa ndi chuma chonse. Mau anu ngoyera ndithu; ndi mtumiki wanu awakonda. Wamng'ono ine, ndi wopepulidwa; koma sindiiwala malemba anu. Chilungamo chanu ndicho chilungamo chosatha; ndi chilamulo chanu ndicho choonadi. Kusautsika ndi kupsinjika kwandigwera; koma malamulo anu ndiwo ondikondweretsa ine. Mboni zanu ndizo zolungama kosatha; mundizindikiritse izi, ndipo ndidzakhala ndi moyo. Ndinaitana ndi mtima wanga wonse; mundiyankhe, Yehova; ndidzasunga malemba anu. Ndinaitanira Inu; ndipulumutseni, ndipo ndidzasamalira mboni zanu. Ndinafuula kusanake: ndinayembekezera mau anu. Maso anga anakumana ndi maulonda a usiku, kuti ndilingirire mau anu. Imvani liu langa monga mwa chifundo chanu; mundipatse moyo monga mwa kuweruza kwanu, Yehova. Ndidzalingirira pa malangizo anu, ndi kupenyerera mayendedwe anu. Otsata zachiwembu andiyandikira; akhala kutali ndi chilamulo chanu. Inu muli pafupi, Yehova; ndipo malamulo anu onse ndiwo choonadi. Kuyambira kale ndinadziwa mu mboni zanu, kuti munazikhazika kosatha. Penyani kuzunzika kwanga, nimundilanditse; pakuti sindiiwala chilamulo chanu. Mundinenere mlandu wanga, nimundiombole; mundipatse moyo monga mwa mau anu. Chipulumutso chitalikira oipa; popeza safuna malemba anu. Zachifundo zanu ndi zazikulu, Yehova; mundipatse moyo monga mwa maweruzo anu. Ondilondola ndi ondisautsa ndiwo ambiri; koma sindinapatukane nazo mboni zanu. Ndinapenya ochita monyenga, ndipo ndinanyansidwa nao; popeza sasamalira mau anu. Penyani kuti ndikonda malangizo anu; mundipatse moyo, Yehova, monga mwa chifundo chanu. Ndidzadzikondweretsa nao malemba anu; sindidzaiwala mau anu. Chiwerengero cha mau anu ndicho choonadi; ndi maweruzo anu olungama onse akhala kosatha. Nduna zinandilondola kopanda chifukwa; koma mtima wanga uchita nao mantha mau anu. Ndikondwera nao mau anu, ngati munthu wakupeza zofunkha zambiri. Ndidana nalo bodza ndi kunyansidwa nalo; koma ndikonda chilamulo chanu. Ndikulemekezani kasanu ndi kawiri, tsiku limodzi, chifukwa cha maweruzo anu olungama. Akukonda chilamulo chanu ali nao mtendere wambiri; ndipo alibe chokhumudwitsa. Ndinayembekeza chipulumutso chanu, Yehova, ndipo ndinachita malamulo anu. Moyo wanga unasamalira mboni zanu; ndipo ndizikonda kwambiri. Ndinasamalira malangizo anu ndi mboni zanu; popeza njira zanga zonse zili pamaso panu. Kufuula kwanga kuyandikire pamaso panu, Yehova; mundizindikiritse monga mwa mau anu. Muchitire chokoma mtumiki wanu kuti ndikhale ndi moyo; ndipo ndidzasamalira mau anu. Kupemba kwanga kudze pamaso panu; mundilanditse monga mwa mau anu. Milomo yanga itulutse chilemekezo; popeza mundiphunzitsa malemba anu. Lilime langa liimbire mau anu; pakuti malamulo anu onse ndiwo olungama. Dzanja lanu likhale lakundithandiza; popeza ndinasankha malangizo anu. Ndinakhumba chipulumutso chanu, Yehova; ndipo chilamulo chanu ndicho chondikondweretsa. Mzimu wanga ukhale ndi moyo, ndipo udzakulemekezani; ndipo maweruzo anu andithandize. Ndinasochera ngati nkhosa yotayika; funani mtumiki wanu; pakuti sindiiwala malamulo anu. Munditsegulire maso, kuti ndipenye zodabwitsa za m'chilamulo chanu. Ine ndine mlendo padziko lapansi; musandibisire malamulo anu. Odala iwo akusunga mboni zake, akumfuna ndi mtima wonse;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:1-2

Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera. M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu; musakhale aulesi m'machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye; kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera. Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo. Dalitsani iwo akuzunza inu; dalitsani, musawatemberere. Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira. Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nao odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha. Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye. Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:10

M'menemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a mdierekezi: yense wosachita chilungamo siali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:15-16

koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu; kuchokera mwa Iye thupi lonse, lolukidwa ndi lolumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kuchititsa kwa chiwalo chonse pa muyeso wake, lichita makulidwe a thupi, kufikira chimango chake mwa chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:13

Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:172

Lilime langa liimbire mau anu; pakuti malamulo anu onse ndiwo olungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:6-7

Ndinaoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa. Chotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:5-6

chifukwa cha chiyembekezo chosungikira kwa inu mu Mwamba, chimene mudachimva kale m'mau a choonadi cha Uthenga Wabwino, umene udafikira kwa inu; monganso m'dziko lonse lapansi umabala zipatso, numakula, monganso mwa inu, kuyambira tsikulo mudamva nimunazindikira chisomo cha Mulungu m'choonadi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 13:6-9

Ndipo Iye ananena fanizo ili: Munthu wina anali ndi mkuyu wooka m'munda wake wampesa. Ndipo anadza nafuna chipatso pa uwu, koma anapeza palibe. Ndipo anati kwa wosungira munda wampesa, Taona, zaka zapita zitatu ndimadza ine kudzafuna chipatso pa mkuyu uwu, ndipo ndimapeza palibe: taulikha; uyeseranjinso nthaka yopanda pake? Ndipo iye anayankha nanena naye, Mbuye, baulekani ngakhale chaka chino chomwe, kufikira ndidzaukumbira kwete, ndithirepo ndowe; ndipo ngati udzabala chipatso kuyambira pamenepo, chabwino; koma ngati iai, mudzaulikhatu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:21-22

Ndipo munali nazo zobala zanji nthawi ija, m'zinthu zimene muchita nazo manyazi tsopano? Pakuti chimaliziro cha zinthu izi chili imfa. Koma tsopano, pamene munamasulidwa kuuchimo, ndi kukhala akapolo a Mulungu, muli nacho chobala chanu chakufikira chiyeretso, ndi chimaliziro chake moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 72:16

M'dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa, ngati za ku Lebanoni, ndipo iwo a m'mizinda adzaphuka ngati msipu wapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 1:8

Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ndi mu Yudeya monse, ndi mu Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:13

Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:5

chifukwa cha chiyanjano chanu chakuthandizira Uthenga Wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:6-8

Koma nditi ichi, kuti iye wakufesa mouma manja, mouma manjanso adzatuta. Ndipo iye wakufesa moolowa manja, moolowa manjanso adzatuta. Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera. Ndipo Mulungu akhoza kuchulukitsira chisomo chonse kwa inu; kuti inu, pokhala nacho chikwaniro chonse m'zinthu zonse, nthawi zonse, mukachulukire kuntchito yonse yabwino;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:38

Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:1

Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:14-30

Pakuti monga munthu, wakunka ulendo, aitana akapolo ake, napereka kwa iwo chuma chake. Ndipo mmodzi anampatsa ndalama za matalente zisanu, ndi wina ziwiri, ndi wina imodzi; kwa iwo onse monga nzeru zao; namuka iye. Pomwepo uyo amene analandira matalente asanu, anapita kugula nazo malonda, napindulapo matalente ena asanu. Chimodzimodzi uyo wa awiriwo, anapindulapo ena awiri. Koma uyo amene analandira imodziyo anamuka, nakumba pansi, naibisa talente ya mbuye wake. Ndipo itapita nthawi yaikulu, anabwera mbuye wa akapolo awo, nawerengera nao pamodzi. Ndipo asanu a iwo anali opusa, ndi asanu anali ochenjera. Ndipo uyo amene adalandira matalente asanu anadza, ali nawo matalente ena asanu, nanena, Mbuye, munandipatsa matalente asanu, onani ndapindulapo matalente ena asanu. Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako. Ndipo wa matalente awiriwo anadzanso, nati, Mbuye, munandipatsa ine matalente awiri; onani, ndapindulapo matalente ena awiri. Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako. Ndipo uyonso amene analandira talente imodzi, anadza, nati, Mbuye, ndinakudziwani inu kuti ndinu munthu wouma mtima, wakututa kumene simunafese, ndi wakusonkhanitsa kumene simunawaze; ndinaopa ine, ndinapita, ndinabisa pansi talente yanu: onani, siyi talente yanuyo. Koma mbuye wake anayankha, nati kwa iye, Kapolo iwe woipa ndi waulesi, unadziwa kuti ndimatuta kumene sindinafese, ndi kusonkhanitsa kumene sindinawaze; chifukwa chake ukadapereka ndalama zanga kwa okongola ndalama, ndipo ine pobwera ndikadatenga zanga ndi phindu lake. Chifukwa chake chotsani kwa iye ndalamayo, muipatse kwa amene ali nazo ndalama khumi. Pakuti kwa yense amene ali nazo, kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zochuluka: koma kwa iye amene alibe, kudzachotsedwa, chingakhale chimene anali nacho. Pakuti opusawo, m'mene anatenga nyali zao, sanadzitengerenso mafuta; Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pake kumdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:11

musakhale aulesi m'machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:10

wa mbiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a oyera mtima, ngati wathandiza osautsidwa, ngati anatsatadi ntchito zonse zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 5:1

Ndiimbire wokondedwa wanga nyimbo ya wokondedwa wanga ya munda wake wampesa. Wokondedwa wanga anali ndi munda wampesa m'chitunda cha zipatso zambiri;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:19

Pakuti chiyembekezetso cha cholengedwa chilindira vumbulutso la ana a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:4

Khalani mwa Ine, ndi Ine mwa inu. Monga nthambi siingathe kubala chipatso pa yokha, ngati siikhala mwampesa; motere mulibe inunso ngati simukhala mwa Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:18

Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 8:22

Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthawi yakubzala ndi yakukunkha, chisanu ndi mafundi, malimwe ndi msakasa, usana ndi usiku sizidzalekai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 126:5

Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 37:31

Ndipo otsala amene opulumuka a nyumba ya Yuda adzaphukanso mizu pansi, nadzabala chipatso pamwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:17

Sikunena kuti nditsata choperekacho, komatu nditsata chipatso chakuchulukira ku chiwerengero chanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 127:3-5

Taonani, ana ndiwo cholowa cha kwa Yehova; chipatso cha m'mimba ndicho mphotho yake. Ana a ubwana wake wa munthu akunga mivi m'dzanja lake la chiphona. Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake: sadzachita manyazi iwo, pakulankhula nao adani kuchipata.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:2

Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:31

Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:3

Pereka zochita zako kwa Yehova, ndipo zolingalira zako zidzakhazikika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:105

Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 10:15

Ndipo adzalalikira bwanji, ngati satumidwa? Monganso kwalembedwa, Okometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira Uthenga Wabwino wa zinthu zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:19-20

Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: Ndipo onani, panali chivomezi chachikulu; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake. ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 9:19-23

Pakuti pokhala ndinali mfulu kwa onse, ndinadzilowetsa ndekha ukapolo kwa onse, kuti ndipindule ochuluka. Ngati sindili mtumwi kwa ena, komatu ndili kwa inu; pakuti chizindikiro cha utumwi wanga ndi inu mwa Ambuye. Ndipo kwa Ayuda ndinakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda; kwa iwo omvera lamulo monga womvera lamulo, ngakhale sindinakhale ndekha womvera lamulo, kuti ndipindule iwo omvera malamulo; kwa iwo opanda lamulo monga wopanda lamulo, wosati wakukhala ine wopanda lamulo kwa Mulungu, koma womvera lamulo kwa Khristu kuti ndipindule iwo opanda lamulo. Kwa ofooka ndinakhala ngati wofooka, kuti ndipindule ofooka. Ndakhala zonse kwa anthu onse, kuti paliponse ndikapulumutse ena. Koma ndichita zonse chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti ndikakhale woyanjana nao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:10

Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:14

ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Chauta wanga wachikondi ndi wamuyaya, Ambuye Wamkulukulu, m'dzina la Yesu ndikubwera kwa Inu, Inu nokha ndinu woyenera kutamandidwa ndi kupembedzedwa kwakukulu. Atate wabwino ndi wachifundo! Ndikukuthokozani chifukwa cha mphatso ya chipulumutso chifukwa kudzera m'mtanda mudatichotsera machimo athu onse. Inu munati m'mawu anu: "Ndabwera kudzapulumutsa otaika." Ndikukupemphani kuti uthenga wanu wabwino wa chipulumutso ukafike kulikonse padziko lapansi ndipo ena alandire ndi kusangalala ndi madalitso akulu omwe uthenga wanu wokongola umatipatsa. Mwandilanditsa ku chiweruzo chamuyaya, mwandimasula ku ukapolo wa uchimo ndi kundipulumutsa ku misampha ya msampha. Zikomo chifukwa mwandigwirizanitsa ndi Atate, mwandipatsa chikhululukiro chanu, chikondi chanu ndi chipulumutso chanu. Ndikukupemphani kuti mawu anu ayende ngati mtsinje, akutsuka ndi kukonzanso miyoyo ya amuna, akazi ndi ana. M'dzina la Yesu. Ameni!
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa