Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Akolose 1:10 - Buku Lopatulika

10 kuti mukayenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m'chizindikiritso cha Mulungu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 kuti mukayenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m'chizindikiritso cha Mulungu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Pamenepo mudzatha kuyenda m'njira zimene Ambuye amafuna, ndi kuŵakondweretsa pa zonse. Pakugwira ntchito zabwino zamitundumitundu, moyo wanu udzaonetsa zipatso, ndipo mudzanka muwonjezerawonjezera nzeru zanu za kudziŵa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ndipo tikupempherera zimenezi ndi cholinga chakuti inu mukhale moyo oyenera Ambuye ndi kumukondweretsa mʼnjira zonse. Kubereka chipatso pa ntchito iliyonse yabwino, ndi kukula mʼchidziwitso cha Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




Akolose 1:10
44 Mawu Ofanana  

Njira za munthu zikakonda Yehova ayanjanitsana naye ngakhale adani ake.


Iye adzaona zotsatira mavuto a moyo wake, nadzakhuta nazo; ndi nzeru zake mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri, nadzanyamula mphulupulu zao.


Koma iwe Daniele, tsekera mau awa, nukomere chizindikiro buku, mpaka nthawi ya chimaliziro; ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziwitso chidzachuluka.


Pakuti mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m'dzina la mulungu wake, ndipo ife tidzayenda m'dzina la Yehova Mulungu wathu kunthawi yonka muyaya.


Pakuti dziko lapansi lidzadzazidwa ndi chidziwitso cha ulemerero wa Yehova, monga madzi amphimba pansi pa nyanja.


Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala chipatso, ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chilichonse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu.


Mwa ichi alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale chipatso chambiri; ndipo mudzakhala ophunzira anga.


Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Khristu amene munamtuma.


Ndipo sindifuna kuti inu, abale, mudzakhala osadziwa, kuti kawirikawiri ndikanena mumtima kuti ndikafike kwa inu, koma ndaletsedwa kufikira lero, kuti ndikaone zobala zina mwa inunso, monga mwa anthu amitundu ena.


ndiponso kholo la mdulidwe wa iwo amene siali a mdulidwe okha, koma wa iwo amene atsata mayendedwe a chikhulupiriro chija cha kholo lathu Abrahamu, chimene iye anali nacho asanadulidwe.


Chifukwa chake tinaikidwa m'manda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Khristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, chotero ifenso tikayende m'moyo watsopano.


Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m'chigonjetso mwa Khristu, namveketsa fungo la chidziwitso chake mwa ife pamalo ponse.


Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu.


Chifukwa chakenso tifunitsitsa, kapena kwathu kapena kwina, kukhala akumkondweretsa Iye.


Ndipo Mulungu akhoza kuchulukitsira chisomo chonse kwa inu; kuti inu, pokhala nacho chikwaniro chonse m'zinthu zonse, nthawi zonse, mukachulukire kuntchito yonse yabwino;


kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa vumbulutso kuti mukamzindikire Iye;


Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.


Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nao,


kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso cha Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Khristu.


kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani;


Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru;


ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.


odzala nacho chipatso cha chilungamo, chimene chili mwa Yesu Khristu, kuchitira Mulungu ulemerero ndi chiyamiko.


Chokhachi, mayendedwe anu ayenere Uthenga Wabwino wa Khristu: kuti, ndingakhale nditi ndilinkudza ndi kuona inu, ndingakhale nditi ndili kwina, ndikamva za kwa inu, kuti muchilimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino;


Koma ndili nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidachokera kwanu, mnunkho wa fungo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.


kuchokera kwa Iye amene thupi lonse, lothandizidwa ndi kulumikizidwa pamodzi mwa mfundo ndi mitsempha, likula ndi makulidwe a Mulungu.


Chifukwa chake monga momwe munalandira Khristu Yesu Ambuye, muyende mwa Iye,


Ana inu, mverani akubala inu m'zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho.


Muyendere munzeru ndi iwo akunja, kuchita machawi nthawi ingatayike.


ndi kukudandaulirani, ndi kukusangalatsani ndi kuchita umboni, kuti muyende koyenera Mulungu, amene akuitanani inu mulowe ufumu wake wa Iye yekha, ndi ulemerero.


Chotsalira tsono, abale, tikupemphani ndi kukudandaulirani mwa Ambuye Yesu, kuti, monga munalandira kwa ife mayendedwe okoma, muyenera kuyendanso ndi kukondweretsa Mulungu, monganso mumayenda, chulukani koposa momwemo.


Msilikali sakodwa nazo ntchito wamba, kuti akakondweretse iye amene adamlemba usilikali.


Uwakumbutse iwo agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera, okonzeka pa ntchito iliyonse yabwino;


Ndipo anthu athu aphunzirenso asunge ntchito zabwino zofunika, kuti asakhale osabala zipatso.


Ndi chikhulupiriro Enoki anatengedwa kuti angaone imfa; ndipo sanapezeke, popeza Mulungu adamtenga: pakuti asanamtenge, anachitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu;


Koma musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.


akuyeseni inu opanda chilema m'chinthu chilichonse chabwino, kuti muchite chifuniro chake; ndi kuchita mwa ife chomkondweretsa pamaso pake, mwa Yesu Khristu; kwa Iyeyu ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.


Pakuti izi zikakhala ndi inu, ndipo zikachuluka, zidzachita kuti musakhale aulesi kapena opanda zipatso pa chizindikiritso cha Ambuye Yesu Khristu.


Koma kulani m'chisomo ndi chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu; kwa Iye kukhale ulemerero, tsopano ndi nthawi zonse. Amen.


ndipo chimene chilichonse tipempha, tilandira kwa Iye, chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zomkondweretsa pamaso pake.


Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.


amene anachita umboni za chikondi chako pamaso pa Mpingo; ngati uwaperekeza amenewo pa ulendo wao koyenera Mulungu, udzachita bwino:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa