Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 1:29 - Buku Lopatulika

29 Ndipo anati Mulungu, Taonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbeu lili padziko lapansi, ndi mitengo yonse m'mene muli chipatso cha mtengo wakubala mbeu; chidzakhala chakudya cha inu:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Ndipo anati Mulungu, Taonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbeu lili pa dziko lapansi, ndi mitengo yonse m'mene muli chipatso cha mtengo wakubala mbeu; chidzakhala chakudya cha inu:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Ndipo Mulungu adati, “Ndikukupatsani zomera zonse za mtundu wokhala njere, ndi mitundu yonse ya zomera zobala zipatso zanjere, kuti muzidya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Kenaka Mulungu anati, “Ine ndakupatsani chomera chilichonse cha pa dziko lapansi chimene chili ndi mbewu komanso mtengo uliwonse wobala zipatso zokhala ndi mbewu mʼkati mwake kuti zikhale chakudya chanu.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 1:29
22 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova Mulungu anamuuza munthuyo, nati, Mitengo yonse ya m'munda udyeko;


Ndipo iwe udzitengereko wekha zakudya zonse zodyedwa, nudzisonkhanitsire izi wekha: ndipo zidzakhala zakudya za iwe ndi za iwo.


Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo.


Pakuti aweruza nazo mitundu ya anthu apatsa chakudya chochuluka.


Anapatsa akumuopa Iye chakudya; adzakumbukira chipangano chake kosatha.


Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.


Ndiye wakupatsa nyama zonse chakudya; pakuti chifundo chake nchosatha.


ndiye wakuchitira chiweruzo osautsika; ndiye wakupatsa anjala chakudya; Yehova amasula akaidi.


Amene apatsa zoweta chakudya chao, ana a khwangwala alikulira.


Dziko lapansi nla Yehova ndi zodzala zake zomwe, dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhala m'mwemo.


iye adzakhala pamsanje; malo ake ochinjikiza adzakhala malinga amiyala; chakudya chake chidzapatsidwa kwa iye; madzi ake adzakhala chikhalire.


Pakuti sanadziwe kuti ndine ndinampatsa tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi kumchulukitsira siliva ndi golide, zimene anapanga nazo Baala.


Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero.


Koma sanadzisiyire Iye mwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero.


pakuti mwa Iye tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda, ndi kupeza mkhalidwe wathu; monga enanso a akuimba anu ati, Pakuti ifenso tili mbadwa zake.


a kuletsa ukwati, osiyitsa zakudya zakuti, zimene Mulungu anazilenga kuti achikhulupiriro ndi ozindikira choonadi azilandire ndi chiyamiko.


Lamulira iwo achuma m'nthawi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa