Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mateyu 12:33 - Buku Lopatulika

33 Ukakoma mtengo, chipatso chake chomwe chikoma; ukaipa mtengo, chipatso chake chomwe chiipa; pakuti ndi chipatso chake mtengo udziwika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

33 Ukakoma mtengo, chipatso chake chomwe chikoma; ukaipa mtengo, chipatso chake mtengo udziwika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

33 “Mukanena kuti, ‘Mtengo uwu ngwabwino,’ ndiye kuti zipatso zakenso nzabwino. Koma mukanena kuti, ‘Mtengo uwu ngwoipa,’ ndiye kuti zipatso zakenso nzoipa. Pajatu mtengo umadziŵika ndi zipatso zake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

33 “Mtengo wabwino umabala zipatso zabwino ndipo mtengo woyipa umabalanso zipatso zoyipa, pajatu mtengo umadziwika ndi zipatso zake.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 12:33
11 Mawu Ofanana  

Tayani, ndi kudzichotsera zolakwa zanu zonse zimene munalakwa nazo, ndi kudzifunira mtima watsopano, ndi mzimu watsopano; pakuti mudzaferanji inu, nyumba ya Israele?


Danani nacho choipa, nimukonde chokoma; nimukhazikitse chiweruzo kuchipata; kapena Yehova Mulungu wa makamu adzachitira chifundo otsala a Yosefe.


Mfarisi iwe wakhungu, yambawatsuka m'kati mwa chikho ndi mbale, kuti kunja kwake kukhalenso koyera.


Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo; chotero mtengo uliwonse wosabala chipatso chabwino udulidwa, nuponyedwa pamoto.


Kodi mkuyu ukhoza kubala azitona, abale anga, kapena mpesa kubala nkhuyu? Kotero madzi amchere sangathe kutulutsa okoma.


Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m'manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa