Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 12:11 - Buku Lopatulika

11 Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondwetsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Palibe chilango chimene chimaoneka kuti ndi chabwino pa nthawiyo, komatu chowawa. Koma pambuyo pake, chimabweretsa chipatso chachilungamo ndi mtendere kwa iwo amene aleredwa mwa njira imeneyi.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 12:11
20 Mawu Ofanana  

Ndipo mauwo anaipira Abrahamu chifukwa cha mwana wake.


Kulanga anandilangadi Yehova: koma sanandipereke kuimfa ai.


Akukonda chilamulo chanu ali nao mtendere wambiri; ndipo alibe chokhumudwitsa.


Pamenepo ndidzazonda zolakwa zao ndi ndodo, ndi mphulupulu zao ndi mikwingwirima.


Wosiya njira adzalangidwa mowawa; wakuda chidzudzulo adzafa.


Menya mwanako, chiyembekezero chilipo, osafunitsa kumuononga.


Ndipo Yehova adzakantha Ejipito kukantha ndi kuchiritsa; ndipo iwo adzabwerera kwa Yehova, ndipo Iye adzapembedzedwa ndi iwo, nadzawachiritsa.


Ndi ntchito ya chilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata chilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika kunthawi zonse.


Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.


Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero;


chotsalira wandiikira ine korona wa chilungamo, amene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa ine tsiku lijalo: ndipo si kwa ine ndekha, komatunso kwa onse amene anakonda maonekedwe ake.


Pakutitu iwo anatilanga masiku owerengeka monga kudawakomera; koma Iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nao pa chiyero chake.


Koma chakudya chotafuna chili cha anthu aakulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloweretsa zizindikiritso zao kusiyanitsa chabwino ndi choipa.


M'menemo mukondwera, kungakhale tsopano kanthawi, ngati kuyenera, mukachitidwe chisoni ndi mayesero a mitundumitundu,


okhala nao maso odzala ndi chigololo, osakhoza kuleka uchimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa