Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 1:8 - Buku Lopatulika

8 Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ndi mu Yudeya monse, ndi mu Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Koma mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera akadzabwera pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi ku Samariya konse, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Koma mudzalandira mphamvu Mzimu Woyera akadzafika pa inu; ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 1:8
34 Mawu Ofanana  

Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira nadzatembenukira kwa Yehova, ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu.


Anakumbukira chifundo chake ndi chikhulupiriko chake kunyumba ya Israele; malekezero onse a dziko lapansi anaona chipulumutso cha Mulungu wathu.


Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, ndi matamando ake kuchokera ku malekezero a dziko lapansi; inu amene mutsikira kunyanja, ndi zonse zili m'menemo, zisumbu ndi okhala mommo.


inde, ati, Chili chinthu chopepuka ndithu kuti Iwe ukhale mtumiki wanga wakuutsa mafuko a Yakobo, ndi kubwezera osungika a Israele; ndidzakupatsanso ukhale kuunika kwa amitundu, kuti ukhale chipulumutso changa mpaka ku malekezero a dziko lapansi.


Yehova wavula mkono wake woyera pamaso pa amitundu onse; ndi malekezero onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.


Ndipo ndidzaika chizindikiro pakati pao, ndipo ndidzatumiza onse amene apulumuka mwa iwo kwa amitundu, kwa Tarisisi, kwa Puti ndi kwa Aludi, okoka uta kwa Tubala ndi Yavani, kuzisumbu zakutali, amene sanamve mbiri yanga, ngakhale kuona ulemerero wanga; ndipo adzabukitsa ulemerero wanga pakati pa amitundu.


Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko, amitundu adzadza kwa Inu kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira cholowa cha bodza lokha, zopanda pake ndi zinthu zosapindula nazo.


Koma ine ndidzala nayo mphamvu mwa Mzimu ya Yehova, ndi chiweruzo, ndi chamuna, kufotokozera Yakobo kulakwa kwake, ndi kwa Israele tchimo lake.


Pamenepo anayankha, nanena kwa ine, ndi kuti, Awa ndi mau a Yehova kwa Zerubabele, Ndi khamu la nkhondo ai, ndi mphamvu ai, koma ndi Mzimu wanga, ati Yehova wa makamu.


Ndipo Uthenga uwu Wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.


Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:


Ndipo ananena nao, Mukani kudziko lonse lapansi, lalikirani Uthenga Wabwino kwa olengedwa onse.


Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: chifukwa chakenso Choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu.


Taonani, ndakupatsani ulamuliro wakuponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi pa mphamvu iliyonse ya mdaniyo; ndipo kulibe kanthu kadzakuipsani konse.


Ndipo anamuumiriza Iye, nati, Khalani ndi ife; pakuti kuli madzulo, ndipo dzuwa lapendekatu. Ndipo analowa kukhala nao.


Ndipo inunso muchita umboni, pakuti muli ndi Ine kuyambira chiyambi.


kuyambira ubatizo wa Yohane, kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba kutisiya ife, mmodzi wa awa akhale mboni ya kuuka kwake pamodzi ndi ife.


pakuti Yohane anabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera, asanapite masiku ambiri.


ndipo anaonekera masiku ambiri ndi iwo amene anamperekeza Iye pokwera ku Yerusalemu kuchokera ku Galileya, amenewo ndiwo akumchitira umboni tsopano kwa anthu.


Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa; za ichi tili mboni ife tonse.


Ndipo udzamkhalira Iye mboni kwa anthu onse, za izo udaziona ndi kuzimva.


ndipo munamupha Mkulu wa moyo; amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa; za ichi ife tili mboni.


Ndipo atumwi anachita umboni ndi mphamvu yaikulu za kuuka kwa Ambuye Yesu; ndipo panali chisomo chachikulu pa iwo onse.


Ndipo ife ndife mboni za zinthu izi; Mzimu Woyeranso, amene Mulungu anapatsa kwa iwo akumvera Iye.


Ndipo Stefano, wodzala ndi chisomo ndi mphamvu, anachita zozizwa ndi zizindikiro zazikulu mwa anthu.


Ndipo Saulo analikuvomerezana nao pa imfa yake. Ndipo tsikulo kunayamba kuzunza kwakukulu pa Mpingo unali mu Yerusalemu; ndipo anabalalitsidwa onse m'maiko a Yudeya ndi Samariya, koma osati atumwi ai.


Koma ine nditi, Sanamva iwo kodi! Indetu, Liu lao linatulukira kudziko lonse lapansi, ndi maneno ao ku malekezero a dziko lokhalamo anthu.


mu mphamvu ya zizindikiro ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iliriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Khristu;


ngatitu, mukhalabe m'chikhulupiriro, ochilimika ndi okhazikika ndi osasunthika kulekana nacho chiyembekezo cha Uthenga Wabwino umene mudaumva, wolalikidwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo; umene ine Paulo ndakhala mtumiki wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa