Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 1:7 - Buku Lopatulika

7 Koma anati kwa iwo, Sikuli kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo, zimene Atate anaziika mu ulamuliro wake wa Iye yekha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Koma anati kwa iwo, Sikuli kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo, zimene Atate anaziika m'ulamuliro wake wa Iye yekha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Iye adati, “Si ntchito yanu kuti mudziŵe nthaŵi kapena nyengo pamene zidzachitike zimene Atate adakhazikitsa mwa mphamvu yao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Yesu anawawuza kuti, “Sikofunika kuti mudziwe za nthawi kapena masiku amene Atate ayika mwa ulamuliro wawo.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 1:7
13 Mawu Ofanana  

Wamphamvuyonse alekeranji kuikiratu nyengo? Ndi iwo omdziwa alekeranji kudziwa masiku ake?


pakuti amasanduliza nthawi ndi nyengo, achotsa mafumu, nalonga mafumu, apatsa anzeru nzeru, ndi chidziwitso kwa iwo okhoza kuzindikira.


Iye ananena kwa iwo, Chikho changa mudzamweradi; koma kukhala kudzanja lamanja kwanga ndi kulamanzere, sikuli kwanga kupatsa, koma kuli kwa iwo omwe kwakonzedweratu ndi Atate wanga.


Koma za tsiku ili ndi nthawi yake saidziwa munthu aliyense, angakhale angelo a Kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha.


koma kukhala kudzanja langa lamanja, kapena lamanzere sikuli kwanga kupatsa; koma kuli kwa iwo amene adawakonzeratu.


Koma za tsiku ilo, kapena nthawi yake sadziwa munthu, angakhale angelo mu Mwamba, angakhale Mwana, koma Atate ndiye.


Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka kumitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza Yerusalemu kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira.


ndipo ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi, atapangiratu nyengo zao, ndi malekezero a pokhala pao;


kuti pa makonzedwe a makwaniridwe a nyengozo, akasonkhanitse pamodzi zonse mwa Khristu, za kumwamba, ndi za padziko.


Zinsinsi nza Yehova Mulungu wathu; koma zovumbuluka nza ife ndi ana athu kosatha, kuti tichite mau onse a chilamulo ichi.


limene adzalionetsa m'nyengo za Iye yekha, amene ali Mwini Mphamvu wodala ndi wayekha, ndiye Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye;


Koma zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthawi zowawitsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa