Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 30:5 - Buku Lopatulika

5 Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Pakuti mkwiyo wake umakhala kwa kanthawi koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse; utha kuchezera kulira usiku wonse, koma chimwemwe chimabwera mmawa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 30:5
28 Mawu Ofanana  

Ndipo anatsala Yakobo yekha; ndipo analimbana naye munthu kufikira mbandakucha.


Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;


Sadzatsutsana nao nthawi zonse; ndipo sadzasunga mkwiyo wake kosatha.


Mundimvetse chifundo chanu mamawa; popeza ndikhulupirira Inu: Mundidziwitse njira ndiyendemo; popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.


Ntchito zanu zonse zidzakuyamikani, Yehova; ndi okondedwa anu adzakulemekezani.


Mudzandidziwitsa njira ya moyo, pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.


Mulungu ali m'kati mwake, sudzasunthika, Mulungu adzauthandiza mbandakucha.


Pakuti Mulungu ndiye mfumu ya dziko lonse lapansi; imbirani ndi chilangizo.


Koma ine, ndidzaimbira mphamvu yanu; inde ndidzaimbitsa chifundo chanu mamawa, pakuti Inu mwakhala msanje wanga, ndi pothawirapo ine tsiku la nsautso yanga.


Pakuti chifundo chanu chiposa moyo makomedwe ake; milomo yanga idzakulemekezani.


Kondwerani mwa Yehova, olungama inu; ndipo yamikani pokumbukira chiyero chake.


Ndipo Mulungu ananenanso kwa Mose, Ukatero ndi ana a Israele, Yehova Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili ndi dzina langa nthawi yosatha, ichi ndi chikumbukiro changa m'mibadwomibadwo.


Tsiku lomwelo udzati, Ndikuyamikani inu Yehova; pakuti ngakhale munandikwiyira, mkwiyo wanu wachoka, ndipo mutonthoza mtima wanga.


Idzani, anthu anga, lowani m'zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthawi kufikira mkwiyo utapita.


Tidziwe tsono, tilondole kudziwa Yehova; kutuluka kwake kwakonzekeratu ngati matanda kucha; ndipo adzatidzera ngati mvula, ngati mvula ya masika yakuthirira dziko.


Odala ali achisoni; chifukwa adzasangalatsidwa.


Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero;


Ndipo anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo, wonyezimira ngati krustalo, otuluka kumpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa.


Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa