Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 72:16 - Buku Lopatulika

16 M'dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa, ngati za ku Lebanoni, ndipo iwo a m'mizinda adzaphuka ngati msipu wapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 M'dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa, ngati za ku Lebanoni, ndipo iwo a m'mudzi adzaphuka ngati msipu wapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 M'dziko mukhale chakudya chambiri, pamwambanso pa mapiri pakhale dzinthu. Zipatso zake zichuluke ngati za ku Lebanoni, anthu ake achuluke m'mizindamo ngati udzu wakuthengo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Mulole kuti tirigu achuluke mʼdziko lonse; pamwamba pa mapiri pakhale tirigu. Zipatso zake zichuluke ngati za ku Lebanoni; zichuluke ngati udzu wakuthengo

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 72:16
23 Mawu Ofanana  

Ayuda ndi Aisraele anachuluka ngati mchenga wa kunyanja, namadya namamwa namakondwera.


Udzapezanso kuti mbeu zako zidzachuluka, ndi obala iwe ngati zitsamba za padziko.


Ndipo chinkana chiyambi chako chinali chaching'ono, chitsiriziro chako chidzachuluka kwambiri.


Mitengo ya Yehova yadzala ndi madzi; mikungudza ya ku Lebanoni imene anaioka;


Adzanga mvula yakugwa pa udzu wosenga, monga mvula yothirira dziko.


Kodi sikatsala kamphindi kakang'ono, ndipo Lebanoni adzasanduka munda wobalitsa, ndi munda wobalitsa udzayesedwa nkhalango?


Ndipo Mulungu adzapatsa mvula ya mbeu yako, ukaibzale m'nthaka; ndi mkate ndiwo phindu la nthaka, ndipo tirigu wake adzacha bwino ndi kuchuluka; tsiku limenelo ng'ombe zako zidzadya m'madambo aakulu.


kufikira mzimu udzathiridwa pa ife kuchokera kumwamba, ndi chipululu chidzasanduka munda wobalitsa, ndi munda wobalitsa udzayesedwa nkhalango.


Odala muli inu, amene mubzala m'mbali mwa madzi monse, amene muyendetsa mapazi a ng'ombe ndi bulu.


Lidzaphuka mochuluka ndi kusangalala, ngakhale kukondwa ndi kuimba; lidzapatsidwa ulemerero wa Lebanoni, ndi ukulu wa Karimele ndi Saroni; anthuwo adzaona ulemerero wa Yehova, ukulu wake wa Mulungu wathu.


Monga khamu la kuthambo silingathe kuwerengedwa, ndi mchenga wa kunyanja sungathe kuyesedwa; chomwecho ndidzachulukitsa mbeu za Davide mtumiki wanga, ndi Alevi akunditumikira Ine.


Ndipo m'masiku awa anaimirira Petro pakati pa abale, nati (gulu la anthu losonkhana pamalo pomwe ndilo ngati zana limodzi ndi makumi awiri),


Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.


Koma ambiri a iwo amene adamva mau anakhulupirira; ndipo chiwerengero cha amuna chinali ngati zikwi zisanu.


Ndipo ndinati kwa iye, Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo anati kwa ine, Iwo ndiwo akutuluka m'chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zao, naziyeretsa m'mwazi wa Mwanawankhosa.


Zitatha izi ndinapenya, taonani, khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliwerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuimirira kumpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala zovala zoyera, ndi makhwatha a kanjedza m'manja mwao;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa