Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -

Masalimo 72 - Buku Lopatulika


Za ufumu wa Mfumu yokoma
Salimo la Solomoni.

1 Patsani mfumu maweruzo anu, Mulungu, ndi mwana wa mfumu chilungamo chanu.

2 Potero adzanenera anthu anu mlandu ndi m'chilungamo, ndi ozunzika anu ndi m'chiweruzo.

3 Mapiri adzatengera anthu mtendere, timapiri tomwe, m'chilungamo.

4 Adzaweruza ozunzika a mwa anthu, adzapulumutsa ana aumphawi, nadzaphwanya wosautsa.

5 Adzakuopani momwe likhalira dzuwa ndi mwezi, kufikira mibadwomibadwo.

6 Adzanga mvula yakugwa pa udzu wosenga, monga mvula yothirira dziko.

7 Masiku ake wolungama adzakhazikika; ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi.

8 Ndipo adzachita ufumu kuchokera kunyanja kufikira kunyanja, ndi kuchokera ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko lapansi.

9 Okhala m'chipululu adzagwadira pamaso pake; ndi adani ake adzaluma nthaka.

10 Mafumu a ku Tarisisi ndi ku Zisumbuzo adzabwera nacho chopereka; mafumu a ku Sheba ndi Seba adzadza nazo mphatso.

11 Inde mafumu onse adzamgwadira iye, amitundu onse adzamtumikira.

12 Pakuti adzapulumutsa waumphawi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi.

13 Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi, nadzapulumutsa moyo wa aumphawi.

14 Adzaombola moyo wao ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wao udzakhala wa mtengo pamaso pake.

15 Ndipo iye adzakhala ndi moyo; ndipo adzampatsa golide wa ku Sheba; nadzampempherera kosalekeza; adzamlemekeza tsiku lonse.

16 M'dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa, ngati za ku Lebanoni, ndipo iwo a m'mizinda adzaphuka ngati msipu wapansi.

17 Dzina lake lidzakhala kosatha, momwe likhalira dzuwa dzina lake lidzamvekera zidzukulu. Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye; amitundu onse adzamutcha wodala.

18 Wolemekezeka Yehova Mulungu, Mulungu wa Israele, amene achita zodabwitsa yekhayo.

19 Ndipo dzina lake la ulemerero lidalitsike kosatha; ndipo dziko lonse lapansi lidzale nao ulemerero wake. Amen, ndi Amen.

20 Mapemphero a Davide mwana wa Yese atha.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi
Titsatireni:



Zotsatsa