Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 72:18 - Buku Lopatulika

18 Wolemekezeka Yehova Mulungu, Mulungu wa Israele, amene achita zodabwitsa yekhayo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Wolemekezeka Yehova Mulungu, Mulungu wa Israele, amene achita zodabwitsa yekhayo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Atamandike Chauta, Mulungu wa Israele. Iye yekha ndiye amene amachita zinthu zodabwitsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Matamando akhale kwa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israeli amene Iye yekha amachita ntchito zodabwitsa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 72:18
14 Mawu Ofanana  

Motero Davide analemekeza Yehova pamaso pa khamu lonse, nati Davide, Wolemekezedwa Inu, Yehova Mulungu wa Israele, Atate wathu ku nthawi zomka muyaya.


Ndipo Davide anati kwa khamu lonse, Mulemekeze tsono Yehova Mulungu wanu. Ndi khamu lonse linalemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao, nawerama, nalambira Yehova, ndi mfumu.


amene achita zazikulu ndi zosalondoleka, zinthu zodabwitsa zosawerengeka.


Wochita zazikulu zosasanthulika, ndi zodabwitsa zosawerengeka.


Wodala Yehova, Mulungu wa Israele, kuyambira kosayamba kufikira kosatha. Ndi anthu onse anene, Amen. Aleluya.


Amene yekha achita zodabwitsa zazikulu; pakuti chifundo chake nchosatha.


Wodalitsika Yehova, Mulungu wa Israele, kuchokera nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha. Amen, ndi Amen.


Inu Mulungu, ndinu woopsa m'malo oyera anu; Mulungu wa Israele ndiye amene apatsa anthu ake mphamvu ndi chilimbiko. Alemekezeke Mulungu.


Inu ndinu Mulungu wakuchita chodabwitsa; munazindikiritsa mphamvu yanu mwa mitundu ya anthu.


Munaombola anthu anu ndi mkono wanu, ndiwo ana a Yakobo, ndi a Yosefe.


Pakuti Inu ndinu wamkulu, ndi wakuchita zodabwitsa; Inu ndinu Mulungu, nokhanu.


Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano; popeza anachita zodabwitsa: Dzanja lake lamanja, mkono wake woyera, zinamchitira chipulumutso.


Afanana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera, woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa