Masalimo 15:5 - Buku Lopatulika5 Ndalama zake sakongoletsa mofuna phindu lalikulu, ndipo salandira chokometsera mlandu kutsutsa wosachimwa. Munthu wakuchita izi sadzagwedezeka kunthawi zonse. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Ndalama zake sakongoletsa mofuna phindu lalikulu, ndipo salandira chokometsera mlandu kutsutsa wosachimwa. Munthu wakuchita izi sadzagwedezeka kunthawi zonse. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Ndi amene sakongoza ndalama zake kuti alandire chiwongoladzanja, amene salandira chiphuphu kuti azunze munthu wosalakwa. Munthu wochita zimenezi, palibe chilichonse chimene chidzamgwedeze. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 amene amakongoletsa ndalama zake popanda chiwongoladzanja ndipo salandira chiphuphu pofuna kutsutsa anthu osalakwa. Iye amene amachita zinthu zimenezi sadzagwedezeka konse. Onani mutuwo |
Ndikalipo ine; chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng'ombe ya yani? Kapena ndinalanda bulu wa yani? Ndinanyenga yani? Ndinasutsa yani? Ndinalandira m'manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga? Ngati ndinatero ndidzachibwezera kwa inu.