Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 52:8 - Buku Lopatulika

8 Koma ine ndine ngati mtengo wauwisi wa azitona m'nyumba ya Mulungu. Ndikhulupirira chifundo cha Mulungu kunthawi za nthawi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Koma ine ndine ngati mtengo wauwisi wa azitona m'nyumba ya Mulungu. Ndikhulupirira chifundo cha Mulungu kunthawi za nthawi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Koma ine ndili ngati mtengo wauŵisi wa olivi m'Nyumba ya Mulungu. Ndimaika mtima nthaŵi zonse pa chikondi chosasinthika cha Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Koma ine ndili ngati mtengo wa olivi wobiriwira bwino mʼnyumba ya Mulungu; ndimadalira chikondi chosatha cha Mulungu kwa nthawi za nthawi.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 52:8
10 Mawu Ofanana  

Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.


Mkazi wako adzanga mpesa wopatsa m'mbali za nyumba yako; ana ako adzanga timitengo ta azitona pozinga podyera pako.


Koma ine ndakhulupirira pa chifundo chanu; mtima wanga udzakondwera nacho chipulumutso chanu.


Yehova akondwera nao akumuopa Iye, iwo akuyembekeza chifundo chake.


Taonani, diso la Yehova lili pa iwo akumuopa Iye, pa iwo akuyembekeza chifundo chake.


Ndipo anthu adzati, Indedi, pali mphotho kwa wolungama. Indedi, pali Mulungu wakuweruza padziko lapansi.


Yehova anatcha dzina lako, Mtengo wa azitona wauwisi, wokoma wa zipatso zabwino; ndi mau a phokoso lalikulu wayatsa moto pamenepo, ndipo nthambi zake zathyoka.


Pakuti ngati iwe unasadzidwa kumtengo wa azitona wa mtundu wakuthengo, ndipo unalumikizidwa ndi mtengo wa azitona wabwino, mokaniza makhalidwe ako; koposa kotani nanga iwo, ndiwo nthambi za mtundu wake, adzalumikizidwa ndi mtengo wao womwewo wa azitona?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa