Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 52:9 - Buku Lopatulika

9 Ndidzakuyamikani kosatha, popeza Inu munachichita ichi, ndipo ndidzayembekeza dzina lanu, pakuti ichi nchokoma, pamaso pa okondedwa anu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndidzakuyamikani kosatha, popeza Inu munachichita ichi, ndipo ndidzayembekeza dzina lanu, pakuti ichi nchokoma, pamaso pa okondedwa anu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ndidzakuthokozani Inu Mulungu mpaka muyaya, chifukwa cha zimene mwachita. Ndidzatamanda dzina lanu pamaso pa anthu okukondani, pakuti ndinu abwino.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ine ndidzakutamandani kwamuyaya chifukwa cha zimene mwachita; chifukwa cha zimene mwachita; mʼdzina lanu ndidzayembekezera pakuti dzina lanulo ndi labwino. Ndidzakutamandani pamaso pa oyera mtima anu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 52:9
17 Mawu Ofanana  

Nawawerengera Hamani kulemera kwake kwakukulu, ndi ana ake ochuluka, ndi zonse mfumu idamkuza nazo, ndi umo adamkweza koposa akalonga ndi anyamata a mfumu.


Ndidzalemekeza Yehova m'moyo mwanga; ndidzaimbira zomlemekeza Mulungu wanga pokhala ndi moyo ine.


Yembekeza Yehova, limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.


kuti ulemu wanga uimbire Inu, wosakhala chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse.


Kuyembekeza ndayembekeza Yehova; ndipo anandilola, namva kufuula kwanga.


Ine mwini ndidzapereka nsembe yaufulu kwa Inu, ndidzayamika dzina lanu, Yehova, pakuti nlokoma.


Moyo wanga ukhalira chete Mulungu yekha; chipulumutso changa chifuma kwa Iye.


Moyo wanga, ukhalire chete Mulungu yekha; pakuti chiyembekezo changa chifuma kwa Iye.


Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu. Ndimuyesa Ambuye Yehova pothawirapo ine, kuti ndifotokozere ntchito zanu zonse.


Dzina la Yehova ndilo nsanja yolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa