Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 53:1 - Buku Lopatulika

1 Chitsiru chimati mumtima mwake, Kulibe Mulungu. Achita zovunda, achita chosalungama chonyansa; kulibe wakuchita bwino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Chitsiru chimati mumtima mwake, Kulibe Mulungu. Achita zovunda, achita chosalungama chonyansa; kulibe wakuchita bwino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Mumtima mwake munthu wopusa amati, “Kulibe Mulungu.” Anthu otereŵa ndi oipa, amachita zonyansa, palibe ndi mmodzi yemwe wochita zabwino.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Chitsiru chimati mu mtima mwake, “Kulibe Mulungu.” Iwo ndi oyipa ndipo njira zawo ndi zonyansa; palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 53:1
24 Mawu Ofanana  

Ndipo Yerobowamu ananena m'mtima mwake, Ufumuwu udzabwereranso kunyumba ya Davide.


panalinso anyamata ochitirana dama m'dzikomo; iwo amachita monga mwa zonyansitsa za amitundu, amene Yehova anapirikitsa pamaso pa ana a Israele.


Adzatulutsa choyera m'chinthu chodetsa ndani? Nnena mmodzi yense.


Koposa kotani nanga munthu wonyansa ndi wodetsa, wakumwa chosalungama ngati madzi.


Anena m'mtima mwake, Mulungu waiwala; wabisa nkhope yake; sapenya nthawi zonse.


Woipa anyozeranji Mulungu, anena m'mtima mwake, Simudzafunsira?


Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yake, akuti, Sadzafunsira. Malingaliro ake onse akuti, Palibe Mulungu.


Ati mumtima mwake, Sindidzagwedezeka ine; ku mibadwomibadwo osagwa m'tsoka ine.


Yehova, Mulungu wa chipulumutso changa, ndinafuula pamaso panu usana ndi usiku.


Munthu wopulukira sachidziwa; ndi munthu wopusa sachizindikira ichi;


Koma sunayende m'njira zao, kapena kuchita monga mwa zonyansa zao pang'ono pokha; unawaposa iwo m'kuvunda kwako, m'njira zako zonse.


Ngakhale Samariya sanachite theka la zochimwa zako, koma unachulukitsa zonyansa zako, kuwaposa iwowa, ndi kuika abale ako olungama ndi zonyansa zako zonse unazichita.


koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.


Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani?


chifukwa kuti, ngakhale anadziwa Mulungu, sanamchitire ulemu wakuyenera Mulungu, ndipo sanamyamike; koma anakhala opanda pake m'maganizo ao, ndipo unada mtima wao wopulukira.


Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'chidziwitso chao, anawapereka Mulungu kumtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera;


pakuti zochitidwa nao m'tseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi.


Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu; pakuti zilizonse zinyansira Yehova, zimene azida Iye, iwowa anazichitira milungu yao; pakuti angakhale ana ao aamuna ndi ana ao aakazi awatentha m'moto, nsembe ya milungu yao.


Pakuti nthawi yapitayi idakufikirani kuchita chifuniro cha amitundu, poyendayenda inu m'kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, maimwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa