Masalimo 53 - Buku LopatulikaKupusa ndi kuipa kwa anthu ( Mas. 14 ) Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Mahalati. Chilangizo cha Davide. 1 Chitsiru chimati mumtima mwake, Kulibe Mulungu. Achita zovunda, achita chosalungama chonyansa; kulibe wakuchita bwino. 2 Mulungu m'mwamba anaweramira pa ana a anthu, kuti aone ngati aliko wanzeru, wakufuna Mulungu. 3 Onse anabwerera; anavunda mtima pamodzi; palibe mmodzi wakuchita bwino, nnena mmodzi. 4 Kodi ochita zopanda pake sadziwa? Pomadya anthu anga monga akudya mkate; ndipo saitana Mulungu. 5 Pamenepo anaopa kwakukulu, popanda chifukwa cha kuopa, pakuti Mulungu anamwaza mafupa a iwo akuzinga iwe; unawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawakaniza. 6 Ha, chipulumutso cha Israele chichokere mu Ziyoni! Pakubweretsa Mulungu anthu ake a m'ndende, Yakobo adzakondwera, Israele adzasekera. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi