Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 53:5 - Buku Lopatulika

5 Pamenepo anaopa kwakukulu, popanda chifukwa cha kuopa, pakuti Mulungu anamwaza mafupa a iwo akuzinga iwe; unawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawakaniza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Pamenepo anaopa kwakukulu, popanda chifukwa cha kuopa, pakuti Mulungu anamwaza mafupa a iwo akuzinga iwe; unawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawakaniza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Tsonotu iwo adzachita mantha aakulu, mantha ake amene sadaoneke ndi kale lonse. Pakuti Mulungu adzaononga adani okuzingani. Inu mudzaŵachititsa manyazi chifukwa Mulungu waŵakana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Iwo anali pamenepo atathedwa nzeru ndi mantha aakulu pamene panalibe kanthu kochititsa mantha. Mulungu anamwazamwaza mafupa a anthu amene anakuthirani nkhondo; inuyo munawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawanyoza.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 53:5
22 Mawu Ofanana  

M'makutu mwake mumveka zoopsetsa; pali mtendere amfikira wakumuononga.


Pamenepa anaopaopatu, pakuti Mulungu ali mu mbadwo wa wolungama.


Mafupa athu amwazika pakamwa pa manda, monga ngati akumba nanyimphula nthaka yapansi.


Wokhala m'mwambayo adzaseka; Ambuye adzawanyoza.


Achite manyazi, nadodome iwo akukondwera chifukwa cha choipa chidandigwera. Avekeke ndi manyazi ndi kupunzika iwo akudzikuza pa ine.


Athe nzeru nachite manyazi iwo akufuna moyo wanga; abwezedwe m'mbuyo nasokonezeke iwo akundipangira chiwembu.


Achite manyazi nadodome iwo akulondola moyo wanga kuti auononge. Abwerere m'mbuyo, nachite manyazi iwo okondwera kundichitira choipa.


Monga anthu atauka, apepula loto; momwemo, Inu Ambuye, pakuuka mudzapeputsa chithunzithunzi chao.


Woipa athawa palibe momthamangitsa; koma olungama alimba mtima ngati mkango.


Pakuti, taona, ndakuyesa iwe wamng'ono mwa amitundu, ndi wonyozedwa mwa anthu.


Anthu adzawatcha nthale ya siliva, pakuti Yehova wakana iwo.


Wachotsa mwamphamvu dindiro lake ngati la m'munda; waononga mosonkhanira mwake; Yehova waiwalitsa anthu msonkhano ndi Sabata mu Ziyoni; wanyoza mfumu ndi wansembe mokwiya mwaukali.


Ndipo ndidzaika mitembo ya ana a Israele pamaso pa mafano anu, ndi kumwaza mafupa anu mozungulira maguwa anu a nsembe.


Ndipo nkhope yanga idzatsutsana nanu; kuti adani anu adzakukanthani, ndipo akudana ndi inu adzachita ufumu pa inu ndipo mudzathawa wopanda wakukulondolani.


Kunena za iwo akutsalira, ndidzalonga kukomoka kumtima kwao m'maiko a adani ao; ndi liu la tsamba lotengeka ndi mphepo lidzawapirikitsa; ndipo adzathawa monga amathawa lupanga; ndipo adzagwa wopanda wakuwalondola.


Ndipo kunali kunthunthumira kuzithando, kuthengoko, ndi pakati pa anthu onse; a ku kaboma ndi owawanya omwe ananthunthumira; ndi dziko linagwedezeka; chomwecho kunali kunthunthumira kwakukulu koposa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa