Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 52:7 - Buku Lopatulika

7 Tapenyani, suyu munthuyu amene sanamuyese Mulungu mphamvu yake; amene anatama kuchuluka kwa chuma chake, nadzilimbitsa m'kuipsa kwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Tapenyani, suyu munthuyu amene sanamuyese Mulungu mphamvu yake; amene anatama kuchuluka kwa chuma chake, nadzilimbitsa m'kuipsa kwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 “Muwoneni munthu amene sadafune kudalira Mulungu, koma adakhulupirira chuma chake chochuluka, nalimbikira kuchita zoipa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 “Pano tsopano pali munthu amene sanayese Mulungu linga lake, koma anakhulupirira chuma chake chambiri nalimbika kuchita zoyipa!”

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 52:7
14 Mawu Ofanana  

Koma oipa adzalikhidwa m'dziko, achiwembu adzazulidwamo.


Kulibe munthu ali ndi mphamvu yolamulira mzimu ndi yakutsekereza mzimu; ngakhale mphamvu tsiku la imfa; munkhondo umo mulibe kumasuka; udyo sudzapulumutsa akuzolowerana nao.


Atero Yehova: Wotembereredwa munthu amene akhulupirira munthu, natama mkono wanyama, nuchoka kwa Yehova mtima wake.


Pamenepo Yesu anatuluka kunja, atavala korona waminga, ndi malaya achibakuwa. Ndipo ananena nao, Taonani munthuyu!


Lamulira iwo achuma m'nthawi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo;


Pa mapazi ake anabzong'onyoka, anagwa, anagona; pa mapazi ake anabzong'onyoka, anagwa; pobzong'onyokapo, pamenepo wagwa wafa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa