Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 52:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo olungama adzachiona, nadzaopa, nadzamseka, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo olungama adzachiona, nadzaopa, nadzamseka, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Anthu ochita zachilungamo adzaona zimenezi, ndipo adzachita mantha. Adzakuseka ndi kumanena kuti,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Olungama adzaona zimenezi ndi kuchita mantha; adzamuseka nʼkumanena kuti,

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 52:6
15 Mawu Ofanana  

Olungama achiona nakondwera; ndi osalakwa awaseka pwepwete,


Thupi langa linjenjemera ndi kuopa Inu; ndipo ndichita mantha nao maweruzo anu.


Yehova, landitsani moyo wanga kumilomo ya mabodza, ndi kulilime lonyenga.


Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko. Pakudulidwa oipa udzapenya.


Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, chilemekezo cha kwa Mulungu wanga; ambiri adzachiona, nadzaopa, ndipo adzakhulupirira Yehova.


Ndipo anthu onse adzachita mantha; nadzabukitsa chochita Mulungu, nadzasamalira ntchito yake.


Ziyoni anamva nakondwera, nasekerera ana aakazi a Yuda; chifukwa cha maweruzo anu, Yehova.


Mlomo wa ntheradi ukhazikika nthawi zonse; koma lilime lonama likhala kamphindi.


awa ndiwo mau amene Yehova wanena za iye, Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni, wakunyoza iwe ndi kuseka iwe ndi chiphwete; mwana wamkazi wa Yerusalemu wapukusa mutu wake pambuyo pako.


Ndipo maso anu adzaona, nimudzati, Yehova ali wamkulu kupitirira malire a Israele.


Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.


Kondwera pa iye, m'mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndi atumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa