Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 119:172 - Buku Lopatulika

172 Lilime langa liimbire mau anu; pakuti malamulo anu onse ndiwo olungama.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

172 Lilime langa liimbire mau anu; pakuti malamulo anu onse ndiwo olungama.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

172 Ndidzaimba nyimbo zoyamikira mau anu, chifukwa malamulo anu onse ndi olungama.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

172 Lilime langa liyimbe mawu anu, popeza malamulo anu onse ndi olungama.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 119:172
15 Mawu Ofanana  

Chifukwa chake ndiyesa ngolunjika malangizo anu onse akunena zonse; koma ndidana nazo njira zonse zonyenga.


Ndinafotokozera ndi milomo yanga maweruzo onse a pakamwa panu.


Mboni zanuzo mudazilamulira zili zolungama ndi zokhulupirika ndithu.


Chilungamo chanu ndicho chilungamo chosatha; ndi chilamulo chanu ndicho choonadi.


Ndidzalankhulanso za umboni wanu pamaso pa mafumu, osachitapo manyazi.


Malamulo anu onse ngokhulupirika; andilondola nalo bodza; ndithandizeni.


Pakamwa pa wolungama palankhula zanzeru, ndi lilime lake linena chiweruzo.


Sitidzazibisira ana ao, koma kufotokozera mbadwo ukudzawo zolemekeza za Yehova, ndi mphamvu yake, ndi zodabwitsa zake zimene anazichita.


Chotero chilamulo chili choyera, ndi chilangizo chake nchoyera, ndi cholungama, ndi chabwino.


Pakuti tidziwa kuti chilamulo chili chauzimu; koma ine ndili wathupi, wogulitsidwa kapolo wa uchimo.


Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.


ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m'nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.


Mau anu akhale m'chisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa