Genesis 8:22 - Buku Lopatulika22 Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthawi yakubzala ndi yakukunkha, chisanu ndi mafundi, malimwe ndi msakasa, usana ndi usiku sizidzalekai. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201422 Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthawi yakubzala ndi yakukunkha, chisanu ndi mafundi, malimwe ndi msakasa, usana ndi usiku sizidzalekai. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa22 “Nthaŵi zonse m'mene dziko lapansi lidzakhalire, padzakhala nyengo yobzala ndi nyengo yokolola. Padzakhala nyengo yachisanu ndi nyengo yotentha, nyengo yachilimwe ndi nyengo yadzinja, ndipo usana ndi usiku zidzakhalapo kosalekeza.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero22 “Nthawi zonse mmene dziko lapansi lidzakhalire, nthawi yodzala ndi nthawi yokolola yozizira ndi yotentha, dzinja ndi chilimwe, usana ndi usiku, sizidzatha.” Onani mutuwo |