Genesis 8:21 - Buku Lopatulika21 Ndipo Yehova anamva chonunkhira chakukondweretsa; nati Yehova m'mtima mwake, Sindidzatembereranso konse nthaka chifukwa cha munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndachitiramo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201421 Ndipo Yehova anamva chonunkhira chakukondweretsa; nati Yehova m'mtima mwake, Sindidzatembereranso konse nthaka chifukwa cha munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndachitiramo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa21 Chauta atamva fungo lokomalo, adati, “Sindidzatembereranso dziko chifukwa cha zochita za anthu, chifukwa ndikudziŵa maganizo a munthu kuti ndi oipa kuyambira ali mwana. Sindidzaononganso zamoyo zonse monga ndachitiramu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero21 Yehova atamva fungo labwino anati mu mtima mwake: “Sindidzatembereranso nthaka chifukwa cha munthu, ngakhale kuti maganizo a mu mtima mwake ndi oyipa kuyambira ubwana wake. Ndipo sindidzawononganso zolengedwa zonse zamoyo monga ndachitiramu. Onani mutuwo |
Chifukwa chake mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wake. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire chopereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipirikitsa lero kuti ndisalandireko cholowa cha Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu ina.