Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -



MAVESI A MAKOLO “ABADI”

MAVESI A MAKOLO “ABADI”

Monga bambo, ndinu munthu wofunika kwambiri pa moyo wa mwana wanu. Ndinu mtsogoleri panyumba panu, wotsogolera ana anu ndi kuwaphunzitsa makhalidwe abwino ndi Mawu a Mulungu. Ndinu chitsanzo kwa anthu amene akuzungulirani. Choncho, zochita zanu n’zofunika kwambiri chifukwa ana anu amatsanzira zitsanzo zanu.

Baibulo limati: “Atate wa wolungama adzasangalala kwambiri; ndipo iye wakubala wanzeru adzakondwera naye.” (Miyambo 23:24). Mulungu wakuyikani kukhala mutu wa banja lanu kuti muzisamalira ndi kutsogolera banja lanu. Mukapempha thandizo kwa Mulungu, Iye adzakuphunzitsani mmene mungachitire zimenezi.

Monga momwe bambo amachitira chifundo ana awo, momwemonso Ambuye amachitira chifundo anthu amene amamuopa. (Masalmo 103:13).




Eksodo 20:12

Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:1-3

Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino. Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake. Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi. Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba. Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika. Chifukwa chake chilimikani, mutadzimangira m'chuuno mwanu ndi choonadi, mutavalanso chapachifuwa cha chilungamo; ndipo mutadziveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere; koposa zonse mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo. Mutengenso chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu; mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse, ndi ine ndemwe, kuti andipatse mau m'kunditsegulira m'kamwa molimbika, kuti ndizindikiritse anthu chinsinsicho cha Uthenga Wabwino, Lemekeza atate wako ndi amai ako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), chifukwa cha umene ndili mtumiki wa mu unyolo, kuti m'menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula. Koma kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndichita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tikiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye; amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichicho, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti akatonthoze mitima yanu. Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu. Akhale nacho chisomo onse akukonda Ambuye wathu Yesu Khristu m'chosaonongeka. kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikulu padziko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:20

Ana inu, mverani akubala inu m'zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:8-9

Mwananga, tamva mwambo wa atate wako, ndi kusasiya chilangizo cha amai ako; pakuti izi ndi korona wa chisomo pamutu pako, ndi mkanda pakhosi pako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:20-22

Mwananga, sunga malangizo a atate wako, usasiye malamulo a mai ako; uwamange pamtima pako osaleka; uwalunze pakhosi pako. Adzakutsogolera ulikuyenda, ndi kukudikira uli m'tulo, ndi kulankhula nawe utauka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 5:16

Lemekeza atate wako ndi amai ako, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira; kuti masiku ako achuluke, ndi kuti chikukomere, m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:3

Aliyense aope mai wake, ndi atate wake; nimusunge masabata anga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:22

Tamvera atate wako anakubala, usapeputse amai ako atakalamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:24-25

Atate wa wolungama adzasekeradi; wobala mwana wanzeru adzakondwera naye. Atate wako ndi amai ako akondwere, amai ako akukubala asekere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:17

Diso lochitira atate wake chiphwete, ndi kunyoza kumvera amake, makwangwala a kumtsinje adzalikolowola, ana a mphungu adzalidya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:4

Pakuti Mulungu anati, Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo, Wakunenera atate wake ndi amake zoipa, afe ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 21:15

Munthu wakukantha atate wake, kapena amai wake, aphedwe ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 27:16

Wotembereredwa iye wakupeputsa atate wake kapena mai wake. Ndi anthu onse anene, Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:1

Mwana wanzeru akondweretsa atate; koma mwana wopusa amvetsa amake chisoni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:6

Zidzukulu ndizo korona wa okalamba; ndipo ulemerero wa ana ndiwo atate ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:19

Lemekeza atate wako ndi amai ako, ndipo, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:20

Mwana wanzeru akondweretsa atate wake; koma munthu wopusa apeputsa amake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 7:10

Pakuti Mose anati, Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo iye wakunenera zoipa atate wake kapena amai wake, afe ndithu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 21:17

Munthu wakutemberera atate wake, kapena amai wake, aphedwe ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:4

Koma ngati wamasiye wina ali nao ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m'banja lao, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 127:3-5

Taonani, ana ndiwo cholowa cha kwa Yehova; chipatso cha m'mimba ndicho mphotho yake. Ana a ubwana wake wa munthu akunga mivi m'dzanja lake la chiphona. Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake: sadzachita manyazi iwo, pakulankhula nao adani kuchipata.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:4

Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m'maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:6

Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:51

Ndipo anatsika nao pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo: ndipo amake anasunga zinthu izi zonse mumtima mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:9

Komanso, tinali nao atate a thupi lathu akutilanga, ndipo tinawalemekeza; kodi sitidzagonjera Atate wa mizimu koposa nanga, ndi kukhala ndi moyo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:8

Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:26

Wolanda za atate, ndi wopirikitsa amai, ndiye mwana wochititsa manyazi ndi wogwetsa nkhope.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:20

Wotemberera atate wake ndi amake, nyali yake idzazima mu mdima woti bii.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:10

Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:15

Nthyole ndi chidzudzulo zipatsa nzeru; koma mwana womlekerera achititsa amake manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:1

Mwana wanzeru amamvera mwambo wa atate; koma wonyoza samvera chidzudzulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 128:1-4

Wodala yense wakuopa Yehova, wakuyenda m'njira zake. Pakuti udzadya za ntchito ya manja ako; wodala iwe, ndipo kudzakukomera. Mkazi wako adzanga mpesa wopatsa m'mbali za nyumba yako; ana ako adzanga timitengo ta azitona pozinga podyera pako. Taonani, m'mwemo adzadalitsika munthu wakuopa Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:1-2

Mwananga, usaiwale malamulo anga, mtima wako usunge malangizo anga; motero nkhokwe zako zidzangoti thee, mbiya zako zidzasefuka vinyo. Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova, ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake; pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda; monga atate mwana amene akondwera naye. Wodala ndi wopeza nzeru, ndi woona luntha; pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golide woyengeka. Mtengo wake uposa ngale; ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye. Masiku ambiri ali m'dzanja lamanja lake; chuma ndi ulemu m'dzanja lake lamanzere. Njira zake zili zokondweretsa, mayendedwe ake onse ndiwo mtendere. Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira; wakuiumirira ngwodala. Yehova anakhazika dziko ndi nzeru; naika zamwamba ndi luntha. pakuti adzakuonjezera masiku ambiri, ndi zaka za moyo ndi mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 6:6-7

Ndipo mau awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m'nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:1-4

Ananu, mverani mwambo wa atate, nimutchere makutu mukadziwe luntha; Tamvera mwananga, nulandire mau anga; ndipo zaka za moyo wako zidzachuluka. Ndakuphunzitsa m'njira ya nzeru, ndakuyendetsa m'mayendedwe olungama. Mapazi ako sadzaombana ulikuyenda; ukathamanga, sudzaphunthwa. Gwira mwambo, osauleka; uusunge; pakuti ndiwo moyo wako. Usalowe m'mayendedwe ochimwa, usayende m'njira ya oipa. Pewapo, osapitamo; patukapo, nupitirire. Pakuti akapanda kuchita zoipa, samagona; ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwachokera. Pakuti amadya chakudya cha uchimo, namwa vinyo wa chifwamba. Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee. Njira ya oipa ikunga mdima; sadziwa chimene chiwaphunthwitsa. pakuti ndikuphunzitsani zabwino; musasiye chilangizo changa. Mwananga, tamvera mau anga; tcherera makutu ku zonena zanga. Asachoke kumaso ako; uwasunge m'kati mwa mtima wako. Pakuti ali moyo kwa omwe awapeza, nalamitsa thupi lao lonse. Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo. Tasiya m'kamwa mokhota, uike patali milomo yopotoka. Maso ako ayang'ane m'tsogolo, zikope zako zipenye moongoka. Sinkhasinkha bwino mayendedwe a mapazi ako; njira zako zonse zikonzeke. Usapatuke kudzanja lamanja kapena kulamanzere; suntha phazi lako kusiya zoipa. Pakuti ndinali mwana kwa atate wanga, wokondedwa ndi mai, ndine ndekha, sanabale wina. Atate nandiphunzitsa, nati kwa ine, mtima wako uumirire mau anga; sunga malamulo anga, nukhale ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:5

Chitsiru chipeputsa mwambo wa atate wake; koma wosamalira chidzudzulo amachenjera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:13

Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 18:19

Chifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu chomwe anamnenera iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:18

Menya mwanako, chiyembekezero chilipo, osafunitsa kumuononga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:17

Langiza mwana wako, ndipo adzakupumitsa; nadzasangalatsa moyo wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 19:26-27

Pamenepo Yesu pakuona amake, ndi wophunzira amene anamkonda, alikuimirirako, ananena kwa amake, Mkazi, taonani, mwana wanu! Pamene ananena kwa wophunzirayo, Taona, amai wako. Ndipo kuyambira ora lomweli wophunzirayo ananka naye kwao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:1

Wokonda mwambo akonda kudziwa; koma wakuda chidzudzulo apulukira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:2

ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:26

Wakuopa Yehova akhulupirira kolimba; ndipo ana ake adzakhala ndi pothawirapo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:5-6

Usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine; ndi kuwachitira chifundo anthu zikwizikwi a iwo amene akondana ndi Ine, nasunga malamulo anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:13-14

Usamane mwana chilango; pakuti ukammenya ndi nthyole safa ai. Udzammenya ndi nthyole, nudzapulumutsa moyo wake kunsi kwa manda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:10-11

Tamvera mwananga, nulandire mau anga; ndipo zaka za moyo wako zidzachuluka. Ndakuphunzitsa m'njira ya nzeru, ndakuyendetsa m'mayendedwe olungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:21

Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 144:12

Kuti ana athu aamuna akhale ngati mmera udakula usanakhwime; ana athu aakazi ngati nsanamira za kungodya, zosema zikometsere nyumba ya mfumu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:7

Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziwa; opusa anyoza nzeru ndi mwambo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 2:1-5

Mwananga, ukalandira mau anga, ndi kusunga malamulo anga; Pakuti nzeru idzalowa m'mtima mwako, moyo wako udzakondwera ndi kudziwa, kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakutchinjiriza; kukupulumutsa kunjira yoipa, kwa anthu onena zokhota; akusiya mayendedwe olungama, akayende m'njira za mdima; omwe asangalala pochita zoipa, nakondwera ndi zokhota zoipa; amene apotoza njira zao, nakhotetsa mayendedwe ao. Nzeru idzakupulumutsa kwa mkazi wachiwerewere, kwa mkazi wachilendo wosyasyalika ndi mau ake; wosiya bwenzi la ubwana wake, naiwala chipangano cha Mulungu wake. Nyumba yake itsikira kuimfa, ndi mayendedwe ake kwa akufa; onse akunka kwa iye sabweranso, safika kunjira za moyo; kutcherera makutu ako kunzeru, kulozetsa mtima wako kukuzindikira; nzeru idzakuyendetsa m'njira ya anthu abwino, kuti usunge mayendedwe a olungama. Pakuti oongoka mtima adzakhala m'dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m'dziko, achiwembu adzazulidwamo. ukaitananso luntha, ndi kufuulira kuti ukazindikire; ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika; pompo udzazindikira kuopa Yehova ndi kumdziwadi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 127:1-2

Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mzinda Yehova, mlonda adikira chabe. Kuli chabe kwa inu kulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo, kudya mkate wosautsa kuupeza; kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ake ngati m'tulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 4:9

Chokhachi, dzichenjerani nokha, ndi kusunga moyo wanu mwachangu, kuti mungaiwale zinthuzi adaziona maso anu, ndi kuti zisachoke kumtima kwanu masiku onse a moyo wanu; koma muzidziwitsa ana anu ndi zidzukulu zanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:1

Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mau owawitsa aputa msunamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 127:4

Ana a ubwana wake wa munthu akunga mivi m'dzanja lake la chiphona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:24

Wolekerera mwanake osammenya amuda; koma womkonda amyambize kumlanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:3

Mwamuna wokonda nzeru akondweretsa atate wake; koma wotsagana ndi akazi adama amwaza chuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 6:2

kuti muope Yehova Mulungu wanu, kusunga malemba ake onse ndi malamulo ake, amene ndikuuzani inu ndi ana anu, ndi zidzukulu zanu, masiku onse a moyo wanu, ndi kuti masiku anu achuluke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:13

Monga munthu amene amake amtonthoza mtima, momwemo ndidzatonthoza mtima wanu; ndipo mudzatonthozedwa mtima mu Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:13

Mwana wopusa ndiye tsoka la atate wake; ndipo makangano a mkazi ndiwo kudonthadonthabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:1-2

Chifukwa chake khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa; kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani; ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse; pakuti zochitidwa nao m'tseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi. Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera; pakuti chonse chakuonetsa chili kuunika. Mwa ichi anena, Khala maso wogona iwe, nuuke kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe. Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa. Chifukwa chake musakhale opusa, koma dziwitsani chifuniro cha Ambuye nchiyani. Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu, ndi kudzilankhulira nokha ndi masalimo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu; ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:7

Wolungama woyenda mwangwiro, anake adala pambuyo pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 3:15

ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 78:4-7

Sitidzazibisira ana ao, koma kufotokozera mbadwo ukudzawo zolemekeza za Yehova, ndi mphamvu yake, ndi zodabwitsa zake zimene anazichita. Kawirikawiri nanga anapikisana ndi Iye kuchigwako, nammvetsa chisoni m'chipululu. Pakuti anabwerera m'mbuyo, nayesa Mulungu, nachepsa Woyerayo wa Israele. Sanakumbukire dzanja lake, tsikuli anawaombola kwa msautsi. Amene anaika zizindikiro zake mu Ejipito, ndi zodabwitsa zake kuchidikha cha Zowani. Nasanduliza nyanja yao mwazi, ndi mitsinje yao, kuti sangakhoze kumwa. Anawatumizira pakati pao mitambo ya ntchentche zakuwatha; ndi achule akuwaononga. Ndipo anapatsa mphuchi dzinthu dzao, ndi dzombe ntchito yao. Anapha mphesa zao ndi matalala, ndi mikuyu yao ndi chisanu. Naperekanso zoweta zao kwa matalala, ndi ng'ombe zao kwa mphezi. Anawatumizira mkwiyo wake wotentha, kuzaza, ndi kupsa mtima, ndi nsautso, ndizo gulu la amithenga ochita zoipa. Anakhazika mboni mwa Yakobo, naika chilamulo mwa Israele, ndizo analamulira atate athu, akazidziwitse ana ao; Analambulira mkwiyo wake njira; sanalekerere moyo wao usafe, koma anapereka moyo wao kumliri. Ndipo anapha ana oyamba onse a mu Ejipito, ndiwo oyamba a mphamvu yao m'mahema a Hamu. Koma anatulutsa anthu ake ngati nkhosa, nawatsogoza ngati gulu la zoweta m'chipululu. Ndipo anawatsogolera mokhulupirika, kotero kuti sanaope; koma nyanja inamiza adani ao. Ndipo anawafikitsa kumalire a malo ake oyera, kuphiri ili, dzanja lamanja lake lidaligula. Ndipo anapirikitsa amitundu pamaso pao, nawagawira cholowa chao, ndi muyeso, nakhalitsa mafuko a Israele m'mahema mwao. Koma anamuyesa napikisana ndi Mulungu Wam'mwambamwamba, osasunga mboni zake; koma anabwerera m'mbuyo, nachita zosakhulupirika monga makolo ao, anapatuka ngati uta wolenda. Ndipo anautsa mtima wake ndi malo amsanje ao, namchititsa nsanje ndi mafano osema. Pakumva ichi Mulungu, anakwiya, nanyozatu Israele; kuti mbadwo ukudzawo udziwe, ndiwo ana amene akadzabadwa; amene adzaimirira nadzafotokozera ana ao. ndipo anachokera chokhalamo cha ku Silo, chihemacho adachimanga mwa anthu; napereka mphamvu yake mu ukapolo, ndi ulemerero wake m'dzanja la msautsi. Naperekanso anthu ake kwa lupanga; nakwiya nacho cholowa chake. Moto unapsereza anyamata ao; ndi anamwali ao sanalemekezeke. Ansembe ao anagwa ndi lupanga; ndipo amasiye ao sanachite maliro. Pamenepo Ambuye anauka ngati wam'tulo; ngati chiphona chakuchita nthungululu ndi vinyo. Ndipo anapanda otsutsana naye kumbuyo; nawapereka akhale otonzeka kosatha. Tero anakana hema wa Yosefe; ndipo sanasankhe fuko la Efuremu; koma anasankha fuko la Yuda, Phiri la Ziyoni limene analikonda. Ndipo anamanga malo oyera ake ngati kaphiri, monga dziko lapansi limene analikhazikitsa kosatha. Ndi kuti chiyembekezo chao chikhale kwa Mulungu, osaiwala zochita Mulungu, koma kusunga malamulo ake ndiko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 18:20

Udziwa malamulo. Usachite chigololo, Usaphe, Usabe, Usachite umboni wonama, Lemekeza atate wako ndi amai ako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 9:27

Mulungu akuze Yafeti, akhale iye m'mahema a Semu; Kanani akhale kapolo wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 11:19

Ndipo muziwaphunzitsa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala inu pansi m'nyumba mwanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pakuuka inu pomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:33

Koma wondimvera ine adzakhala osatekeseka, nadzakhala phee osaopa zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:5

Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:7

Nzeru ipambana, tatenga nzeru; m'kutenga kwako konseko utenge luntha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 6:20-25

Akakufunsani ana anu m'tsogolomo, ndi kuti, Mbonizo, ndi malemba, ndi maweruzo, zimene Yehova Mulungu wathu anakulamulirani, zitani? Pamenepo muzinena kwa ana anu, Tinali akapolo a Farao mu Ejipito; ndipo Yehova anatitulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu. Ndipo Yehova anapatsa zizindikiro ndi zozizwa zazikulu ndi zowawa mu Ejipito, pa Farao, ndi pa nyumba yake yonse, pamaso pathu; ndipo anatitulutsa komweko, kuti atilowetse, kutipatsa dzikoli analumbirira makolo athu. Ndipo Yehova anatilamulira tizichita malemba awa onse, kuopa Yehova Mulungu wathu, kuti tipindule nako masiku onse, kuti atisunge amoyo, monga lero lino. Ndipo kudzakhala kwa ife chilungamo, ngati tisamalira kuchita malamulo awa onse pamaso pa Yehova Mulungu wathu, monga anatilamulira ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:5

Wokolola m'malimwe ndi mwana wanzeru; koma wogona pakututa ndi mwana wochititsa manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:29

Wovuta banja lake adzalowa m'zomsautsa; wopusa adzatumikira wanzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:10

M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:4-5

Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:12

Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 112:1-2

Aleluya. Wodala munthu wakuopa Yehova, wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake. Woipa adzaziona, nadzapsa mtima; adzakukuta mano, nadzasungunuka; chokhumba oipa chidzatayika. Mbeu yake idzakhala yamphamvu padziko lapansi; mbadwo wa oongoka mtima udzadalitsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:31

Imvi ndiyo korona wa ulemu, idzapezedwa m'njira ya chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:18

Tiana, tisakonde ndi mau, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m'choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:17

Wachifundo achitira moyo wake zokoma; koma wankhanza avuta nyama yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:1

Mbiri yabwino ifunika kopambana chuma chambiri; kukukomera mtima anzako kuposa siliva ndi golide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 113:9

Asungitsa nyumba mkazi wosaona mwana, akhale mai wokondwera ndi ana. Aleluya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:3

musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:1

Ananu, mverani mwambo wa atate, nimutchere makutu mukadziwe luntha;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:6-7

sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi choonadi; chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:15

Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana; koma nthyole yomlangira idzauingitsira kutali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:25

Mwana wopusa achititsa atate wake chisoni, namvetsa zowawa amake wombala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:8

Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:23

Pakuti malangizo ndi nyali, malamulo ndi kuunika; ndi zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 127:5

Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake: sadzachita manyazi iwo, pakulankhula nao adani kuchipata.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:7

Kumbukirani masiku akale, zindikirani zaka za mibadwo yambiri; funsani atate wanu, adzakufotokozerani; akulu anu, adzakuuzani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:7-8

Okondedwa, tikondane wina ndi mnzake: chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kuchokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu. Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:14

Potero udzadziwa kuti nzeru ili yotero m'moyo wako; ngati waipeza padzakhala mphotho, ndipo chiyembekezo chako sichidzalephereka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:7

Perekani kwa anthu onse mangawa ao; msonkho kwa eni ake a msonkho; kulipira kwa eni ake a kulipidwa; kuopa kwa eni ake a kuwaopa; ulemu kwa eni ake a ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:6

koma yense amene adzakhumudwitsa kamodzi ka tiana iti, takukhulupirira Ine, kumuyenera iye kuti mphero yaikulu ikolowekedwe m'khosi mwake, namizidwe poya pa nyanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:17

Bwenzi limakonda nthawi zonse; ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:22

Wabwino asiyira zidzukulu zake cholowa chabwino; koma wochimwa angosungira wolungama chuma chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 28:1

Ndipo Isaki anamuitana Yakobo, namdalitsa iye, namuuza iye, nati kwa iye, Usatenge mkazi wa ana aakazi a Kanani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 13:11

Chotsalira, abale, kondwerani. Muchitidwe angwiro; mutonthozedwe; khalani a mtima umodzi, khalani mumtendere; ndipo Mulungu wa chikondi ndi mtendere akhale pamodzi ndi inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:15-16

Mwananga, mtima wako ukakhala wanzeru, mtima wanga wa inedi udzakondwa. Imso zanga zidzasangalala, polankhula milomo yako zoongoka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:2

Yense wa ife akondweretse mnzake, kumchitira zabwino, zakumlimbikitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:8

Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:4-6

Pakuti Mulungu anati, Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo, Wakunenera atate wake ndi amake zoipa, afe ndithu. Koma inu munena, Aliyense amene anena kwa atate wake kapena kwa amake, Icho ukanathandizidwa nacho, nchoperekedwa kwa Mulungu; iyeyo sadzalemekeza atate wake. Ndipo inu mupeputsa mau a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:10

Mwananga, akakukopa ochimwa usalole.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 133:1

Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:12-13

Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:8

Musakhale ndi mangawa kwa munthu aliyense, koma kukondana ndiko; pakuti iye amene akondana ndi mnzake wakwanitsa lamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:28-29

Anake adzanyamuka, nadzamutcha wodala; mwamuna wake namtama, nati, Ana aakazi ambiri anachita mwangwiro, koma iwe uposa onsewo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 21:7

Ndipo anati, Akadatero ndani kwa Abrahamu kuti Sara adzayamwitsa ana? Pakuti ndambalira iye mwana wamwamuna mu ukalamba wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:7

Wosunga chilamulo ndiye mwana wozindikira; koma mnzao wa adyera achititsa atate wake manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:11

Pali mbadwo wotemberera atate ao, osadalitsa amai ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:3

Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 111:10

Kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru; onse akuchita chotero ali nacho chidziwitso chokoma; chilemekezo chake chikhalitsa kosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:9

Odala ali akuchita mtendere; chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:25

Nkhawa iweramitsa mtima wa munthu; koma mau abwino aukondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:16

Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nao odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:13-14

Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo. Pakuti mau amodzi akwaniritsa chilamulo chonse ndiwo; Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:2-3

Lemekeza atate wako ndi amai ako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), chifukwa cha umene ndili mtumiki wa mu unyolo, kuti m'menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula. Koma kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndichita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tikiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye; amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichicho, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti akatonthoze mitima yanu. Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu. Akhale nacho chisomo onse akukonda Ambuye wathu Yesu Khristu m'chosaonongeka. kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikulu padziko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:3-4

Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:7

Chifukwa chake mulandirane wina ndi mnzake, monganso Khristu anakulandirani inu, kukachitira Mulungu ulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:32

Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 86:5

Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira, ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 27:34-35

Pamene Esau anamva mau a atate wake Isaki, analira ndi kulira kwakukulu ndi kowawa kopambana, nati kwa atate wake, Mundidalitse ine, inenso atate wanga. Ndipo iye anati, Mphwako anadza monyenga, nalanda mdalitso wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:3-4

Nzeru imangitsa nyumba; luntha liikhazikitsa. Ndinapita pamunda wa waulesi, polima mphesa munthu wosowa nzeru. Taonani, ponsepo panamera minga, ndi kuwirirapo khwisa; tchinga lake lamiyala ndi kupasuka. Pamenepo ndinayang'ana ndi kuganizira, ndinaona ndi kulandira mwambo. Tulo tapang'ono, kungoodzera pang'ono, kungomanga manja pang'ono m'kugona, ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala; ndi kusauka kwako ngati munthu wachikopa. Kudziwa kudzaza zipinda zake ndi chuma chonse chofunika cha mtengo wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:4

Mbadwo wina udzalemekezera ntchito zanu mbadwo unzake, ndipo udzalalikira zamphamvu zanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:25-26

Avala mphamvu ndi ulemu; nangoseka nthawi ya m'tsogolo. Atsegula pakamwa pake ndi nzeru, ndipo chilangizo cha chifundo chili pa lilime lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:13

kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 22:37-39

Ndipo Yesu anati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Ili ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba. Ndipo lachiwiri lolingana nalo ndili, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:11

Idzani ananu ndimvereni ine, ndidzakulangizani zakumuopa Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:40

Ndipo mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi chisomo cha Mulungu chinali pa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 18:19-20

Tamvera mau anga tsopano, ndikupangire nzeru, ndi Mulungu akhale nawe; ukhale m'malo mwa anthu kwa Mulungu, nupite nayo milandu kwa Mulungu; Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anabwera naye Zipora mkazi wa Mose (atamtuma kwao), ndi ana ake awiri; nuwamasulire malemba, ndi malamulo, ndi kuwadziwitsa njira imene ayenera kuyendamo, ndi ntchito imene ayenera kuchita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:15

Ndipo ngati mbale wako akuchimwira iwe, pita, numlangize pa nokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 8:32-33

Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine, ngodala akusunga njira zanga. Imvani mwambo, mukhale anzeru osaukana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:19-21

Tamvera tsopano, mwananga, utenge nzeru, ulunjikitse mtima wako m'njiramo. nuike mpeni pakhosi pako, ngati uli wadyera. Usakhale mwa akumwaimwa vinyo, ndi ankhuli osusuka. Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka; ndipo kusinza kudzaveka munthu nsanza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 48:9

Ndipo Yosefe anati kwa atate wake, Amenewa ndi ana anga, amene Mulungu wandipatsa ine pano. Ndipo iye anati, Udze naotu kwa ine, ndipo ndidzawadalitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 71:17-18

Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga; ndipo kufikira lero ndilalikira zodabwitsa zanu. Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m'mbuyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 38:19

Wamoyo, wamoyo, iye adzakuyamikani inu, monga ine lero; Atate adzadziwitsa ana ake zoona zanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:13

Ndipo tsopano zitsala zitatu izi: chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:19

Tikonda ife, chifukwa anayamba Iye kutikonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:31-32

Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse. Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:12-13

Munthuyo wakuopa Yehova ndani? Adzamlangiza iye njira adzasankheyo. Moyo wake udzakhala mokoma; ndi mbumba zake zidzalandira dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:50

Ndipo chifundo chake chifikira anthu a mibadwomibadwo pa iwo amene amuopa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:1-2

Chikondi cha pa abale chikhalebe. Tili nalo guwa la nsembe, limene iwo akutumikira chihema alibe ulamuliro wa kudyako. Pakuti matupi a nyama zija, mwazi wa izo umatengedwa, ndi mkulu wa ansembe kulowa m'malo opatulidwa, chifukwa cha zoipa, amatenthedwa kunja kwa tsasa. Mwa ichi Yesunso, kuti akayeretse anthuwo mwa mwazi wa Iye yekha, adamva chowawa kunja kwa chipata. Chifukwa chake titulukire kwa Iye kunja kwa tsasa osenza tonzo lake. Pakuti pano tilibe mzinda wokhalitsa, komatu tifunafuna ulinkudzawo. Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake. Koma musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo. Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu. Mutipempherere ife; pakuti takopeka mtima kuti tili nacho chikumbumtima chokoma m'zonse, pofuna kukhala nao makhalidwe abwino. Ndipo ndikudandaulirani koposa kuchita ichi, kuti kubwera kwanga kwa inu kufulumidwe. Musaiwale kuchereza alendo; pakuti mwa ichi ena anachereza angelo osachidziwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:14

Koma Yesu anati, Tilekeni tiana, musatikanize kudza kwa Ine: chifukwa Ufumu wa Kumwamba uli wa totere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:17-18

Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana; kwa iwo akusunga chipangano chake, ndi kwa iwo akukumbukira malangizo ake kuwachita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:28

Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 22:30-31

Mbumba ya anthu idzamtumikira; kudzanenedwa za Ambuye ku mibadwo yakudza. Iwo adzadza nadzafotokozera chilungamo chake kwa anthu akadzabadwa, kuti Iye anachichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:16

Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Wamphamvuzonse! Atate Woyera ndikubwera kwa Inu kudzera mwa Ambuye wanga Yesu Khristu, lero ndikufuna kukuyamikani chifukwa cha makolo anga. Ndikupemphani kuti mundiphunzitse tsiku lililonse kuwalemekeza ndi kuwateteza kotero kuti ndibwezere pang'ono pa zonse zomwe achita chifukwa cha ine ndipo koposa zonse ndilandire cholowa chawo cha chikhulupiriro ndi chikondi cha mawu anu. Inu mukuti m'mawu anu: "Lemekeza atate wako ndi amayi wako, monga momwe Yehova Mulungu wako anakulangizira, kuti masiku ako atalikirane, ndi kuti zinthu zikuyendere bwino m'dziko limene Yehova Mulungu wako akuupatsa." Atate Woyera, Inu ndinu chitsanzo chabwino kwambiri cha kumvera Makolo ndipo ndithudi chifuniro chanu ndicho kuti tikhale ngati Inu, ana okhala ndi mtima womvera ndi wolangika, omwe amayamikira malamulo ndi mawu anu, akuyamika chiphunzitso chilichonse ndi malangizo a makolo. Ikani mwa iwo chilakolako chofuna kufunafuna kukhalapo kwanu ndi kusinkhasinkha mawu anu, kuti miyoyo yawo isinthe ndi kutsogozedwa ndi Inu. Ambuye, ndikukuyamikani chifukwa cha makolo anga omwe akhala anthu ofunikira kwambiri pa moyo wanga, ndikupemphani kuti mundiphunzitse kugonjera ndi kumvera chifukwa izi n'zokondweretsa ndi zolungama pamaso panu. M'dzina la Yesu, ndikukupatsani ulemerero ndi ulemu. Ameni!
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa