Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 144:12 - Buku Lopatulika

12 Kuti ana athu aamuna akhale ngati mmera udakula usanakhwime; ana athu aakazi ngati nsanamira za kungodya, zosema zikometsere nyumba ya mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Kuti ana athu amuna akhale ngati mmera udakula usanakhwime; ana athu akazi ngati nsanamira za kungodya, zosema zikometsere nyumba ya mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Ana athu aamuna pachinyamata pao akhale amphamvu ngati mitengo, ana athu aakazi akhale okongola ngati nsanamira zozokotedwa zapangodya, zoti zikometse nyumba yaufumu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Ndipo ana aamuna pa chinyamata chawo adzakhala ngati mbewu yosamalidwa bwino, ana athu aakazi adzakhala ngati zipilala zosemedwa bwino, zokongoletsera nyumba yaufumu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 144:12
12 Mawu Ofanana  

Ndipo m'dziko monse simunapezeke akazi okongola ngati ana aakazi a Yobu, nawapatsa cholowa atate wao pamodzi ndi alongo ao.


Mkazi wako adzanga mpesa wopatsa m'mbali za nyumba yako; ana ako adzanga timitengo ta azitona pozinga podyera pako.


Ana a Ziyoni a mtengo wapatali, olingana ndi golide woyengetsa, angoyesedwa ngati mbiya zadothi zozipanga manja a woumba.


Pakuti ukoma wake ndi waukulu ndithu, ndi kukongola kwake nkwakukulu ndithu! Tirigu adzakometsera anyamata, ndi vinyo watsopano anamwali.


ndipo adzakukondani, ndi kukudalitsani, ndi kukuchulukitsani; adzadalitsanso zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi anaankhosa anu, m'dziko limene analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa