Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Timoteyo 5:8 - Buku Lopatulika

8 Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Ngati wina aliyense saŵapatsa zofunika achibale ake, makamaka a m'banja mwake momwe, ameneyo wataya chikhulupiriro chake, ndipo kuipa kwake nkoposa kwa munthu wosakhulupirira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ngati wina sasamalira abale ake, makamaka a mʼbanja mwake mwenimweni, ameneyo wakana chikhulupiriro ndipo ndi woyipa kuposa wosakhulupirira.

Onani mutuwo Koperani




1 Timoteyo 5:8
19 Mawu Ofanana  

Chifukwa ndisadafike ine, iwe unali nazo zowerengeka, ndipo zachuluka zambirimbiri; Yehova wakudalitsa iwe kulikonse ndinayendako: tsopano ndidzamanga liti banja langa?


Kodi si ndiko kupatsa chakudya chako kwa anjala, ndi kuti ubwere nao kunyumba kwako aumphawi otayika? Pakuona wamaliseche kuti umveke, ndi kuti usadzibisire wekha a chibale chako?


Ndipo ngati iye samvera iwo, uuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.


Chomwecho, ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye?


Sindikadadza ndi kulankhula nao sakadakhala nalo tchimo; koma tsopano alibe chowiringula pa machimo ao.


koma mbale anena mlandu ndi mbale, ndikotu kwa osakhulupirira?


Taonani, nthawi yachitatu iyi ndapukwa ine kudza kwa inu, ndipo sindidzakusaukitsani; pakuti sindifuna zanu, koma inu; pakuti ana sayenera kuunjikira atate ndi amai, koma atate ndi amai kuunjikira ana.


Ndipo Khristu avomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupirira?


Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.


ngati tipirira, tidzachitanso ufumu ndi Iye: ngati timkana Iye, Iyeyunso adzatikana ife:


akukhala nao maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.


Avomereza kuti adziwa Mulungu, koma ndi ntchito zao amkana Iye, popeza ali onyansitsa, ndi osamvera, ndi pa ntchito zonse zabwino osatsimikizidwa.


Koma padakhalanso pakati pa anthuwo aneneri onama, monganso padzakhala aphunzitsi onama pakati pa inu, amene adzalowa nayo m'tseri mipatuko yotayikitsa, nadzakana Ambuye amene adawagula, nadzadzitengera iwo okha chitayiko chakudza msanga.


Pakuti pali anthu ena anakwawira m'tseri, ndiwo amene aja adalembedwa maina ao kale, kukalandira chitsutso ichi, anthu osapembedza, akusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa, nakaniza Mfumu wayekha, ndi Ambuye wathu, Yesu Khristu.


Ndidziwa kumene ukhalako kuja kuli mpando wachifumu wa Satana; ndipo ugwira dzina langa, osakaniza chikhulupiriro changa, angakhale m'masiku a Antipa, mboni yanga, wokhulupirika wanga, amene anaphedwa pali inu, kuja akhalako Satana.


Ndidziwa ntchito zako (taona, ndapatsa pamaso pako khomo lotseguka limene munthu sangathe kutsekapo), kuti uli nayo mphamvu pang'ono, ndipo unasunga mau anga, osakana dzina langa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa