Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 84:10 - Buku Lopatulika

10 Pakuti tsiku limodzi m'mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena. Kukhala ine wapakhomo m'nyumba ya Mulungu wanga, kundikonda ine koposa kugonera m'mahema a choipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Pakuti tsiku limodzi m'mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena. Kukhala ine wapakhomo m'nyumba ya Mulungu wanga, kundikonda ine koposa kugonera m'mahema a choipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Kukhala tsiku limodzi m'mabwalo anu nkwabwino kwambiri kupambana kukhala masiku ambiri kwina kulikonse. Nkadakonda kukhala wapakhomo wa Nyumba ya Mulungu wanga kupambana kukhala m'nyumba za anthu oipa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Nʼkwabwino kukhala mʼmabwalo anu tsiku limodzi kuposa kukhala kwina kwake kwa zaka 1,000; Ine ndingakonde kukhala mlonda wa pa khomo la Nyumba ya Mulungu wanga kuposa kukhala mʼmatenti a anthu oyipa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 84:10
13 Mawu Ofanana  

Yehova Mulungu, musabweza nkhope ya wodzozedwa wanu, mukumbukire zachifundo za Davide mtumiki wanu.


Chifukwa cha Davide mtumiki wanu musabweze nkhope ya wodzozedwa wanu.


Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa mu Kachisi wake.


Kuti ndione mphamvu yanu ndi ulemerero wanu, monga ndinakuonani m'malo oyera.


Ndipo pakupita masiku atatu, anampeza Iye mu Kachisi, analikukhala pakati pa aphunzitsi, namva iwo, nawafunsanso mafunso.


Pakuti ufulu wathu uli Kumwamba; kuchokera komwenso tilindirira Mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu;


ndipo mukapenyerera iye wovala chokometsetsa, nimukati naye, Inu mukhale apa pabwino; ndipo mukati kwa wosaukayo, Iwe, imauko, kapena, khala pansi pa mpando wa mapazi anga;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa