Nkhani ya kugonana nthawi zambiri imakhala yovuta kuyankhula, yokutidwa ndi manyazi ndi kukana. Koma monga Akhristu, tiyenera kudzifunsa kuti, “Kodi cholinga cha Mulungu ndi chotani pankhani ya kugonana?” Baibulo silikhala chete pankhaniyi, koma limatipatsa malangizo ofunikira.
Ahebri 13:4 amati, “Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.” Ukwati ndi chinthu cholemekezeka, ndipo tonsefe tiyenera kuulemekeza.
Thawa chigololo. Danyani ndi kupewa zodetsa zonse. Mulungu amadana ndi kugonana kunja kwa ukwati. Ngakhale kuti maganizo a anthu pa nkhani ya kugonana amasiyana, tiyenera kudziwa kuti Mulungu ndiye amene analenga zonse zokongola, ndipo sitiyenera kuchita manyazi ndi chilichonse chimene iye analenga.
Popeza Mulungu ndiye analenga kugonana, njira yokhayo yololeka yokhutiritsira chilakolako cha kugonana ndi mkati mwa pangano la ukwati. Ukwati ndiwo chizindikiro cha pangano limeneli, ndipo ndi zimene Mulungu amafuna. Mulungu analenga kugonana kuti chizikhala mkati mwa ukwati, osati kunja kwake.
Aukwati okhulupirika sadzadwala matenda opatsirana pogonana chifukwa chogonana kwambiri. Koma ngati mmodzi wa iwo atathyola pangano la ukwati n’kupita kukagonana ndi wina, akhoza kudwala matenda opatsirana pogonana ndi mavuto ena chifukwa cha tchimo limenelo.
koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.
Thawani dama. Tchimo lililonse munthu akalichita lili kunja kwa thupi; koma wachiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha.
Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano;
Mulungu ndipo adalenga munthu m'chifanizo chake, m'chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi. Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.
Koma za izi munalembazi; kuli bwino kwa munthu kusakhudza mkazi. Koma okwatitsidwawo ndiwalamulira, si ine ai, koma Ambuye, kuti mkazi asasiye mwamuna, komanso ngati amsiya akhale osakwatiwa, kapena ayanjanitsidwenso ndi mwamunayo, ndipo mwamuna asalekane naye mkazi. Koma kwa otsalawo ndinena ine, si Ambuye, Ngati mbale wina ali naye mkazi wosakhulupirira, ndipo iye avomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye. Ndipo mkazi amene ali naye mwamuna wosakhulupirira, navomera mtima iye kukhala naye pamodzi, asalekane naye mwamunayo. Pakuti mwamuna wosakhulupirirayo ayeretsedwa mwa mkaziyo, ndi mkazi wosakhulupirira ayeretsedwa mwa mbaleyo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala osakonzeka, koma tsopano akhala oyera. Koma ngati wosakhulupirirayo achoka, achoke. M'milandu yotere samangidwa ukapolo mbaleyo, kapena mlongoyo. Koma Mulungu watiitana ife mumtendere. Pakuti udziwa bwanji mkazi iwe, ngati udzapulumutsa mwamunayo? Kapena udziwa bwanji, mwamuna iwe, ngati udzapulumutsa mkazi? Koma, monga Ambuye wagawira kwa yense, monga Mulungu waitana yense, momwemo ayende. Ndipo kotero ndiika mu Mipingo yonse. Kodi waitanidwa wina wodulidwa? Asakhale wosadulidwa. Kodi waitanidwa wina wosadulidwa? Asadulidwe. Mdulidwe ulibe kanthu, ndi kusadulidwa kulibe kanthu, koma kusunga kwa malamulo a Mulungu. Koma chifukwa cha madama munthu yense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha.
Koma chifukwa cha madama munthu yense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha.
Musakanizana, koma ndi kuvomerezana kwanu ndiko, kwa nthawi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni, chifukwa cha kusadziletsa kwanu.
Adalitsike kasupe wako; ukondwere ndi mkazi wokula nayo. Ngati mbawala yokonda ndi chinkhoma chachisomo, maere ake akukwanire nthawi zonse; ukodwe ndi chikondi chake osaleka.
Chifukwa chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.
Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.
Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wake Heva: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova.
Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, nati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.
ndipo anamuitana Loti, nati kwa iye, Ali kuti anthu amene anadza kwa iwe madzulo ano, utitulutsire iwo kuti tiwadziwe.
Asasendere mmodzi wa inu kwa mbale wake kumvula; Ine ndine Yehova. Usamavula atate wako, ndi mai wako; ndiye mai wako, usamamvula.
Ndipo usamagonana ndi nyama iliyonse, kudetsedwa nayo; kapena mkazi asamaima panyama, kugonana nayo; chisokonezo choopsa ichi.
Munthu akachita chigololo ndi mkazi wa mwini, popeza wachita chigololo ndi mkazi wa mnansi wake, awaphe ndithu, mwamuna ndi mkazi onse awiri.
Munthu akagonana ndi mwamuna mnzake, monga amagonana ndi mkazi, achita chonyansa onse awiri; awaphe ndithu; mwazi wao ukhale pamutu pao.
Mwamuna akagona ndi nyama amuphe ndithu; muiphenso nyamayi. Mkazi akasendera kwa nyama iliyonse kugonana nayo, umuphe mkaziyo, ndi nyama yomwe; muwaphe ndithu; mwazi wao ukhale pamutu pao.
Munthu akatenga mkazi, nalowana naye, namuda, namneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kumveketsa dzina loipa, ndi kuti, Ndinamtenga mkazi uyu, koma polowana naye sindinapeze zizindikiro zakuti ndiye namwali ndithu; pamenepo atate wa namwaliyo ndi mai wake azitenga ndi kutuluka nazo zizindikiro za unamwali wake wa namwaliyo, kunka nazo kwa akulu a mzinda kuchipata; ndipo atate wa namwaliyo azinena kwa akulu, Ndinampatsa munthuyu mwana wanga wamkazi akhale mkazi wake, koma amuda; ndipo, taonani, wamneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kuti, Sindinapeze zizindikiro za unamwali wake m'mwana wako wamkazi; koma si izi zizindikiro za unamwali wa mwana wanga wamkazi. Ndipo azifunyulula chovalacho pamaso pa akulu a mzindawo. Pamenepo akulu a mzindawo azitenga munthuyu ndi kumkwapula; ndi kumlipitsa masekeli makumi okhaokha khumi a siliva, ndi kuipereka kwa atate wa namwaliyo, popeza anamveketsa dzina loipa namwali wa Israele, ndipo azikhala mkazi wake, sangathe kumchotsa masiku ake onse. Ndipo ngati mbale wanu sakhala pafupi ndi inu, kapena mukapanda kumdziwa, mubwere nayo kwanu kunyumba yanu, kuti ikhale kwanu, kufikira mbale wanu akaifuna, ndipo wambwezera iyo. Koma chikakhala choona ichi, kuti zizindikiro zakuti ndiye namwali zidamsowa namwaliyo; pamenepo azimtulutsa namwaliyo ku khomo la nyumba ya atate wake, ndipo amuna a mzinda wake azimponya miyala kuti afe; popeza anachita chopusa mu Israele, kuchita chigololo m'nyumba ya atate wake; chotero uzichotsa choipacho pakati panu.
Akampeza munthu alikugona ndi mkazi wokwatibwa ndi mwamuna; afe onse awiri, mwamuna wakugona ndi mkazi, ndi mkazi yemwe; chotero muzichotsa choipacho mwa Israele.
Pakakhala namwali, wosadziwa mwamuna, wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, ndipo anampeza m'mzinda mwamuna, nagona naye; muziwatulutsa onse awiri kunka nao ku chipata cha mzinda uwo, ndi kuwaponya miyala kuti afe; namwaliyo popeza sanafuule angakhale anali m'mzinda; ndi mwamuna popeza anachepetsa mkazi wa mnansi wake; chotero muzichotsa choipacho pakati panu.
Munthu akapeza namwali wosadziwa mwamuna, ndiye wosapalidwa ubwenzi, nakamgwira nagona naye, napezedwa iwo, pamenepo mwamuna amene anagona naye azipatsa atate wake wa namwaliyo masekeli makumi asanu a siliva, ndipo azikhala mkazi wake; popeza anamchepetsa; sangathe kumchotsa masiku ake onse.
Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wake nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wochititsa kaso pomuyang'ana. kudzali kuti ukapsa mtima wa mfumu nikati kwa iwe, Chifukwa ninji munayandikira pafupi potere pamzinda kukamenyana nao? Simunadziwe kodi kuti apalingawo adzaponya? Ndani anakantha Abimeleki mwana wa Yerubeseti? Sadamponyera kodi mphero mkazi wa palinga nafa iye ku Tebezi? Munasendera bwanji pafupi potere pa lingalo? Tsono udzanena, Mnyamata wanu Uriya Muhiti, iyenso adafa. Chomwecho mthengawo unamuka, nufika, nudziwitsa Davide zonse Yowabu anamtumiza. Ndipo mthengawo unati kwa Davide, Anthuwo anatipambana natulukira kwa ife kumundako, koma tinawagwera kufikira polowera kuchipata. Ndipo akuponyawo amene anali palinga anaponya anyamata anu; ndipo anyamata ena a mfumu anafa, ndi mnyamata wanu Uriya Muhiti, iyenso anafa. Pomwepo Davide ananena ndi mthengawo, Udzatero kwa Yowabu, Chisakuipire ichi, lupanga limaononga wina ndi mnzake. Onjeza kulimbitsa nkhondo yako pamzindapo, nuupasule; numlimbikitse motere. Ndipo pamene mkazi wa Uriya anamva kuti Uriya mwamuna wake adamwalira, iye analira maliro a mwamuna wake. Ndipo pakutuluka malirowo, Davide anatumiza munthu namtenga afike kwao kunyumba yake; ndipo iyeyo anakhala mkazi wake nambalira mwana wamwamuna. Koma Yehova anaipidwa ndi chinthu chimene Davide adachita. Ndipo Davide anatumiza munthu nafunsa za mkaziyo. Ndipo wina anati, Sindiye Bateseba, mwana wamkazi wa Eliyamu, mkazi wa Uriya Muhiti? Ndipo Davide anatumiza mithenga, namtenga iye; iye nabwera kwa iye, ndipo anagona naye, pakuti adachoka mumsambo; ndipo anabwereranso kunyumba yake.
Ndipo pamene anabwera nato pafupi kuti adye, iye anamgwira, nanena naye, Idza nugone nane, mlongo wanga. Koma iye anamyankha nati, Iai, mlongo wanga, usandichepetsa ine, pakuti chinthu chotere sichiyenera kuchitika mu Israele, usachita kupusa kumeneku. Ndipo ine, manyazi anga ndidzapita nao kuti? Ndipo iwenso udzakhala ngati wina wa zitsiru mu Israele. Chifukwa chake tsono ulankhule ndi mfumu; iyeyu sadzakukaniza ine. Koma iye sadafune kumvera mau ake, ndipo popeza anali wamphamvu ndi iye, anamkakamiza, nagona naye.
Imwa madzi a m'chitsime mwako, ndi madzi oyenda a m'kasupe mwako. Kodi magwero ako ayenera kumwazika kunja, ndi mitsinje ya madzi m'makwalala? Ikhale ya iwe wekha, si ya alendo okhala nawe ai. Adalitsike kasupe wako; ukondwere ndi mkazi wokula nayo. Ngati mbawala yokonda ndi chinkhoma chachisomo, maere ake akukwanire nthawi zonse; ukodwe ndi chikondi chake osaleka.
Zikutchinjiriza kwa mkazi woipa, ndi kulilime losyasyalika la mkazi wachiwerewere. Asakuchititse kaso m'mtima mwako, asakukole ndi zikope zake. Pakuti ukayamba ndi mkazi wadama, udzamaliza ndi nyenyeswa; ndipo mkazi wa mwini amasaka moyo wa mtengowapatali. Kodi mwamuna angatenge moto pa chifuwa chake, osatentha zovala zake? Pena kodi mwamuna angayende pa makala oyaka, osapsa mapazi ake? Chomwecho wolowa kwa mkazi wa mnzake; womkhudzayo sadzapulumuka chilango.
Amkakamiza ndi kukoka kwa mau ake, ampatutsa ndi kusyasyalika kwa milomo yake. Mnyamatayo amtsata posachedwa, monga ng'ombe ipita kukaphedwa; ndi monga unyolo umadza kulanga chitsiru; mpaka muvi ukapyoza mphafa yake; amtsata monga mbalame yothamangira msampha; osadziwa kuti adzaononga moyo wake.
madzi akuba atsekemera, ndi chakudya chobisika chikoma. Ndipo mwamunayo sadziwa kuti akufa ali konko; omwe achezetsa utsiru ali m'manda akuya.
Khalani mokondwa ndi mkazi umkonda masiku onse a moyo wako wachabe, umene Mulungu wakupatsa pansi pano masiku ako onse achabe; pakuti ilo ndi gawo lako la m'moyo ndi m'ntchito zimene uvutika nazo pansi pano.
Mnyamatayo andipsompsonetse ndi m'kamwa mwake; pakuti chikondi chako chiposa vinyo. Mafuta ako anunkhira bwino; dzina lako likunga mafuta onunkhira otsanulidwa; chifukwa chake anamwali akukonda. Undikoke; tikuthamangire; mfumu yandilowetsa m'zipinda zake: Tidzasangalala ndi kukondwera ndi iwe. Tidzatchula chikondi chako koposa vinyo: Akukonda molungama.
Dzanja lake lamanzere anditsamiritse kumutu, dzanja lake lamanja ndi kundifungatira. Ndikulumbirirani, ana aakazi inu a ku Yerusalemu, pali mphoyo, ndi mbawala zakuthengo, kuti musautse, ngakhale kugalamutsa chikondi, mpaka chikafuna mwini.
Ha, chikondi chako nchokongola, mlongo wanga, mkwatibwi! Kodi chikondi chako sichiposa vinyo? Kununkhira kwa mphoka yako ndi kuposa zonunkhiritsa za mitundumitundu! M'milomo yako, mkwatibwi, mukukha uchi, uchi ndi mkaka zili pansi pa lilime lako; kununkhira kwa zovala zako ndi kunga kununkhira kwa Lebanoni. Mlongo wanga, mkwatibwi ndiye munda wotsekedwa; ngati kasupe wotsekedwa, ndi chitsime chopikiza.
Ha, ndiwe wokongola ndi wofunika, bwenziwe, m'zokondweretsa! Msinkhu wakowu ukunga mgwalangwa, mawere ako akunga matsango amphesa. Ndinati, Ndikakwera pa mgwalangwapo, ndikagwira nthambi zake: Mawere ako ange ngati matsango amphesa, ndi kununkhira kwa mpweya wako ngati maula. M'kamwa mwako munge ngati vinyo woposa, womeza tseketseke bwenzi langa, wolankhulitsa milomo ya ogona tulo.
Koma sendererani kuno chifupi, inu ana aamuna a watsenga, mbeu yachigololo ndi yadama. Ndiye yani mudzikondweretsa momseka? Ndani mulikumyasamira kukamwa, ndi kumtulutsira lilime? Kodi inu simuli ana akulakwa, mbeu yonama? Inu amene muutsa zilakolako zanu pakati pa mathundu, patsinde pa mitengo yonse ya gudugudu, amene mupha ana m'zigwa pansi pa mapanga a matanthwe?
Wachitanso chigololo ndi Ejipito oyandikizana nawe, aakulu thupi, ndi kuchulukitsa chigololo chako kuutsa mkwiyo wanga.
Pakuti anachita chigololo, ndi m'manja mwao muli mwazi, ndipo anachita chigololo ndi mafano ao, nawapititsiranso pamoto ana ao aamuna amene anandibalira, kuti athedwe. Anandichitiranso ichi, anadetsa malo anga opatulika tsiku lomwelo, naipsa masabata anga; pakuti ataphera mafano ao, ana ao analowa tsiku lomwelo m'malo anga opatulika kuwadetsa; ndipo taona, anatero m'kati mwa nyumba yanga.
Ndipo kubadwa kwake kwa Yesu Khristu kunali kotere: Amai wake Maria anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera.
Munamva kuti kunanenedwa, Usachite chigololo; koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.
Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano;
Ndipo Iye anayankha, nati, Kodi simunawerenga kuti Iye amene adalenga anthu pachiyambi, anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, nati, Chifukwa cha ichi mwamuna adzasiya atate wake ndi amake, nadzaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi? Chotero kuti salinso awiri koma thupi limodzi. Chifukwa chake ichi chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.
Pakuti m'kati mwake mwa mitima ya anthu, mutuluka maganizo oipa, zachiwerewere, zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa: zoipa izi zonse zituluka m'kati, nkudetsa munthu.
Koma kuyambira pa chiyambi cha malengedwe anawapanga mwamuna ndi mkazi. Chifukwa chake mwamuna adzasiya atate wake ndi amai wake, ndipo adzaphatikizana ndi mkazi wake; ndipo awiriwa adzakhala thupi limodzi: kotero kuti salinso awiri, koma thupi limodzi. Chifukwa chake chimene Mulungu anachimanga pamodzi, asachilekanitse munthu.
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ana a dziko lapansi akwatira nakwatiwa: koma iwo akuyesedwa oyenera kufikira dziko lijalo, ndi kuuka kwa akufa, sakwatira kapena kukwatiwa.
Chifukwa chake Mulungu anawapereka iwo m'zilakolako za mitima yao, kuzonyansa, kuchititsana matupi ao wina ndi mnzake zamanyazi; amenewo anasandutsa choonadi cha Mulungu chabodza napembedza, natumikira cholengedwa, ndi kusiya Wolengayo, ndiye wolemekezeka nthawi yosatha. Amen. Chifukwa cha ichi Mulungu anawapereka iwo ku zilakolako za manyazi: pakuti angakhale akazi ao anasandutsa machitidwe ao a chibadwidwe akhale machitidwe osalingana ndi chibadwidwe: ndipo chimodzimodzinso amuna anasiya machitidwe a chibadwidwe cha akazi, natenthetsana ndi cholakalaka chao wina ndi mnzake, amuna okhaokha anachitirana chamanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho yakuyenera kulakwa kwao.
Chifukwa chake musamalola uchimo uchite ufumu m'thupi lanu la imfa kumvera zofuna zake: ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo.
Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m'madyerero ndi kuledzera ai, si m'chigololo ndi chonyansa ai, si mu ndeu ndi nkhwidzi ai. Koma valani inu Ambuye Yesu Khristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake.
Kwamveka ndithu kuti kuli chigololo pakati panu, ndipo chigololo chotere chonga sichimveka mwa amitundu, kuti wina ali naye mkazi wa atate wake.
Zakudya ndizo za mimba, ndi mimba ndiyo ya zakudya; koma Mulungu adzathera iyi ndi izi. Koma thupi silili la chigololo, koma la Ambuye, ndi Ambuye wa thupi;
Thawani dama. Tchimo lililonse munthu akalichita lili kunja kwa thupi; koma wachiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha. Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha. Kapena kodi simudziwa kuti oyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi liweruzidwa ndi inu, muli osayenera kodi kuweruza timilandu tochepachepa? Pakuti munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m'thupi lanu.
Mwamunayo apereke kwa mkazi mangawa ake; koma modzimodzinso mkazi kwa mwamuna. ndi iwo akulira, monga ngati salira, ndi iwo akukondwera, monga ngati sakondwera; ndi iwo akugula monga ngati alibe kanthu; ndi iwo akuchita nalo dziko lapansi, monga ngati osachititsa; pakuti maonekedwe a dziko ili apita. Koma ndifuna kuti mukhale osalabadira. Iye amene wosakwatira alabadira zinthu za Ambuye, kuti akondweretse Ambuye; koma iye wokwatira alabadira zinthu za dziko lapansi, kuti akondweretse mkazi wake. Ndi mkazi wokwatiwa ndi namwali asiyananso. Iye wosakwatiwa alabadira za Ambuye, kuti akhale woyera m'thupi ndi mumzimu; koma wokwatiwayo, alabadira za dziko lapansi, kuti akondweretse mwamunayo. Koma ichi ndinena mwa kupindula kwanu kwa inu nokha; sikuti ndikakutchereni msampha, koma kukuthandizani kuchita chimene chiyenera, ndi kutsata chitsatire Ambuye, opanda chocheukitsa. Koma wina akayesa kuti achitira mwana wake wamkazi chosamuyenera, ngati palikupitirira pa unamwali wake, ndipo kukafunika kutero, achite chimene afuna, sachimwa; akwatitsidwe. Koma iye amene aima wokhazikika mumtima mwake, wopanda chikakamizo, koma ali nao ulamuliro wa pa chifuniro cha iye yekha, natsimikiza ichi mumtima mwa iye yekha, kusunga mwana wake wamkazi, adzachita bwino. Chotero iye amene akwatitsa mwana wake wamkazi achita bwino, ndipo iye wosamkwatitsa achita koposa. Mkazi amangika pokhala mwamuna wake ali ndi moyo; koma atamwalira mwamuna ali womasuka, kuti akwatiwe naye amene afuna, koma mwa Ambuye. Mkazi alibe ulamuliro wa pa thupi lake la iye yekha, koma mwamuna ndiye; koma momwemonso mwamuna alibe ulamuliro wa pa thupi la iye yekha, koma mkazi ndiye. Koma akhala wokondwera koposa ngati akhala monga momwe ali, monga mwa kuyesa kwanga; ndipo ndinagiza kuti inenso ndili naye Mzimu wa Mulungu. Musakanizana, koma ndi kuvomerezana kwanu ndiko, kwa nthawi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni, chifukwa cha kusadziletsa kwanu.
Koma ngati sadziwa kudziletsa, akwatitsidwe; pakuti nkwabwino kukwatira koposa kutentha mtima.
Koma wina akayesa kuti achitira mwana wake wamkazi chosamuyenera, ngati palikupitirira pa unamwali wake, ndipo kukafunika kutero, achite chimene afuna, sachimwa; akwatitsidwe. Koma iye amene aima wokhazikika mumtima mwake, wopanda chikakamizo, koma ali nao ulamuliro wa pa chifuniro cha iye yekha, natsimikiza ichi mumtima mwa iye yekha, kusunga mwana wake wamkazi, adzachita bwino. Chotero iye amene akwatitsa mwana wake wamkazi achita bwino, ndipo iye wosamkwatitsa achita koposa.
Musakhale omangidwa m'goli ndi osakhulupirira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima? Ndipo Khristu avomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupirira?
Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, Taonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mulola akuduleni, Khristu simudzapindula naye kanthu. kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.
amenewo popeza sazindikiranso kanthu konse, anadzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite chidetso chonse mu umbombo.
Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima;
Chifukwa cha ichi munthu azisiya atate ndi amai, nadzaphatikizana ndi mkazi wake; ndipo iwo awiri adzakhala thupi limodzi. Chinsinsi ichi nchachikulu; koma ndinena ine za Khristu ndi Mpingo. Komanso inu, yense pa yekha, yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo mkaziyo akumbukire kuti aziopa mwamuna.
Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.
Pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu, chiyeretso chanu, kuti mudzipatule kudama; yense wa inu adziwe kukhala nacho chotengera chake m'chiyeretso ndi ulemu, kosati m'chisiriro cha chilakolako chonyansa, monganso amitundu osadziwa Mulungu;
Koma thawa zilakolako za unyamata, nutsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.
kuti akalangize akazi aang'ono akonde amuna ao, akonde ana ao, akhale odziletsa, odekha, ochita m'nyumba mwao, okoma, akumvera amuna a iwo okha, kuti mau a Mulungu angachitidwe mwano.
koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, ndikumnyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.
Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo;
Momwemonso amuna inu, khalani nao monga mwa chidziwitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu, monganso wolowa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.
Pakuti nthawi yapitayi idakufikirani kuchita chifuniro cha amitundu, poyendayenda inu m'kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, maimwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka;
Ndipo ambiri adzatsata zonyansa zao; chifukwa cha iwo njira ya choonadi idzanenedwa zamwano.
koma makamaka iwo akutsata za thupi, m'chilakolako cha zodetsa, napeputsa chilamuliro; osaopa kanthu, otsata chifuniro cha iwo eni, santhunthumira kuchitira mwano akulu aulemerero;
okhala nao maso odzala ndi chigololo, osakhoza kuleka uchimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero;
Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi.
Monga Sodomu ndi Gomora, ndi mizinda yakuizungulira, potsatana nayoyo, idadzipereka kudama, ndi kutsata zilakolako zachilendo, iikidwa chitsanzo, pakuchitidwa chilango cha moto wosatha.
Komatu ndili nazo zinthu pang'ono zotsutsana ndi iwe, popeza uli nao komweko akugwira chiphunzitso cha Balamu, amene anaphunzitsa Balaki aponye chokhumudwitsa pamaso pa ana a Israele, kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano, nachite chigololo.
Komatu ndili nako kotsutsana ndi iwe, kuti ulola mkazi Yezebele, wodzitcha yekha mneneri; ndipo aphunzitsa, nasocheretsa akapolo anga, kuti achite chigololo ndi kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano. Ndipo ndampatsa iye nthawi kuti alape; koma safuna kulapa kusiyana nacho chigololo chake. Taona, ndimponya iye pakama, ndi iwo akuchita chigololo naye kuwalonga m'chisautso chachikulu, ngati salapa iwo ndi kuleka ntchito zake.
ndipo sanalape mbanda zao, kapena nyanga zao, kapena chigololo chao, kapena umbala wao.
Iwo ndiwo amene sadetsedwa pamodzi ndi akazi; pakuti ali anamwali. Iwo ndiwo amene atsata Mwanawankhosa kulikonse amukako. Iwowa anagulidwa mwa anthu, zipatso zoyamba kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.
Ndipo anadza mmodzi mwa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, nalankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa chitsutso cha mkazi wachigololo wamkulu, wakukhala pamadzi ambiri, ndipo ali mafumu asanu ndi awiri asanu adagwa, imodzi iliko, yinayo siinadze; ndipo pamene ifika iyenera iyo kukhala kanthawi. Ndipo chilombo chinalicho, ndi kulibe, icho chomwe ndicho chachisanu ndi chitatu, ndipo chili mwa zisanu ndi ziwirizo, ndipo chinamuka kuchitayiko. Ndipo nyanga khumi udaziona ndiwo mafumu khumi, amene sanalandire ufumu; koma alandira ulamuliro ngati mafumu, ora limodzi, pamodzi ndi chilombo. Iwo ali nao mtima umodzi, ndipo apereka mphamvu ndi ulamuliro wao kwa chilombo. Iwo adzachita nkhondo pa Mwanawankhosa, ndipo Mwanawankhosa adzawagonjetsa, chifukwa ali Mbuye wa ambuye, ndi Mfumu ya mafumu; ndipo adzawalakanso iwo akukhala naye, oitanidwa, ndi osankhika ndi okhulupirika. Ndipo anena ndi ine, Madziwo udawaona uko akhalako mkazi wachigololoyo ndiwo anthu, ndi makamu, ndi mitundu, ndi manenedwe. Ndipo nyanga khumi udaziona, ndi chilombo, izi zidzadana ndi mkazi wachigololoyo, ndipo zidzamkhalitsa wabwinja wausiwa, ndi kudya nyama yake, ndipo zidzampsereza ndi moto. Pakuti Mulungu anapatsa kumtima kwao kuchita za m'mtima mwake, ndi kuchita cha mtima umodzi ndi kupatsa ufumu wao kwa chilombo, kufikira akwaniridwa mau a Mulungu. Ndipo mkaziyo unamuona, ndiye mzinda waukulu, wakuchita ufumu pa mafumu a dziko. amene mafumu a dziko anachita chigololo naye, ndipo iwo akukhala padziko analedzera ndi vinyo wa chigololo chake.
ndipo pamphumi pake padalembedwa dzina, CHINSINSI, BABILONI WAUKULU, AMAI WA ACHIGOLOLO NDI WA ZONYANSITSA ZA DZIKO.
Chifukwa ndi vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake mitundu yonse idagwa; ndipo mafumu a dziko anachita naye chigololo; ndipo ochita malonda a dziko analemera ndi mphamvu ya kudyerera kwake.
Ndipo mafumu a dziko ochita chigololo nadyerera naye, adzalira nadzaulira maliro pamene aona utsi wa kutentha kwake, poima patali,
Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.
Kunja kuli agalu ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita.
Mkazi wangwiro ndani angampeze? Pakuti mtengo wake uposa ngale. Mtima wa mwamuna wake umkhulupirira, sadzasowa phindu. Mkaziyo amchitira zabwino, si zoipa, masiku onse a moyo wake.
Pakuti Inu munalenga impso zanga; munandiumba ndisanabadwe ine. Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.
Pakuti mkazi wadama ndiye dzenje lakuya; ndipo mkazi wachiwerewere ndiye mbuna yopapatiza. Pakuti abisalira ngati wachifwamba, nachulukitsa anthu a chiwembu.
Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda chilema pa kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
Koma, monga Ambuye wagawira kwa yense, monga Mulungu waitana yense, momwemo ayende. Ndipo kotero ndiika mu Mipingo yonse.
Pakuti iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu: pakuti chisamaliro cha thupi chili imfa; koma chisamaliro cha mzimu chili moyo ndi mtendere.
Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m'thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.
Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.
Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Khristu anakonda Mpingo, nadzipereka yekha m'malo mwake; kuti akampatule, atamyeretsa ndi kumsambitsa madzi ndi mau; kuti Iye akadziikire yekha Mpingo wa ulemerero, wopanda banga, kapena khwinya, kapena kanthu kotere; komatu kuti akhale woyera, ndi wopanda chilema. Koteronso amuna azikonda akazi ao a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha;