1 Petro 4:3 - Buku Lopatulika3 Pakuti nthawi yapitayi idakufikirani kuchita chifuniro cha amitundu, poyendayenda inu m'kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, maimwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Pakuti nthawi yapitayi idatifikira kuchita chifuno cha amitundu, poyendayenda ife m'kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, maimwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Paja kale mudakhala mukutaya nthaŵi yochuluka pakuchita zinthu zimene akunja amazikonda. Munkatsata zonyansa, zilakolako zoipa, kuledzera, dyera, maphokoso apamoŵa, ndi kupembedza mafano konyansa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Pakuti mwataya kale nthawi yambiri mʼmbuyomu pochita zimene anthu osapembedza amachita, moyo wokhumba zonyansa, zilakolako zoyipa kuledzera, zochitika zoyipa za pa phwando, mapokoso ndi kupembedza mafano onyansa. Onani mutuwo |