Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 9:9 - Buku Lopatulika

9 Khalani mokondwa ndi mkazi umkonda masiku onse a moyo wako wachabe, umene Mulungu wakupatsa pansi pano masiku ako onse achabe; pakuti ilo ndi gawo lako la m'moyo ndi m'ntchito zimene uvutika nazo pansi pano.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Khalani mokondwa ndi mkazi umkonda masiku onse a moyo wako wachabe, umene Mulungu wakupatsa pansi pano masiku ako onse achabe; pakuti ilo ndi gawo lako la m'moyo ndi m'ntchito zimene uvutika nazo pansi pano.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Uzikondwerera moyo pamodzi ndi mkazi amene umamkonda, pa masiku onse a moyo wako wopandapakewu umene Mulungu wakupatsa pansi pano. Ndi zokhazo zimene ungaziyembekeze pa moyo wako ndiponso pa ntchito zako zolemetsa zimene umazigwira pansi pano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Uzikondwerera moyo pamodzi ndi mkazi wako amene umamukonda, masiku onse a moyo uno wopanda phindu, amene Mulungu wakupatsa pansi pano. Pakuti mkaziyo ndiye gawo la moyo wako pa ntchito yako yolemetsa pansi pano.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 9:9
14 Mawu Ofanana  

Ndipo panali atakhala komwe masiku ambiri, Abimeleki mfumu ya Afilisti, anayang'ana kunja kwa zenera, napenya, taona, Isaki analinkuseka ndi Rebeka mkazi wake.


Munthu akunga mpweya; masiku ake akunga mthunzi wopitirira.


Onani, munaika masiku anga akhale monga kuyesa dzanja; ndipo zaka zanga zili ngati chabe pamaso panu, Indedi munthu aliyense angakhale wokhazikika, ali chabe konse.


Wopeza mkazi apeza chinthu chabwino; Yehova amkomera mtima.


Nyumba ndi chuma ndizo cholowa cha atate; koma mkazi wanzeru achokera kwa Yehova.


Ndipo chilichonse maso anga anachifuna sindinawamane; sindinakanize mtima wanga chimwemwe chilichonse pakuti mtima wanga unakondwera ndi ntchito zanga zonse; gawo langa la m'ntchito zanga zonse ndi limeneli.


Kodi si chabwino kuti munthu adye namwe, naonetse moyo wake zabwino m'ntchito yake? Ichinso ndinachizindikira kuti chichokera kudzanja la Mulungu.


Ndiponso kuti munthu yense adye namwe naone zabwino m'ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.


M'mwemo ndinazindikira kuti kulibe kanthu kabwino kopambana aka, kuti munthu akondwere ndi ntchito zake; pakuti gawo lake ndi limeneli; pakuti ndani adzamfikitsa kuona chomwe chidzachitidwa atafa iyeyo?


Taonani, chomwe ine ndapenyera kukoma ndi kuyenera munthu ndiko kudya, ndi kumwa, ndi kukondwera ndi ntchito zake zonse asauka nazo kunja kuno, masiku onse a moyo wake umene Mulungu ampatsa; pokhala gawo lake limeneli.


Pakuti ndani adziwa chomwe chili chabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wake wachabe umene autsiriza ngati mthunzi? Pakuti ndani adzauza munthu chimene chidzaoneka m'tsogolo mwake kunja kuno?


Ndaona zonsezi masiku anga achabe; pali wolungama angofa m'chilungamo chake, ndipo pali woipa angokhalabe ndi moyo m'kuipa kwake.


Ndipo sanatero kodi wina womtsalira mzimu? Ndipo winayo anatero bwanji? Anatero pofuna mbeu ya Mulungu. Koma sungani mzimu wanu; ndipo asamchitire monyenga mkazi wa ubwana wake ndi mmodzi yense.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa