Yuda 1:7 - Buku Lopatulika7 Monga Sodomu ndi Gomora, ndi mizinda yakuizungulira, potsatana nayoyo, idadzipereka kudama, ndi kutsata zilakolako zachilendo, iikidwa chitsanzo, pakuchitidwa chilango cha moto wosatha. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Monga Sodomu ndi Gomora, ndi midzi yakuizungulira, potsatana nayoyo, idadzipereka kudama, ndi kutsata zilakolako zachilendo, iikidwa chitsanzo, pakuchitidwa chilango cha moto wosatha. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Mukumbukirenso mizinda ya Sodomu ndi Gomora ija, ndi mizinda yoyandikana nayo. Anthu ake m'menemonso ankangochita dama, namachitanso zonyansa zotsutsana ndi umunthu. Mulungu adaaŵaika ngati chitsanzo pakuŵalanga ndi moto wosatha. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Musayiwale mizinda ya Sodomu ndi Gomora ija, ndi mizinda yoyandikana nayo. Anthu mʼmenemo anadziperekanso kuchita zadama ndi kuchita zonyansa zachilendo. Mizinda imeneyi yakhala ngati chitsanzo cha amene adzalangidwa ndi moto wosatha. Onani mutuwo |