Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yuda 1:8 - Buku Lopatulika

8 Momwemonso iwo m'kulota kwao adetsa matupi ao, napeputsa ufumu, nachitira mwano maulemerero.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Momwemonso iwo m'kulota kwao adetsa matupi ao, napeputsa ufumu, nachitira mwano maulemerero.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Komabe anthu ameneŵa akuchita chimodzimodzi. Potsata maloto ao, amaipitsa matupi ao, amakana ulamuliro wa Mulungu, ndipo amachita chipongwe aulemerero a Kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Nʼchimodzimodzinso zimene akuchita anthu amenewa potsata maloto awo, amadetsa matupi awo, amakana ulamuliro wa Mulungu ndiponso amachitira chipongwe angelo akumwamba.

Onani mutuwo Koperani




Yuda 1:8
23 Mawu Ofanana  

chifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.


Usapeputsa oweruza, kapena kutemberera mkulu wa anthu a mtundu wako.


Pali mbadwo wotemberera atate ao, osadalitsa amai ao.


Diso lochitira atate wake chiphwete, ndi kunyoza kumvera amake, makwangwala a kumtsinje adzalikolowola, ana a mphungu adzalidya.


Usatemberere mfumu ngakhale poganizira; usatemberere wolemera m'chipinda chogona iwemo; pakuti mbalame ya mlengalenga idzanyamula mauwo, ndipo chouluka ndi mapiko chidzamveketsa zonenazo.


Ndipo anasonkhana motsutsana pa Mose ndi Aroni, nanena nao, Mukula mphamvu inu, pakuti khamu lonse nlopatulika, onsewa, ndipo Yehova ali pakati pao; mudzikuza bwanji pa msonkhano wa Yehova?


ndipo pofika, uipeza yosesa ndi yokonzeka.


Ndipo pamene paliponse adzamuka nanu kumlandu wa m'sunagoge ndi kwa akulu, ndi aulamuliro, musade nkhawa ndi kuti mukadzikanira bwanji, ndipo ndi mau otani, kapena mukanena chiyani;


Koma mfulu za pamudzi pake zinamuda, nkutuma akazembe amtsate m'mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyo akhale mfumu yathu.


Ndipo Paulo anati, Sindinadziwe, abale, kuti ndiye mkulu wa ansembe; pakuti kwalembedwa, Usamnenera choipa mkulu wa anthu ako.


Koma iye wakumchitira mnzake choipa anamkankha, nati, Wakuika iwe ndani mkulu ndi wotiweruzira?


amene makolo athu sanafune kumvera iye, koma anamkankha achoke, nabwerera m'mbuyo mumtima mwao ku Ejipito,


Ngati wina aononga Kachisi wa Mulungu, ameneyo Mulungu adzamuononga; pakuti Kachisi wa Mulungu ali wopatulika, ameneyo ndi inu.


Chifukwa chake iye wotaya ichi, sataya munthu, komatu Mulungu, wakupatsa Mzimu wake Woyera kwa inu.


achigololo, akuchita zoipa ndi amuna, akuba anthu, amabodza, olumbira zonama, ndipo ngati kuli kena kakutsutsana nacho chiphunzitso cholamitsa;


Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.


Chitirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Opani Mulungu, Chitirani mfumu ulemu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa