Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yuda 1:9 - Buku Lopatulika

9 Koma Mikaele mkulu wa angelo, pakuchita makani ndi mdierekezi anatsutsana za thupi la Mose, sanalimbike mtima kumtchulira chifukwa chomchitira mwano, koma anati, Ambuye akudzudzule.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Koma Mikaele mkulu wa angelo, pakuchita makani ndi mdierekezi anatsutsana za thupi la Mose, sanalimbika mtima kumtchulira chifukwa chomchitira mwano, koma anati, Ambuye akudzudzule.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Koma ngakhale Mikaele yemwe, mkulu wa angelo, pamene iye ankakangana ndi Satana ndi kutsutsana naye za mtembo wa Mose, sadafune kutchuliliza mwachipongwe kuti ndi wolakwa. Adangoti, “Ambuye akulange!”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Koma ngakhale mkulu wa angelo Mikayeli, pamene ankalimbana ndi Mdierekezi za mtembo wa Mose, sanamunene kuti wachipongwe, koma anati, “Ambuye akudzudzule iwe!”

Onani mutuwo Koperani




Yuda 1:9
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anatuluka kukomana nao, nayankha, nanena nao, Ngati mwandidzera mwamtendere kundithandiza, mtima wanga udzalumikizana nanu; koma ngati mwafika kundipereka kwa adani anga, popeza m'manja mwanga mulibe chiwawa, Mulungu wa makolo athu achione ndi kuchilanga.


Usapeputsa oweruza, kapena kutemberera mkulu wa anthu a mtundu wako.


Koma kalonga wa ufumu wa Persiya ananditsekerezera njira masiku makumi awiri ndi limodzi; ndipo taonani, Mikaele, wina wa akalonga omveka, anadza kundithandiza; ndipo ndinakhala komweko ndi mafumu a Persiya.


Koma ndidzakufotokozera cholembedwa pa lemba la choonadi; ndipo palibe wina wakudzilimbikitsa pamodzi ndi ine, kutsutsana ndi aja, koma Mikaele kalonga wanu.


Ndipo nthawi yomweyi adzauka Mikaele kalonga wamkulu wakutumikira ana a anthu a mtundu wako; ndipo padzakhala nthawi ya masautso, siinakhale yotere kuyambira mtundu wa anthu kufikira nthawi yomwe ija; ndipo nthawi yomweyo anthu ako adzapulumutsidwa, yense amene ampeza wolembedwa m'buku.


Ndipo Yehova anati kwa Satana, Yehova akudzudzula, Satana iwe; inde Yehova amene anasankha Yerusalemu akudzudzula; uyu sindiye muuni wofumulidwa kumoto?


Ndipo iwo akupitirirapo anamchitira mwano, napukusa mitu yao, nanena, Ha! Iwe wakupasula Kachisi, ndi kummanga masiku atatu,


Ndipo Iye anamuika m'chigwa m'dziko la Mowabu popenyana ndi Betepeori; koma palibe munthu wakudziwa kumanda kwake kufikira lero lino.


Pakuti Ambuye adzatsika Kumwamba mwini yekha ndi mfuu, ndi mau a mngelo wamkulu, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Khristu adzayamba kuuka;


osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ichi mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.


popeza angelo, angakhale awaposa polimbitsa mphamvu, sawaneneza kwa Ambuye mlandu wakuchita mwano.


Ndipo munali nkhondo m'mwamba. Mikaele ndi angelo ake akuchita nkhondo ndi chinjoka; chinjokanso ndi angelo ake chinachita nkhondo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa