Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 5:28 - Buku Lopatulika

28 koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti munthu aliyense woyang'ana mkazi ndi kumkhumba, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Koma Ine ndikuwuzani kuti aliyense woyangʼana mkazi momusirira wachita naye kale chigololo mu mtima mwake.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 5:28
20 Mawu Ofanana  

Pamene anamuona iye Sekemu, mwana wake wamwamuna wa Hamori Muhivi, kalonga wa dzikolo, anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa.


Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wake nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wochititsa kaso pomuyang'ana.


Ndinapangana ndi maso anga, potero ndipenyerenji namwali?


Ngati mtima wanga wakopeka ndi mkazi, ngati ndalalira pa khomo la mnzanga,


Ndinapenya malekezero ake a ungwiro wonse; koma lamulo lanu ndi lotakasuka ndithu.


Usasirire nyumba yake ya mnzako, usasirire mkazi wake wa mnzako, kapena wantchito wake wa mwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.


Asakuchititse kaso m'mtima mwako, asakukole ndi zikope zake.


Ndipo pakuwaona anawalakalaka, nawatumira mithenga kudziko la Ababiloni.


Usagona naye mkazi wa mnansi wako, kudetsedwa naye limodzi.


Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano;


koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.


koma ndinena kwa inu, Musakanize munthu woipa; koma amene adzakupanda iwe pa tsaya lako lamanja, umtembenuzire linanso.


Pakuti tidziwa kuti chilamulo chili chauzimu; koma ine ndili wathupi, wogulitsidwa kapolo wa uchimo.


Akampeza munthu alikugona ndi mkazi wokwatibwa ndi mwamuna; afe onse awiri, mwamuna wakugona ndi mkazi, ndi mkazi yemwe; chotero muzichotsa choipacho mwa Israele.


okhala nao maso odzala ndi chigololo, osakhoza kuleka uchimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero;


Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa