Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 7:5 - Buku Lopatulika

5 Musakanizana, koma ndi kuvomerezana kwanu ndiko, kwa nthawi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni, chifukwa cha kusadziletsa kwanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Musakanizana, koma ndi kuvomerezana kwanu ndiko, kwa nthawi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni, chifukwa cha kusadziletsa kwanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Musamakanane, koma pokhapokha mutavomerezana kutero pa kanthaŵi kuti mudzipereke ku mapemphero. Pambuyo pake mukhalenso pamodzi, kuwopa kuti Satana angakuyeseni chifukwa cha kulephera kudzigwira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Musamakanizane, pokhapokha mutagwirizana awiri kuti mwakanthawi mudzipereke kumapemphero. Kenaka mukhalirenso pamodzi kuopa kuti Satana angakuyeseni chifukwa cholephera kudziretsa.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 7:5
11 Mawu Ofanana  

Ndipo anati kwa anthu, Mukonzekeretu tsiku lachitatu nimusayandikiza mkazi.


Akamtengera mkazi wina, asachepetse chakudya chake, zovala zake, ndi za ukwati zakezake.


sonkhanitsani anthu, patulani msonkhano, memezani akuluakulu, sonkhanitsani ana ndi oyamwa mawere; mkwati atuluke m'chipinda mwake, ndi mkwatibwi m'mogona mwake.


nanene kwa ansembe a nyumba ya Yehova wa makamu, ndi kwa aneneri, ndi kuti, Kodi ndilire mwezi wachisanu, ndi kudzipatula, monga umo ndikachitira zaka izi zambiri?


Koma Iye anati kwa iwo, Onse sangathe kulandira chonena ichi, koma kwa iwo omwe chapatsidwa.


Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekhayekha udzamlambira.


Mkazi alibe ulamuliro wa pa thupi lake la iye yekha, koma mwamuna ndiye; koma momwemonso mwamuna alibe ulamuliro wa pa thupi la iye yekha, koma mkazi ndiye.


Mwa ichi inenso, posalekereranso, ndinatuma kukazindikira chikhulupiriro chanu, kuti kapena woyesa akadakuyesani, ndipo chivuto chathu chikadakhala chopanda pake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa