Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 37:4 - Buku Lopatulika

4 Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Udzikondweretse wekha mwa Yehova ndipo Iye adzakupatsa zokhumba za mtima wako.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 37:4
14 Mawu Ofanana  

Pakuti pamenepo udzakondwera naye Wamphamvuyonse, ndi kuweramutsa nkhope yako kwa Mulungu.


Kodi adzadzikondweretsa naye Wamphamvuyonse, ndi kuitana kwa Mulungu nthawi zonse?


Pakuti anati, Munthu sapindula kanthu nako kuvomerezana naye Mulungu.


Pomlingirira Iye pandikonde; ndidzakondwera mwa Yehova.


Adzachita chokhumba iwo akumuopa; nadzamva kufuula kwao, nadzawapulumutsa.


Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu, kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni, ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.


Chomwe woipa achiopa chidzamfikira; koma chomwe olungama achifuna chidzapatsidwa.


Ngati maula pakati pa mitengo ya m'nkhalango, momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana aamuna. Ndinakondwa pakukhala pa mthunzi wake, zipatso zake zinatsekemera m'kamwa mwanga.


pomwepo udzakondwa mwa Yehova; ndipo Ine ndidzakuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi; ndipo ndidzakudyetsa cholowa cha kholo lako Yakobo; pakuti pakamwa pa Yehova pananenapo.


Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala chipatso, ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chilichonse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu.


Ngati mukhala mwa Ine, ndi mau anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene muchifuna ndipo chidzachitika kwa inu.


amene mungakhale simunamuone mumkonda; amene mungakhale simumpenya tsopano, pokhulupirira, mukondwera naye ndi chimwemwe chosaneneka, ndi cha ulemerero:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa