Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -

Masalimo 149 - Buku Lopatulika


Okhulupirira onse alemekeze Mulungu wao

1 Aleluya, Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano, ndi chilemekezo chake mu msonkhano wa okondedwa ake.

2 Akondwere Israele mwa Iye amene anamlenga; ana a Ziyoni asekere mwa mfumu yao.

3 Alemekeze dzina lake ndi kuthira mang'ombe; amuimbire zomlemekeza ndi lingaka ndi zeze.

4 Popeza Yehova akondwera nao anthu ake; adzakometsa ofatsa ndi chipulumutso.

5 Okondedwa ake atumphe mokondwera mu ulemu: Afuule mokondwera pamakama pao.

6 Nyimbo zakukweza Mulungu zikhale pakamwa pao, ndi lupanga lakuthwa konsekonse m'dzanja lao;

7 kubwezera chilango akunja, ndi kulanga mitundu ya anthu;

8 kumanga mafumu ao ndi maunyolo, ndi omveka ao ndi majerejede achitsulo,

9 kuwachitira chiweruzo cholembedwacho. Ulemu wa okondedwa ake onse ndi uwu. Aleluya.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi
Titsatireni:



Zotsatsa