Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 149:1 - Buku Lopatulika

1 Aleluya, Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano, ndi chilemekezo chake mu msonkhano wa okondedwa ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Aleluya, Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano, ndi chilemekezo chake mu msonkhano wa okondedwa ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Tamandani Chauta! Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, imbani nyimbo yomtamanda pa msonkhano wa anthu ake oyera mtima.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Tamandani Yehova. Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, matamando ake mu msonkhano wa oyera mtima.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 149:1
15 Mawu Ofanana  

Aleluya. Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse, mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.


Ndidzachita zowinda zanga za kwa Yehova, tsopano, pamaso pa anthu ake onse.


Ndidzakuimbirani nyimbo yatsopano, Mulungu; pa chisakasa cha zingwe khumi ndidzaimbira zakukulemekezani.


Aleluya. Lemekezani Yehova kochokera kumwamba; mlemekezeni m'misanje.


Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga, pakati pa msonkhano ndidzakulemekezani.


Lemekezo langa lidzakhala la Inu mu msonkhano waukulu, zowinda zanga ndidzazichita pamaso pa iwo akumuopa Iye.


Mumuimbire Iye nyimbo yatsopano; muimbe mwaluso kumveketsa mau.


Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu; m'chikhamu cha anthu ndidzakulemekezani.


Lemekezani Mulungu m'misonkhano, ndiye Yehova, inu a gwero la Israele.


Ndipo kumwamba kudzalemekeza zodabwitsa zanu, Yehova; chikhulupiriko chanunso mu msonkhano wa oyera mtima.


Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano; muimbireni Yehova, inu, dziko lonse lapansi.


Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano; popeza anachita zodabwitsa: Dzanja lake lamanja, mkono wake woyera, zinamchitira chipulumutso.


Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, ndi matamando ake kuchokera ku malekezero a dziko lapansi; inu amene mutsikira kunyanja, ndi zonse zili m'menemo, zisumbu ndi okhala mommo.


Ndi kuti, Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga, pakati pa Mpingo ndidzakuimbirani.


Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa