Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 148:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo anakweza nyanga ya anthu ake, chilemekezo cha okondedwa ake onse; ndiwo ana a Israele, anthu a pafupi pa Iye. Aleluya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo anakweza nyanga ya anthu ake, chilemekezo cha okondedwa ake onse; ndiwo ana a Israele, anthu a pafupi pa Iye. Aleluya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Chauta wakweza anthu ake poŵapatsa mphamvu. Walemekeza anthu ake onse oyera mtima, Aisraele amene Iye amaŵakonda. Tamandani Chauta!

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Iye wakwezera nyanga anthu ake, matamando a anthu ake onse oyera mtima, Aisraeli, anthu a pamtima pake. Tamandani Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 148:14
19 Mawu Ofanana  

Anagawagawa, anapatsa aumphawi; chilungamo chake chikhalitsa kosatha; nyanga yake idzakwezeka ndi ulemu.


Ntchito zanu zonse zidzakuyamikani, Yehova; ndi okondedwa anu adzakulemekezani.


kuwachitira chiweruzo cholembedwacho. Ulemu wa okondedwa ake onse ndi uwu. Aleluya.


Ndipo ndidzatseteka nyanga zonse za oipa; koma nyanga za wolungama zidzakwezeka.


Popeza Inu ndinu ulemerero wa mphamvu yao; ndipo potivomereza Inu nyanga yathu idzakwezeka.


Pakuti chikopa chathu chifuma kwa Yehova; ndi mfumu yathu kwa Woyera wa Israele.


Koma munakweza nyanga yanga ngati ya njati; anandidzoza mafuta atsopano.


Mundichiritse ine, Yehova, ndipo ndidzachiritsidwa; mundipulumutse ine, ndipo ndidzapulumutsidwa; pakuti chilemekezo changa ndinu.


Iye anatsitsa mafumu pa mipando yao yachifumu, ndipo anakweza aumphawi.


kuunika kukhale chivumbulutso cha kwa anthu a mitundu, ndi ulemerero wa anthu anu Israele.


Koma tsopano mwa Khristu Yesu inu amene munali kutali kale, anakusendezani mukhale pafupi m'mwazi wa Khristu.


ndipo m'mene anadza, analalikira Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu akutali, ndi mtendere kwa iwo apafupi;


Pamenepo ndipo simulinso alendo ndi ogonera, komatu muli a mudzi womwewo wa oyera mtima ndi a banja la Mulungu;


Iye ndiye lemekezo lanu, Iye ndiye Mulungu wanu, amene anachita nanu zazikulu ndi zoopsa izi, mudaziona m'maso mwanu.


Pakuti mtundu waukulu wa anthu ndi uti, wakukhala ndi Mulungu pafupi pao monga amakhala Yehova Mulungu wathu, pamene paliponse timaitanira Iye?


Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;


Ndipo Hana anapemphera, nati, Mtima wanga umyuka mokondwera kwa Yehova, nyanga yanga yakwezeka mwa Yehova; pakamwa panga pakula kwa adani anga; popeza ndikondwera m'chipulumutso chanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa