Masalimo 148 - Buku LopatulikaZolengedwa zonse zilemekeze Mulungu 1 Aleluya. Lemekezani Yehova kochokera kumwamba; mlemekezeni m'misanje. 2 Mlemekezeni, angelo ake onse; mlemekezeni, makamu ake onse. 3 Mlemekezeni, dzuwa ndi mwezi; mlemekezeni, nyenyezi zonse zounikira. 4 Mlemekezeni, m'mwambamwamba, ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo. 5 Alemekeze dzina la Yehova; popeza analamulira, ndipo zinalengedwa. 6 Anazikhazikanso kunthawi za nthawi; anazipatsa chilamulo chosatumphika. 7 Lemekezani Yehova kochokera ku dziko lapansi, zinsomba inu, ndi malo ozama onse; 8 moto ndi matalala, chipale chofewa ndi nkhungu; mphepo ya namondwe, yakuchita mau ake; 9 mapiri ndi zitunda zonse; mitengo yazipatso ndi yamikungudza yonse: 10 Nyama zakuthengo ndi zoweta zonse; zokwawa, ndi mbalame zakuuluka. 11 Mafumu a padziko ndi mitundu yonse ya anthu; zinduna ndi oweruza onse a padziko. 12 Anyamata ndiponso anamwali; okalamba pamodzi ndi ana. 13 Alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka; ulemerero wake uli pamwamba padziko lapansi ndi thambo. 14 Ndipo anakweza nyanga ya anthu ake, chilemekezo cha okondedwa ake onse; ndiwo ana a Israele, anthu a pafupi pa Iye. Aleluya. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi