Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 148:4 - Buku Lopatulika

4 Mlemekezeni, m'mwambamwamba, ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Mlemekezeni, m'mwambamwamba, ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Mtamandeni inu thambo lakumwambamwamba, ndi inu madzi a pamwamba pa thambo!

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Mutamandeni, inu thambo la kumwambamwamba ndi inu madzi a pamwamba pa thambo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 148:4
12 Mawu Ofanana  

Ndipo anati Mulungu, Pakhale thambo pakati pamadzi, lilekanitse madzi ndi madzi.


Ndipo Mulungu anapanga thambo, nalekanitsa madzi anali pansi pathambolo ndi madzi anali pamwamba pathambolo; ndipo kunatero.


Chaka cha mazana asanu ndi limodzi cha moyo wa Nowa, mwezi wachiwiri, tsiku la khumi ndi asanu ndi awiri la mwezi, tsiku lomwelo akasupe onse a madzi aakulu anasefuka, ndi mazenera a kumwamba anatseguka.


Kodi Mulungu adzakhala ndithu padziko lapansi? Taonani, thambo ndi mu Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.


Ndipo nyumba nditi ndimangeyi ndi yaikulu; pakuti Mulungu wathu ndiye wamkulu woposa milungu yonse.


Inu ndinu Yehova, nokhanu; mwalenga thambo, kumwambamwamba, ndi khamu lao lonse, dziko lapansi, ndi zonse zili pomwepo, nyanja ndi zonse zili m'mwemo, ndi Inu muzisunga zamoyo zonsezi, ndi khamu lakumwamba lilambira Inu.


Amene alumikiza mitanda ya zipinda zake m'madzi; naika makongwa akhale agaleta ake; nayenda pa mapiko a mphepo.


nadzichepetsa apenye zam'mwamba ndi za padziko lapansi.


Kwa Iye wakuberekeka pamwambamwamba, oyambira kale lomwe; taonani; amveketsa liu lake, ndilo liu lamphamvu.


Pakuti Mulungu adzapulumutsa Ziyoni, nadzamanga mizinda ya Yuda; ndipo iwo adzakhala komweko, likhale laolao.


Ndidziwa munthu wa mwa Khristu, zitapita zaka khumi ndi zinai (ngati m'thupi, sindidziwa; ngati kunja kwa thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu), anakwatulidwa wotereyo kunka naye Kumwamba kwachitatu.


Taonani thambo, ndi kumwambamwamba, dziko lapansi, ndi zonse zili m'mwemo ndi zake za Yehova Mulungu wanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa