Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -

Masalimo 148 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero


Salimo 148

1 Tamandani Yehova. Tamandani Yehova, inu a kumwamba, mutamandeni Iye, inu a mlengalenga.

2 Mutamandeni, inu angelo ake onse, mutamandeni, mutamandeni, inu zolengedwa za mmwamba.

3 Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi, mutamandeni, inu nonse nyenyezi zowala.

4 Mutamandeni, inu thambo la kumwambamwamba ndi inu madzi a pamwamba pa thambo.

5 Zonse zitamande dzina la Yehova pakuti Iye analamula ndipo zinalengedwa.

6 Iye anaziyika pa malo ake ku nthawi za nthawi; analamula ndipo sizidzatha.

7 Tamandani Yehova pa dziko lapansi, inu zolengedwa zikuluzikulu za mʼnyanja, ndi nyanja zonse zakuya,

8 inu zingʼaningʼani ndi matalala, chipale ndi mitambo, mphepo yamkuntho imene imakwaniritsa mawu ake,

9 inu mapiri ndi zitunda zonse, inu mitengo ya zipatso ndi mikungudza yonse,

10 inu nyama zakuthengo ndi ngʼombe zonse, inu zolengedwa zingʼonozingʼono ndi mbalame zowuluka.

11 Inu mafumu a dziko lapansi ndi anthu a mitundu yonse, inu akalonga ndi olamulira a dziko lapansi.

12 Inu anyamata ndi anamwali, inu nkhalamba ndi ana omwe.

13 Onsewo atamande dzina la Yehova pakuti dzina lake lokha ndi lolemekezeka; ulemerero wake ndi woopsa pa dziko lapansi pano ndi kumwamba komwe.

14 Iye wakwezera nyanga anthu ake, matamando a anthu ake onse oyera mtima, Aisraeli, anthu a pamtima pake. Tamandani Yehova.

The Word of God in Contemporary Chichewa

Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®

Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.®

Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.

Biblica, Inc.
Titsatireni:



Zotsatsa