Timatamanda Mulungu chifukwa cha tsiku lililonse lapadera limene timakumana nalo, ndi masiku osangalala ndi kukondwerera. Mulungu amasangalala tikamayenda mu mtendere ndi chimwemwe. Muzimutamanda Yehova m'masiku amenewa ndipo musaiwale kuti ndi Mulungu amene amakuchititsani kukhala ndi nthawi zapadera.
Masalimo 30:11-12 amati, “Munasintha kulira kwanga kukhala kuvina; Munandichotsa chiguduli, n’kundiveka chokondwerera; kuti moyo wanga uziyimba nyimbo zotamanda Inu, osakhala chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzakutamandani nthawi zonse.” M’Baibulo muli mavesi ambiri okhudza zochitika zapadera.
Ndipo msonkhano wonse unapangana kuchita masiku asanu ndi awiri ena, nachita masiku asanu ndi ena ndi chimwemwe.
Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa. Uzidya mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri, monga ndakuuza pa nthawi yonenedwa, m'mwezi wa Abibu; pakuti mwezi wa Abibu unatuluka mu Ejipito.
Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa; masiku asanu ndi awiri uzidya mkate wopanda chotupitsa, monga ndinakuuza, nyengo yoikika, mwezi wa Abibu, pakuti m'menemo unatuluka mu Ejipito; koma asaoneke munthu pamaso panga opanda kanthu;
Chifukwa chake ana a Israele azisunga Sabata, kuchita Sabata mwa mibadwo yao, likhale pangano losatha;
Napeza munalembedwa m'chilamulo kuti Yehova analamulira ndi Mose, kuti ana a Israele azikhala m'misasa pa chikondwerero cha mwezi wachisanu ndi chiwiri, ndi kuti azilalikira ndi kumveketsa m'midzi mwao monse ndi mu Yerusalemu, ndi kuti, Muzitulukira kuphiri, ndi kutengako nthambi za azitona, ndi nthambi za mitengo yamafuta, ndi nthambi za mitengo yamchisu, ndi zinkhwamba za migwalangwa, ndi nthambi za mitengo zothonana, kumanga nazo misasa monga munalembedwa.
Ndidzaleketsanso kusekerera kwake konse, zikondwerero zake, pokhala mwezi pake, ndi masabata ake, ndi misonkhano yake yonse yoikika.
Musadze nazonso, nsembe zachabechabe; nsembe zofukiza zindinyansa; tsiku lokhala mwezi ndi Sabata, kumema misonkhano, sindingalole mphulupulu ndi misonkhano. Masiku anu okhala mwezi ndi nthawi ya zikondwerero zanu mtima wanga uzida; zindivuta Ine; ndalema ndi kupirira nazo.
Pakuchiona Aroni, anamanga guwa la nsembe patsogolo pake; ndipo Aroni anafuula nati, Mawa aliko madyerero a Yehova.
Ndipo kudzakhala kuti kuyambira pa mwezi wokhala kufikira ku unzake, ndi kuyambira pa Sabata lina kufikira kulinzake, anthu onse adzafika kudzapembedzera pamaso pa Ine, ati Yehova.
ndipo mukakonzera Yehova nsembe yamoto, nsembe yopsereza, kapena yophera, pochita chowinda cha padera, kapena nsembe yaufulu, kapena nsembe ya pa nyengo zanu zoikika, kumchitira Yehova fungo lokoma, la ng'ombe kapena nkhosa;
Ndipo Mose anawauza, ndi kuti, Pakutha pake pa zaka zisanu ndi ziwiri, pa nyengo yoikika ya m'chaka chakulekerera, pa chikondwerero cha Misasa; pakufika Israele wonse kuoneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m'malo amene adzasankha, muzilalikira chilamulo ichi pamaso pa Israele wonse, m'makutu mwao.
Usapereka mwazi wa nsembe yanga pamodzi ndi mkate wa chotupitsa; ndi mafuta a madyerero anga asagonamo kufikira m'mawa.
Muzipereka ndithu limodzi la magawo khumi la zipatso zonse za mbeu zanu, zofuma kumunda, chaka ndi chaka. Ndipo muzidye pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m'malo m'mene asankhamo Iye, kukhalitsamo dzina lake; limodzi la magawo khumi la tirigu wanu, la vinyo wanu, ndi la mafuta anu, ndi oyamba kubadwa a ng'ombe zanu ndi a nkhosa ndi mbuzi zanu; kuti muphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu masiku onse.
Ndipo ndidzasanduliza zikondwerero zanu zikhale maliro, ndi nyimbo zanu zikhale za maliro, ndi kufikitsa ziguduli m'chuuno monse, ndi mpala pamutu uliwonse; nadzakhala ngati maliro a mwana mmodzi yekha, ndi chitsiriziro chake ngati tsiku lowawa.
Ndipo uziwerengera masabata a zaka asanu ndi awiri, zaka zisanu ndi ziwiri kasanu ndi kawiri; kotero kuti zaka za masabata a zaka asanu ndi awiri, zifikire zaka makumi anai kudza zisanu ndi zinai. Pamenepo uzitumizira lipenga lomveka m'mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi la mweziwo; tsiku la chitetezero mutumizire lipenga lifikire m'dziko lanu lonse.
Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi womwewo ndilo chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa a Yehova; masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda chotupitsa.
Mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi, pachikondwerero, achite momwemo masiku asanu ndi awiri, monga mwa nsembe yauchimo, monga mwa nsembe yopsereza, ndi monga mwa nsembe yaufa, ndi monga mwa mafuta.
Mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi, muzichita Paska, chikondwerero cha masiku asanu ndi awiri; audye mkate wopanda chotupitsa.
Nachita chikondwerero cha Misasa monga kwalembedwa, napereka nsembe yopsereza tsiku ndi tsiku mawerengedwe ake, monga mwa lamulo lake la tsiku lake pa tsiku lake;
Ndipo ana a Israele opezeka mu Yerusalemu anachita chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri ndi chimwemwe chachikulu; ndi Alevi ndi ansembe analemekeza Yehova tsiku ndi tsiku ndi zoimbira zakuliritsa kwa Yehova.
monga momwe mudayenera, tsiku ndi tsiku; napereka monga momwe adauza Mose pamasabata, pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika, katatu m'chaka: pa chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa, ndi pa chikondwerero cha Masabata, ndi pa chikondwerero cha Misasa.
Amuna onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'malo amene Iye adzasankha, katatu m'chaka; pa chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa, pa chikondwerero cha masabata, ndi pa chikondwerero cha Misasa; ndipo asaoneke pamaso pa Yehova opanda kanthu;
Ana a Israele achite Paska pa nyengo yoikidwa. Ndipo pokhala mtambo pamwamba pa chihema masiku pang'ono; pamenepo anakhala m'chigono monga awauza Yehova, nayendanso ulendo monga anauza Yehova. Koma mtambo ukakhala kuyambira madzulo kufikira m'mawa; pokwera mtambo m'mawa, ayenda ulendo. Ngakhale masiku awiri, kapena mwezi, kapena masiku ambiri, pokhalitsa mtambo pamwamba pa chihema ndi kukhalapo, ana a Israele anakhala m'chigono, osayenda ulendo; koma pakukwera uwu, anayenda ulendo. Powauza Yehova amanga mahema, powauza Yehova ayenda ulendo; anasunga udikiro wa Yehova powauza Yehova mwa dzanja la Mose. Tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo, muziuchita, pa nyengo yake yoikidwa; muuchite monga mwa malemba ake onse, ndi maweruzo ake onse.
Koma tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chiwiri, mutatuta zipatso za m'dziko, muzisunga chikondwerero cha Yehova masiku asanu ndi awiri; tsiku loyamba mupumule, ndi tsiku lachisanu ndi chitatu mupumule.
Nena ndi ana a Israele, kuti, Tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi uno wachisanu ndi chiwiri pali chikondwerero cha Misasa ya Yehova, masiku asanu ndi awiri.
Komatu, tsiku lakhumi la mwezi uwu wachisanu ndi chiwiri, ndilo tsiku la chitetezero; mukhale nao msonkhano wopatulika, ndipo mudzichepetse; ndi kubwera nayo nsembe yamoto kwa Yehova.
Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzipumula, ndiko chikumbutso cha kuliza malipenga, msonkhano wopatulika.
Ndipo mudziwerengere kuyambira tsiku lotsata Sabata, kuyambira tsikuli mudadza nao mtolo wansembe yoweyula; pakhale masabata asanu ndi awiri amphumphu; muwerenge masiku makumi asanu kufikira tsiku lotsata sabata lachisanu ndi chiwiri; pamenepo mubwere nayo kwa Yehova nsembe ya ufa watsopano.
Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutakalowa m'dziko limene ndikupatsani, ndi kucheka dzinthu zake, pamenepo muzidza nao mtolo wa zipatso zoyamba za masika anu kwa wansembe; ndipo iye aweyule mtolowo pamaso pa Yehova, ulandirikire inu, tsiku lotsata Sabata wansembe aweyule.
Izi ndi nyengo zoikika za Yehova, misonkhano yopatulika, zimene muzilalikira pa nyengo zoikika zao.
Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Nyengo zoikika za Yehova zimene muzilalikira zikhale misonkhano yopatulika, ndizo nyengo zanga zoikika.
Ndipo muzisunga chinthu ichi chikhale lemba la kwa inu, ndi kwa ana anu ku nthawi zonse. Ndipo kudzakhala, pamene mulowa m'dziko limene Yehova adzakupatsani, monga analankhula, muzisunga kutumikira kumeneku. Ndipo kudzakhala, pamene ana anu adzanena ndi inu, Kutumikiraku muli nako nkutani? Mudzati, Ndiko nsembe ya Paska wa Yehova, amene anapitirira nyumba za ana a Israele mu Ejipito, pamene anakantha Aejipito, napulumutsa nyumba zathu.
Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi uwu pali zikondwerero; masiku asanu ndi awiri azidya mkate wopanda chotupitsa. Tsiku loyamba pali kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena;
Ndipo mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena; likukhalireni inu tsiku lakuliza malipenga.
Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha.
Samalirani mwezi wa Abibu, kuti muzichitira Yehova Mulungu wanu Paska; popeza m'mwezi wa Abibu Yehova Mulungu wanu anakutulutsani m'dziko la Ejipito usiku.
Ndipo uzichita chikondwerero cha Masabata, ndicho chikondwerero cha Zipatso zoyamba za Masika a tirigu, ndi chikondwerero cha Kututa pakutha pa chaka.
Muzindichitira Ine madyerero katatu m'chaka. Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa; masiku asanu ndi awiri uzidya mkate wopanda chotupitsa, monga ndinakuuza, nyengo yoikika, mwezi wa Abibu, pakuti m'menemo unatuluka mu Ejipito; koma asaoneke munthu pamaso panga opanda kanthu; ndi chikondwerero cha Masika, zipatso zoyamba za ntchito zako, zimene udazibzala m'munda; ndi chikondwerero cha Kututa, pakutha chaka, pamene ututa ntchito zako za m'munda.
Mudzichitire chikondwerero cha Misasa masiku asanu ndi awiri, mutasunga za padwale ndi za mopondera mphesa; nimukondwere m'madyerero mwanu, inu, ndi ana anu aamuna, ndi ana anu aakazi, ndi antchito anu aamuna, ndi antchito anu aakazi, ndi Mlevi, ndi mlendo, ndi mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye okhala m'mudzi mwanu.
Ndipo muchitire Yehova Mulungu wanu chikondwerero cha Masabata, ndiwo msonkho waufulu wa dzanja lanu, umene mupereke monga Yehova Mulungu wanu akudalitsani.
Ndipo kudzachitika kuti otsala onse a amitundu onse anadzawo kulimbana ndi Yerusalemu, adzakwera chaka ndi chaka kulambira mfumu Yehova wa makamu, ndi kusunga chikondwerero cha Misasa.
Ndipo pakuona kuti kudakondweretsa Ayuda, anaonjezapo nagwiranso Petro. Ndipo awo ndi masiku a mkate wopanda chotupitsa. Ndipo m'mene adamgwira, anamuika m'ndende, nampereka kwa magulu anai a alonda, lonse anaianai, amdikire iye; ndipo anafuna kumtulutsa kudza naye kwa anthu atapita Paska.
Ndipo muchipatule chaka cha makumi asanu, ndi kulalikira kwa onse okhala m'dzikomo kuti akhale aufulu; muchiyese chaka choliza lipenga; ndipo mubwerere munthu aliyense ku zakezake, ndipo mubwerere yense ku banja lake.
Tayang'ana pa Ziyoni, mzinda wa zikondwerero zathu; maso ako adzaona, Yerusalemu malo a phee, chihema chimene sichidzasunthidwa, zichiri zake sizidzazulidwa konse, zingwe zake sizidzadulidwa.
Koma Paska wa Ayuda anali pafupi; ndipo ambiri anakwera kunka ku Yerusalemu kuchoka kuminda, asanafike Paska, kukadziyeretsa iwo okha.
Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chiwiri muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena, koma muchitire Yehova madyerero masiku asanu ndi awiri;
nasunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri ndi chimwemwe; pakuti Yehova adawakondweretsa, nawatembenuzira mtima wa mfumu ya Asiriya, kulimbitsa manja ao mu ntchito ya nyumba ya Mulungu, Mulungu wa Israele.
Momwemo tsiku lakukondwera inu, ndi nyengo zoikidwa zanu, ndi poyamba miyezi yanu, muziliza malipenga pa nsembe zanu zopsereza, ndi pa nsembe zanu zoyamika; ndipo akhale kwa inu chikumbutso pamaso pa Mulungu wanu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
Ndipo tsiku la khumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri uwu muzikhala nako kusonkhana kopatulika; pamenepo mudzichepetse, musamagwira ntchito;
Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri muliyese lopatulika, Sabata lakupuma la Yehova: aliyense agwira ntchito pamenepo, aphedwe.
Ndipo tinapita m'ngalawa kuchokera ku Filipi, atapita masiku a mkate wopanda chotupitsa, ndipo popita masiku asanu tinawapeza ku Troasi; pamenepo tinatsotsa masiku asanu ndi awiri.
Ndipo mfumu inalamulira anthu onse, kuti, Mchitireni Yehova Mulungu wanu Paska, monga mulembedwa m'buku ili la chipangano.
ndiwo masiku amene Ayuda anapumula pa adani ao; ndi mwezi wachisoni unawasandulikira wakukondwera, ndi wamaliro ukhale tsiku lokoma, awayese masiku amadyerero ndi akukondwera, akutumizirana magawo, ndi akupatsa zaufulu kwa osauka.
Likhale ndi inu Sabata lakupumula; ndipo mudzichepetse; tsiku lachisanu ndi chinai madzulo, kuyambira madzulo kufikira madzulo musunge Sabata lanu.
Ndipo muzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa; pakuti tsiku lomwe lino ndinatulutsa makamu anu m'dziko la Ejipito; chifukwa chake muzisunga tsiku lino m'mibadwo yanu, lemba losatha.
Koma tsiku lomaliza, lalikululo la chikondwerero, Yesu anaimirira nafuula, ndi kunena, Ngati pali munthu akumva ludzu, adze kwa Ine, namwe.
Atero Yehova wa makamu: Kusala kwa mwezi wachinai, ndi kusala kwa mwezi wachisanu, ndi kusala kwa mwezi wachisanu ndi chiwiri, ndi kusala kwa mwezi wakhumi kukhale kwa nyumba ya Yuda chimwemwe ndi chikondwerero, ndi nyengo zoikika zosekerera; chifukwa chake kondani choonadi ndi mtendere.
Munthu akakhala woyera, wosakhala paulendo, koma akaleka kuchita Paska, amsadze munthuyo kwa anthu a mtundu wake; popeza sanabwere nacho chopereka cha Yehova pa nyengo yake yoikidwa, munthuyu asenze kuchimwa kwake.
Ndipo ana a Israele okhalako anachita Paska nthawi yomweyo, ndi chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri.
Ndipo m'phiri limeneli Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.
Inu mudzakhala ndi nyimbo, monga usiku, podya phwando lopatulika; ndi mtima wokondwa, monga pomuka wina ndi chitoliro, kufikira kuphiri la Yehova, kuthanthwe la Israele.
Momwemo munali chimwemwe chachikulu mu Yerusalemu; pakuti kuyambira masiku a Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israele simunachitike chotero mu Yerusalemu.
Ndidzikumbukira izi ndipo nditsanulira moyo wanga m'kati mwa ine, pakuti ndinkapita ndi unyinji wa anthu, ndinawatsogolera kunyumba ya Mulungu, ndi mau akuimbitsa ndi kuyamika, ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera.
Ndipo itapita nthawi yambiri, ndipo unayambokhala woopsa ulendowo, popezanso nyengo ya kusala chakudya idapita kale, Paulo anawachenjeza,
Kwerani inu kunka kuphwando; sindikwera Ine kuphwando ili tsopano apa; pakuti nthawi yanga siinakwanire.
Koma pofika anthu a m'dziko pamaso pa Yehova m'zikondwerero zoikika, iye amene alowera njira ya kuchipata cha kumpoto kudzalambira, atulukire njira ya kuchipata cha kumwera; ndi iye amene alowera njira ya kuchipata cha kumwera, atulukire njira ya kuchipata cha kumpoto; asabwerere njira ya chipata anadzeracho, koma atulukire m'tsogolo mwake.
Izi ndi nyengo zoikika za Yehova, zimene muzilalikira zikhale misonkhano yopatulika, kukabwera nayo nsembe yamoto kwa Yehova, nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa, nsembe yophera, ndi nsembe yothira, yonse pa tsiku lakelake;
Anawerenganso m'buku la chilamulo cha Mulungu tsiku ndi tsiku, kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lotsiriza. Nachita chikondwerero masiku asanu ndi awiri; ndi tsiku lachisanu ndi chitatu ndilo msonkhano woletsa, monga mwa malemba.
Ayuda anakhazikitsa ichi, nadzilonjezetsa okha, ndi mbeu yao, ndi onse akuphatikana nao, chingalekeke, kuti adzasunga masiku awa awiri monga mwalembedwa, ndi monga mwa nyengo yao yoikika, chaka ndi chaka; ndi kuti masikuwa adzakumbukika ndi kusungika mwa mibadwo yonse, banja lililonse, dziko lililonse, ndi mzinda uliwonse; ndi kuti masiku awa sadzalekeka mwa Ayuda, kapena kusiyidwa chikumbukiro chao mwa mbeu yao.
Muchiyese chaka cha makumi asanucho choliza lipenga, musamabzala, kapena kucheka zophuka zokha m'mwemo; kapena kucheka mphesa zake za mipesa yosadzombola.
Dzipangire malipenga awiri asiliva; uwasule mapangidwe ake; uchite nao poitana khamu, ndi poyendetsa a m'zigono.
Ndipo Yerobowamu anaika madyerero mwezi wachisanu ndi chitatu, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi olingana ndi madyerero aja a ku Yuda, napereka nsembe paguwa la nsembe; anatero mu Betele, nawaphera nsembe anaang'ombe aja anawapanga, naika mu Betele ansembe a misanje imene anaimanga.
Ndipo udindo wa kalonga ndiwo kupereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi nsembe zothira, pachikondwerero, ndi pokhala mwezi, ndi pa masabata; pa zikondwerero zonse zoikika a nyumba ya Israele; ndipo apereke nsembe yauchimo, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zamtendere, kuchitira chotetezera nyumba ya Israele.
Popeza ndicho chaka choliza lipenga; muchiyese chopatulika, mudye zipatso zake kunja kwa munda.
Ndipo tsiku loyamba la mikate yopanda chotupitsa, pamene amapha Paska, ophunzira ananena naye, Mufuna tinke kuti, tikakonze mkadyereko Paska?
Ndipo tsiku la mikate yopanda chotupitsa linafika, limene inayenera kuphedwa nsembe ya Paska.
Ndipo tsiku loyamba la mkate wopanda chotupitsa, ophunzira anadza kwa Yesu, nati, Mufuna tikakonzere kuti Paska, kuti mukadye?