Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 14:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo tsiku loyamba la mikate yopanda chotupitsa, pamene amapha Paska, ophunzira ananena naye, Mufuna tinke kuti, tikakonze mkadyereko Paska?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo tsiku loyamba la mikate yopanda chotupitsa, pamene amapha Paska, ophunzira ananena naye, Mufuna tinke kuti, tikakonze mkadyereko Paska?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Pa tsiku loyamba la masiku a buledi wosafufumitsa, tsiku lomwe anthu ankapha mwanawankhosa wochitira phwando la Paska, ophunzira a Yesu adamufunsa kuti, “Kodi tikakukonzereni kuti malo okadyerako phwando la Paska?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Pa tsiku loyamba la Phwando la Buledi wopanda yisiti, nthawi imene mwa mwambo inali ya kupha mwana wankhosa wa Paska, ophunzira a Yesu anafunsa Iye kuti, “Mufuna tipite kuti kumene tikakonzekere kuti mukadyere Paska?”

Onani mutuwo Koperani




Marko 14:12
16 Mawu Ofanana  

Mwezi woyamba, tsiku lake lakhumi ndi chinai madzulo ake, muzidya mkate wopanda chotupitsa, kufikira tsiku la makumi awiri mphambu limodzi la mwezi, madzulo ake.


Ndipo mukhale naye chisungire kufikira tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi womwe; ndipo gulu lonse la Israele lizamuphe madzulo.


Ndipo azidya nyamayo usiku womwewo, yoocha pamoto, ndi mkate wopanda chotupitsa; aidye ndi ndiwo zowawa.


Ndipo Mose ananena ndi anthu, Kumbukirani tsiku lino limene munatuluka mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo; pakuti Yehova anakutulutsani muno ndi dzanja lamphamvu; ndipo asadye kanthu ka chotupitsa.


Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye.


Ndipo popita masiku awiri kuli phwando la Paska ndi Mkate wopanda chotupitsa; ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna momchitira chiwembu, ndi kumupha:


Ndipo pamene iwo anamva, anasekera, nalonjezana naye kuti adzampatsa ndalama. Ndipo iye anafunafuna pompereka Iye bwino.


Ndipo anatuma awiri a ophunzira ake, nanena nao, Lowani m'mzinda, ndipo adzakomana nanu munthu wakusenza mtsuko wa madzi; mumtsate iye;


koma pokwaniridwa nthawi, Mulungu anatuma Mwana wake, wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo,


Simuyenera kuphera nsembe ya Paska m'midzi yanu iliyonse, imene Yehova Mulungu wanu akupatsani;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa