Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 3:4 - Buku Lopatulika

4 Nachita chikondwerero cha Misasa monga kwalembedwa, napereka nsembe yopsereza tsiku ndi tsiku mawerengedwe ake, monga mwa lamulo lake la tsiku lake pa tsiku lake;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Nachita chikondwerero cha Misasa monga kwalembedwa, napereka nsembe yopsereza tsiku ndi tsiku mawerengedwe ake, monga mwa lamulo lake la tsiku lake pa tsiku lake;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ankasunga tsiku la chikondwerero cha misasa monga momwe kudalembedwera. Masiku onse ankaperekanso nsembe zopsereza potsata chiŵerengero chake chofunika tsiku ndi tsiku, monga kudalembedwera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ankasunga tsiku la chikondwerero cha misasa monga momwe zinalembedwera. Ankaperekanso nsembe za tsiku ndi tsiku monga mwa chiwerengero chake potsata mwambo wake wa tsiku ndi tsiku monga zinalembedwa.

Onani mutuwo Koperani




Ezara 3:4
14 Mawu Ofanana  

Ndipo anasiyako ku likasa la chipangano la Yehova Asafu ndi abale ake, atumikire kulikasa kosalekeza, monga umo mudzafunika tsiku ndi tsiku;


pamodzi ndi iwo oyesedwa mwa chibadwidwe cha amuna, kuyambira a zaka zitatu ndi mphambu, kwa aliyense amene adalowa m'nyumba ya Yehova, monga mwa ntchito yake pa tsiku lake, kukachita za utumiki wao mu udikiro wao monga mwa zigawo zao;


ndi chikondwerero cha Masika, zipatso zoyamba za ntchito zako, zimene udazibzala m'munda; ndi chikondwerero cha Kututa, pakutha chaka, pamene ututa ntchito zako za m'munda.


Koma izi ndizo uzikonza paguwa la nsembelo; anaankhosa awiri a chaka chimodzi, tsiku ndi tsiku kosalekeza.


Ndipo akufulumiza anawakakamiza, ndi kuti, Tsirizani ntchito zanu, ntchito ya tsiku pa tsiku lake, monga muja munali ndi udzu.


Koma phoso lake mfumu ya ku Babiloni sanaleke kumpatsa, phoso tsiku ndi tsiku gawo lake, mpaka tsiku la kufa kwake, masiku onse a moyo wake.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,


Izi muzikonzera Yehova mu zikondwerero zanu zoikika, pamodzi ndi zowinda zanu, ndi zopereka zanu zaufulu, za nsembe zanu zopsereza, ndi za nsembe zanu zaufa, ndi za nsembe zanu zothira, ndi za nsembe zanu zoyamika.


Koma chikondwerero cha Ayuda cha Misasa, linayandikira.


Koma tsiku lomaliza, lalikululo la chikondwerero, Yesu anaimirira nafuula, ndi kunena, Ngati pali munthu akumva ludzu, adze kwa Ine, namwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa