Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 11:55 - Buku Lopatulika

55 Koma Paska wa Ayuda anali pafupi; ndipo ambiri anakwera kunka ku Yerusalemu kuchoka kuminda, asanafike Paska, kukadziyeretsa iwo okha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

55 Koma Paska wa Ayuda anali pafupi; ndipo ambiri anakwera kunka ku Yerusalemu kuchoka ku milaga, usanafike Paska, kukadziyeretsa iwo okha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

55 Chikondwerero cha Paska chija chinkayandikira. Choncho anthu ambiri ochokera ku midzi adapita ku Yerusalemu kukachita mwambo wa kudziyeretsa, Paska isanayambe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

55 Nthawi ya Paska wa Ayuda itayandikira, ambiri anakwera kupita ku Yerusalemu kuchokera ku madera a ku midzi chifukwa cha mwambo wa kuyeretsedwa Paska asanafike.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 11:55
30 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anati kwa a banja lake, ndi kwa onse amene anali ndi iye, Chotsani milungu yachilendo ili mwa inu, mudziyeretse, ndi kupindula zovala zanu:


Ndipo kunatero, atatha masiku a madyererowa Yobu anatumiza mau, nawapatula, nauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, monga mwa kuwerenga kwa iwo onse; pakuti Yobu anati, Kapena anachimwa ana anga, nachitira Mulungu mwano m'mtima mwao, Anatero Yobu masiku onse.


Ndidzasamba manja anga mosalakwa; kuti ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova;


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka kwa anthuwo, nuwapatulitse lero ndi mawa, ndipo atsuke zovala zao.


Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Angakhale munthu wa inu kapena wa mibadwo yanu, adetsedwa, chifukwa cha mtembo, kapena pokhala paulendo, koma azichitira Yehova Paska.


Pamenepo panali amuna, anadetsedwa ndi mtembo wa munthu, ndipo sanakhoze kuchita Paska tsiku lomwelo; m'mwemo anafika pamaso pa Mose ndi pamaso pa Aroni tsiku lomwelo;


Ndipo panali pamene Yesu anatha mau onse amenewa, anati kwa ophunzira ake,


Mudziwa kuti akapita masiku awiri, Paska afika, ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kupachikidwa pamtanda.


Ndipo popita masiku awiri kuli phwando la Paska ndi Mkate wopanda chotupitsa; ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna momchitira chiwembu, ndi kumupha:


Ndipo chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa chinayandikira, ndicho chotchedwa Paska.


Pomwepo anatsala masiku asanu ndi limodzi asanafike Paska, Yesu anadza ku Betaniya kumene kunali Lazaro, amene Yesu adamuukitsa kwa akufa.


Koma pasanafike chikondwerero la Paska, Yesu, podziwa kuti nthawi yake idadza yakuchoka kutuluka m'dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m'mene anakonda ake a Iye yekha a m'dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.


Pamenepo anamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita ku Pretorio; koma munali mamawa; ndipo iwo sanalowe ku Pretorio, kuti angadetsedwe, koma kuti akadye Paska.


Ndipo Paska wa Ayuda unayandikira, ndipo Yesu anakwera kunka ku Yerusalemu.


Ndipo panali pamenepo mitsuko yamiyala isanu ndi umodzi yoikidwako monga mwa mayeretsedwe a Ayuda, yonse ya miyeso iwiri kapena itatu.


Zitapita izi panali chikondwerero cha Ayuda; ndipo Yesu anakwera kunka ku Yerusalemu.


Ndipo Paska, chikondwerero cha Ayuda, anayandikira.


amenewa uwatenge nudziyeretse nao pamodzi, nuwalipirire, kuti amete mutu; ndipo adzadziwa onse kuti zomveka za iwe nzachabe, koma kuti iwe wekhanso uyenda molunjika, nusunga chilamulo.


Pamenepo Paulo anatenga anthuwo, ndipo m'mawa mwake m'mene anadziyeretsa nao pamodzi, analowa mu Kachisi, nauza chimalizidwe cha masiku a kuyeretsa, kufikira adawaperekera iwo onse mtulo.


popereka izi anandipeza woyeretsedwa mu Kachisi, wopanda khamu la anthu, kapena phokoso;


Koma munthu adziyese yekha, ndi kotero adye mkate, ndi kumwera chikho.


Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m'manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.


Nati iye, Ndi mtendere umene; ndadza kudzaphera nsembe kwa Yehova; mudzipatule ndi kufika ndi ine kunsembeko. Ndipo iye anapatula Yese ndi ana ake, nawaitanira kunsembeko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa