Masalimo 81:3 - Buku Lopatulika3 Ombani lipenga, pokhala mwezi, utakula mwezi, tsiku la phwando lathu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Ombani lipenga, pokhala mwezi, utakula mwezi, tsiku la phwando lathu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Imbani lipenga mwezi ukaoneka chatsopano, ukaoneka kwathunthu, pa tsiku lathu lachikondwerero. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Imbani lipenga la nyanga ya nkhosa yayimuna pa mwezi watsopano, ndi pamene mwezi waoneka wonse, pa tsiku la phwando; Onani mutuwo |
Taonani, nditi ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, kumpatulira iyo, ndi kufukiza pamaso pake zonunkhira za fungo lokoma, ndiyo ya mkate woonekera wachikhalire, ndi ya nsembe zopsereza, m'mawa ndi madzulo, pamasabata, ndi pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika za Yehova Mulungu wathu. Ndiwo machitidwe osatha mu Israele.