Masalimo 81:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Imbani lipenga la nyanga ya nkhosa yayimuna pa mwezi watsopano, ndi pamene mwezi waoneka wonse, pa tsiku la phwando; Onani mutuwoBuku Lopatulika3 Ombani lipenga, pokhala mwezi, utakula mwezi, tsiku la phwando lathu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Ombani lipenga, pokhala mwezi, utakula mwezi, tsiku la phwando lathu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Imbani lipenga mwezi ukaoneka chatsopano, ukaoneka kwathunthu, pa tsiku lathu lachikondwerero. Onani mutuwo |
Tsono ine ndikufuna kumanga Nyumba ya Yehova Mulungu wanga ndi kuyipereka kwa Iye kuti tiziyikamo buledi wopatulika nthawi zonse ndiponso kuperekeramo nsembe zopsereza mmawa uliwonse ndi madzulo ndi pa masabata ndi pa masiku a chikondwerero cha mwezi watsopano ndiponso pa masiku osankhika a chikondwerero cha Yehova Mulungu wathu, monga mwa malamulo a Aisraeli mpaka muyaya.