Eksodo 12:14 - Buku Lopatulika14 Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 “Tsiku limeneli muzidzalisunga. Tsiku limeneli muzidzalikumbukira, ndipo muzidzachita chikondwerero, kupembedza Chauta. Mibadwo yonse izidzakumbukira tsikuli, kuti likhale lamulo lamuyaya, lakuti muzidzachita chikondwerero pa tsiku limenelo.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 “Ili ndi tsiku la chikumbutso. Tsiku limeneli muzidzachita chikondwerero, kupembedza Yehova. Mibado yonse imene ikubwera izidzakumbukira tsiku limeneli ngati lamulo lamuyaya ndi kuti pa tsikuli azidzachita chikondwerero cholemekeza Yehova. Onani mutuwo |
Ndipo mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu aamuna, ndi ana anu aakazi, ndi antchito anu aamuna, ndi antchito anu aakazi, ndi Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, ndi mlendo, ndi mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala pakati pa inu, m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake.