Eksodo 12:15 - Buku Lopatulika15 Masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda chotupitsa; lingakhale tsiku loyamba muzichotsa chotupitsa m'nyumba zanu; pakuti aliyense wakudya mkate wa chotupitsa kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lachisanu ndi chiwiri, munthu ameneyo adzachotsedwa kwa Israele. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 Masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda chotupitsa; lingakhale tsiku loyamba muzichotsa chotupitsa m'nyumba zanu; pakuti aliyense wakudya mkate wa chotupitsa kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lachisanu ndi chiwiri, munthu amene adzasadzidwa kwa Israele. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 Tsono Chauta adati, “Muzidzadya buledi wosafufumitsa pa masiku asanu ndi aŵiri. Pa tsiku loyamba muzidzachotsa zotupitsira buledi m'nyumba zanu zonse, chifukwa pa masiku asanu ndi aŵiri aliyense wodya buledi wofufumitsa adzachotsedwa pakati pa Aisraele. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 Kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti. Tsiku loyamba muzichotsa yisiti mʼnyumba zanu, ngati aliyense adzadya kanthu kalikonse kali ndi yisiti kuyambira tsiku loyamba mpaka tsiku lachisanu ndi chiwiri, munthu ameneyo adzayenera kuchotsedwa mʼgulu la Israeli. Onani mutuwo |